bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 28
Matthew 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
1
Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja adabwera mbandakucha pa tsiku lotsatira Sabatalo, kudzaona manda aja.
2
Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo.
3
Maonekedwe ake anali ngati a mphezi, ndipo chovala chake chinali choyera chambee.
4
Pamenepo alonda aja adachita mantha nayamba kunjenjemera, nkungoti gwa ngati anthu akufa.
5
Koma mngeloyo adalankhula ndi azimai aja naŵauza kuti, “Inu musaope ai. Ndikudziŵa kuti mukufuna Yesu, uja adaampachika pa mtandayu.
6
Sali muno ai, wauka monga muja adaaneneramu. Bwerani, dzaoneni pamene adaagona.
7
Pitani msanga tsono, kauzeni ophunzira ake aja kuti, ‘Iye wauka kwa akufa, ndipo watsogolako kupita ku Galileya, mukamuwonera kumeneko.’ Kumbukirani zimene ndakuuzanizi.”
8
Apo azimaiwo adachoka kumandako msanga, ali ndi mantha komanso ndi chimwemwe chachikulu, nathamanga kukauza ophunzira ake aja.
9
Mwadzidzidzi Yesu adakumana nawo nati, “Monitu azimai!” Iwo adadza pafupi, nkugwira mapazi ake, nampembedza.
10
Apo Yesu adaŵauza kuti, “Musaope. Pitani, kauzeni abale anga kuti apite ku Galileya. Akandiwonera kumeneko.”
11
Pamene akazi aja ankapita, ena mwa alonda aja adakafika ku mzinda, nakasimbira akulu a ansembe zonse zimene zidaachitika.
12
Tsono akulu a ansembe aja ndi akulu a Ayuda adasonkhana napangana nzeru. Adapatsa alonda aja ndalama zambiri,
13
naŵauza kuti, “Muziti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku nkuba mtembo wake ife tili m'tulo.’
14
Choncho bwanamkubwa akamva zimenezi, ife tidzamkhazika mtima pansi, ndipo sipadzakhala kanthu kokuvutani.”
15
Alonda aja atalandira ndalama zija, adachitadi monga momwe adaaŵauzira. Motero mbiri imeneyi idawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino.
16
Ophunzira khumi ndi mmodzi aja adapita ku Galileya kuphiri kumene Yesu adaapangana nawo kuti akakumane.
17
Pamene adamuwona, adampembedza, koma ena ankakayika.
18
Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
19
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.
20
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28