bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 3
Matthew 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 4 →
1
Pa masiku amenewo kudaabwera Yohane Mbatizi nayamba kulalika m'chipululu cha ku Yudeya.
2
Ankati, “Tembenukani mtima chifukwa Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.”
3
Paja Yesaya ankanena za iyeyu pamene adaati, “Liwu la munthu wofuula m'chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.’ ”
4
Yohaneyo ankavala zovala za ubweya wangamira, ndipo ankamangira lamba wachikopa m'chiwuno. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wam'thengo.
5
Anthu ochokera ku Yerusalemu ndi ku dera lonse la Yudeya, ndi ku madera onse a pafupi ndi mtsinje wa Yordani ankadza kwa iye.
6
Ndiye ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumaŵabatiza mu Mtsinje wa Yordaniwo.
7
Ankaona Ayuda ambiri a m'gulu la Afarisi ndi la Asaduki akubwera kuti iye aŵabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthaŵe chilango cha Mulungu chikudzachi?
8
Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima.
9
Ndipo m'mitima mwanu musayerekeze zomanena kuti, ‘Atate athu ndi Abrahamu.’ Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu angathe kusandutsa ngakhale miyala ili apayi kuti ikhale ana a Abrahamu.
10
Pali pano nkhwangwa ili kale patsinde pa mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, adzaudula nkuuponya pa moto.
11
“Ine ndimakubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenuka mtima. Koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto.
12
Chopetera chake chili m'manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m'nkhokwe, koma mankhusu adzaŵatentha m'moto wosazimika.”
13
Pa masiku amenewo Yesu adachoka ku Galileya kubwera kwa Yohane ku mtsinje wa Yordani, kuti Yohaneyo amubatize.
14
Yohane poyesa kukana, adati, “Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi Inuyo. Nanga mukubweranso kwa ine kodi?”
15
Koma Yesu adamuyankha kuti, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m'mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera.
16
Yesu atangobatizidwa, adatuluka m'madzimo. Pomwepo kuthambo kudatsekuka, ndipo adaona Mzimu wa Mulungu akutsika ngati nkhunda nkutera pa Iye.
17
Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera naye kwambiri.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28