bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 23
Matthew 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 24 →
1
Pambuyo pake Yesu adalankhula ndi gulu la anthu ochuluka pamodzi ndi ophunzira ake.
2
Adaŵauza kuti, “Aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi ali ndi udindo wotanthauzira malamulo a Mose.
3
Nchifukwa chake muzichita ndi kutsata zonse zimene iwo amakuphunzitsani. Komatu musamatsanzira zimene amachita, pakuti sachita zimene amaphunzitsa.
4
Iwo amamanga katundu wosautsa kunyamula nkusenzetsa anthu, koma iwowo samukhudzako mpang'ono pomwe.
5
Zonse zimene amachita amangozichita kuti anthu aŵaone. Amadzimangirira timapukusi tikulutikulu ta mau a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono. Amatalikitsanso mphonje za zovala zao.
6
Amakonda malo olemekezeka pa maphwando ndiponso mipando yaulemu kwambiri ku nyumba zamapemphero.
7
Amakondanso kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika, ndipo kuti aziŵatchula aphunzitsi.
8
“Koma inuyo anthu asati azikutchulani aphunzitsi, pakuti muli ndi Mphunzitsi mmodzi yekha, ndipo nonsenu muli pa chibale.
9
Musamatchulanso munthu pansi pano kuti atate, popeza kuti muli ndi atate amodzi okha, ndiwo Atate anu akumwamba.
10
Anthu asatinso azikutchulani atsogoleri, popeza kuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi yekha, ndiye Khristu.
11
Pakati panupa wamkulu akhale mtumiki wanu.
12
Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”
13
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatseka pakhomo pa Ufumu wakumwamba kuti anthu asaloŵemo. Paja inu nomwe simuloŵamo, ndipo mumatsekereza amene amafuna kuloŵamo.” [
14
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumagongolera azimai amasiye nkumaŵadyera chuma chao, kwinaku nkumanyengezera kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa.”]
15
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumayenda maulendo ambirimbiri pa nyanja ndi pa mtunda, kufunafuna ngakhale munthu mmodzi yekha kuti atembenuke ndi kusanduka wophunzira wanu. Tsono akapezeka, mumamsandutsa woyenera kulangidwa ku Gehena kuposa inu kaŵiri.
16
“Muli ndi tsoka, inu atsogoleri akhungu! Inu mumati, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, asunge lumbiro lakelo.’
17
Inu anthu opusa ndi akhungu! Chachikulu nchiti, chuma chija, kapena Nyumba imene ikusandutsa chumacho kuti chikhale chopatulika?
18
Mumatinso, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali guwa lansembe, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali choperekedwa pa guwa, asunge lumbiro lakelo.’
19
Anthu akhungu inu! Chachikulu nchiti, choperekedwa chija, kapena guwa lansembe lija limene likusandutsa choperekedwacho kuti chikhale chopatulika?
20
Tsonotu munthu akalumbira kuti, Pali guwa la nsembe, walumbiranso pa zonse zimene zili paguwapo.
21
Akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, walumbiranso pa zonse zimene zili m'Nyumbamo.
22
Ndipo akalumbira kuti, Kumwambadi, walumbiranso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndiponso pa Iye amene amakhala pampandopo.
23
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.
24
Inu atsogoleri akhungu, mumasuza zakumwa zanu kuti muchotsemo kanchenche, koma mumameza ngamira.
25
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatsuka kunja kwa chikho ndi kwa mbale koma m'kati mwake m'modzaza ndi nzeru zakuba, ndi zaumbombo.
26
Afarisi akhungu inu, yambani mwatsuka m'kati mwa chikho, ndipo kunja kwakenso kudzayera.
27
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Muli ngati manda opaka njeresa, amene amaoneka okongola kunja, pamene m'kati mwake m'modzaza ndi mafupa a anthu akufa ndi zoola zina zilizonse.
28
Inunso muli chimodzimodzi: pamaso pa anthu mumaoneka olungama, pamene m'kati mwanu m'modzaza ndi chiphamaso ndi zoipa zina.
29
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumakonza bwino manda a aneneri, ndipo mumakongoletsa ziliza za anthu olungama.
30
Ndiye mumati, ‘Tikadakhala ndi moyo pa nthaŵi ya makolo athu ija, sibwenzi ife titaŵapha nao aneneriwo ai.’
31
Koma potero mukuvomera nokha kuti ndinu zidzukulu za anthu amene adapha aneneriwo.
32
Chabwino tsono, itsirizeni ntchitoyo imene makolo anu aja adaiyamba.”
33
“Njoka inu, ana a mamba, mudzachipeŵa bwanji chilango cha ku Gehena?
34
Mvetsetsani tsono! Ine ndidzakutumizirani aneneri, ndiponso anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena mudzaŵapha ndi kuŵapachika pa mtanda. Ena mudzaŵakwapula m'nyumba zanu za mapemphero, ndipo mudzaŵazunza pakuŵapirikitsa kuchokera ku mudzi wina mpaka ku mudzi wina.
35
Motero chilango chidzakugwerani chifukwa cha anthu olungama onse amene adaphedwa, kuyambira kuphedwa kwa Abele, munthu wolungama uja, mpaka kuphedwa kwa Zakariya, mwana wa Barakiya, amene mudamuphera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa lansembe ndi Malo Opatulika kopambana.
36
Ndithu ndikunenetsa kuti chilango cha zonsezi chidzaŵagwera ndithu anthu amakonoŵa.”
37
“Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri, nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana!
38
Ndithu nyumba yanu yaikuluyi idzasanduka bwinja.
39
Ndipo ndikunenetsa kuti simudzandiwonanso konse mpaka mudzati, ‘Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye.’ ”
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28