bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 10
Matthew 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 11 →
1
Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
2
Atumwi khumi ndi aŵiriwo maina ao ndi aŵa: Woyamba ndi Simoni, wotchedwa Petro, ndipo mbale wake Andrea; Yakobe, mwana wa Zebedeo, ndi mbale wake Yohane;
3
Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
4
Simoni, wa m'chipani chandale cha Azelote; ndiponso Yudasi Iskariote, amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.
5
Anthu khumi ndi aŵiri ameneŵa Yesu adaŵatuma ndi malamulo akuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kukaloŵa m'mudzi uliwonse wa Asamariya ai.
6
Koma makamaka mupite kwa Aisraele amene ali ngati nkhosa zotayika.
7
Pitani, muzikalalika kuti, ‘Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.’
8
Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere.
9
Musatenge ndalama m'zikwama, kaya nzagolide, kaya nzasiliva, kaya nzakopala.
10
Musatenge thumba lapaulendo, kapena mikanjo iŵiri, kapena nsapato, kapena ndodo. Paja wantchito ngwoyenera kulandira zosoŵa zake.
11
“Pamene mwaloŵa mu mzinda kapena m'mudzi uliwonse, mufunsitse za munthu wofunadi kukulandirani. Mukakhale kunyumba kwake mpaka nthaŵi yochoka.
12
Poloŵa m'nyumba, muzikanena kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu’.
13
Tsono ngati anthu am'nyumbamo akulandiranidi, mtendere wanuwo ukhale nawo ndithu. Koma ngati anthu am'nyumbamo akana kukulandirani, mtendere wanuwo ubwerere kwa inu.
14
Munthu aliyense akakana kukulandirani kapena kumvera mau anu, musanse fumbi la kumapazi kwanu potuluka m'nyumbamo kapena m'mudzimo.
15
Ndithu ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga mudzi wa Sodomu ndi wa Gomora, koma osati polanga mudzi umenewo.
16
“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda.
17
Anthu muchenjere nawo, pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero.
18
Adzapita nanu kwa nduna ndi mafumu chifukwa cha Ine, mwakuti mudzandichitira umboni pamaso pao, ndi pa anthu a mitundu ina.
19
Akadzakutengerani ku milandu, musadzade nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Kodi tikakambe bwanji?’ Kapena kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Mudzapatsidwa pa nthaŵi imeneyo mau oti munene.
20
Pajatu odzalankhula si ndinu ai, koma Mzimu wa Atate anu ndiye amene adzalankhula kudzera mwa inu.
21
“Mbale azidzapereka mbale wake kuti aphedwe, bambo azidzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo ao, mpaka kuŵaphetsa.
22
Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
23
Tsono akamadzakuzunzani ku mudzi wakutiwakuti, mukathaŵire ku mudzi wina. Ndithu ndikunenetsa kuti musanathe kuyendera midzi yonse ya Aisraele, Mwana wa Munthu adzakhala atabwera.
24
Paja wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo wantchito saposa mbuye wake ai.
25
Kumkwanira wophunzira kuti alingane ndi mphunzitsi wake, ndiponso wantchito kuti alingane ndi mbuye wake. Tsono ngati mwini banja anthu adamutcha Belezebulu, nanji a m'banja mwake, kodi sadzaŵatcha maina oipa koposa apa?
26
“Choncho inu musamaopa anthu. Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika.
27
Zimene ndikukuuzirani m'chibisibisi, inu mukazilankhulire poyera, ndipo zimene mukuzimvera m'manong'onong'o, inu mukazilalikire pa madenga.
28
Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena.
29
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa.
30
Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse.
31
Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
32
“Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba.
33
Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa.
34
“Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Sindidadzapereke mtendere ai, koma nkhondo.
35
Inetu paja ndidadzalekanitsa mwana wamwamuna ndi bambo wake, mwana wamkazi ndi mai wake, mkazi ndi apongozi ake aakazi,
36
mwakuti adani a munthu adzakhala a m'banja mwake omwe.
37
“Munthu wokonda bambo wake kapena mai wake koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. Ndipo wokonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga.
38
Amene sasenza mtanda wake ndi kumanditsata, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga.
39
Munthu woyesa kusunga moyo wake, adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzausunga.
40
“Munthu wokulandirani inu, amandilandira Ine ndemwe. Ndipo wondilandira Ine, amalandiranso Iye uja amene adandituma.
41
Munthu wolandira nthumwi ya Mulungu chifukwa choti ndi nthumwi, adzalandira mphotho ya nthumwi ya Mulungu. Wolandira munthu wolungama chifukwa choti ngwolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama.
42
Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28