bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 19
Matthew 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 20 →
1
Yesu atatsiriza kunena mau ameneŵa, adachoka ku Galileya nakafika ku dera la Yudeya kutsidya kwa mtsinje wa Yordani.
2
Anthu ambirimbiri adamtsata, ndipo Iye ankachiritsa odwala kumeneko.
3
Afarisi ena adadza kwa Iye. Tsono kufuna pomupezera chifukwa, adamufunsa kuti, “Kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”
4
Yesu adaŵayankha kuti, “Kodi simunaŵerenge kuti Mulungu amene adalenga anthu pa chiyambi, adalenga wina wamwamuna, wina wamkazi?
5
Ndipo kuti Iye yemweyo adati, ‘Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ake ndi amai ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’
6
Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”
7
Afarisi aja adamufunsa kuti, “Nanga bwanji Mose adalamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo kenaka nkumuchotsa?”
8
Yesu adaŵayankha kuti, “Mose adaakulolani kusudzula akazi anu chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pa chiyambi sizinali choncho ai.
9
Tsono ndikunenetsa kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, nakwatira wina, akuchita chigololo.”
10
Ophunzira ake adamuuza kuti, “Ndiyetu ngati zili choncho pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, ndi bwino tsono kusakwatira.”
11
Yesu adaŵauza kuti, “Si anthu onse angamvetse zimenezi ai, koma okhawo amene Mulungu aŵathandiza.
12
Paja pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa adabadwa motero. Pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa anthu adaŵafula. Pali enanso amene adachita kusankha okha kusakwatira, kuti azitumikira bwino Mulungu. Yemwe angathe kumvetsa, amvetse.”
13
Anthu ena ankabwera ndi ana kuti Yesu aŵasanjike manja ndi kuŵapempherera, ophunzira ake nkumaŵazazira.
14
Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”
15
Atatero adaŵasanjika manja, kenaka nkumapita.
16
Munthu wina wachinyamata adadza kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndizichita chabwino chanji kuti ndikalandire moyo wosatha?”
17
Yesu adamuyankha kuti, “Bwanji ukundifunsa za chimene chili chabwino? Wabwino ndi Mmodzi yekha. Ngati ufuna kukaloŵa ku moyo, uzimvera Malamulo.”
18
Iye adati, “Malamulo ake oti?” Yesu adayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama,
19
lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
20
Munthu uja adati, “Malamulo onseŵa ndakhala ndikuŵatsata, nanga chanditsaliranso nchiyani?”
21
Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”
22
Koma pamene munthu uja adamva mau ameneŵa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa anali wolemera kwambiri.
23
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti nkwapatali kwambiri kuti munthu wolemera adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba.
24
Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”
25
Pamene ophunzira aja adamva zimenezi, adadabwa kwambiri nati, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?”
26
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”
27
Pamenepo Petro adayankhapo kuti, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani. Tsono ndiye kuti tidzalandira chiyani?”
28
Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu akadzakonzanso zinthu zonse, Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake wachifumu ndi waulemerero. Tsono inunso amene mudanditsatanu, mudzakhala pa mipando yachifumu khumi ndi iŵiri mukuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.
29
Motero aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ameneyo adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka adzalandira moyo wosatha.
30
Komatu ambiri amene ali oyambirira adzakhala otsirizira, ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.”
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28