bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 13
Matthew 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 14 →
1
Tsiku lomwelo Yesu adatuluka m'nyumba nakakhala pansi m'mbali mwa nyanja.
2
Anthu ambirimbiri adasonkhana kumene kunali Iye. Tsono Yesu adaloŵa m'chombo nakhala pansi, anthu onse aja ataima pa mtunda.
3
Yesu adalankhula nawo zambiri m'mafanizo. Adati, “Munthu wina adaapita kukafesa mbeu.
4
Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira, ndipo mbalame zidabwera nkuzitolatola.
5
Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga chifukwa nthakayo inali yosazama.
6
Koma pamene dzuŵa lidakwera, zidapserera kenaka zidauma, chifukwa zinali zosazika mizu.
7
Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija.
8
Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino, ndipo zidabereka. Ngala zina zinali ndi njere makumi khumi, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi atatu.”
9
Tsono Yesu adati, “Amene ali ndi makutu, amve!”
10
Pambuyo pake ophunzira a Yesu aja adadzamufunsa kuti, “Kodi bwanji anthuŵa mumalankhula nawo m'mafanizo?”
11
Iye adati, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wakumwamba. Koma enaŵa sadaŵaululire ai.
12
Pajatu amene ali nkanthu kale, adzampatsanso zina, nadzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe kanthu, adzamlanda ngakhale kakang'onong'ono kamene ali nako.
13
Tsono anthuŵa ndimalankhula nawo m'mafanizo, chifukwa ngakhale amapenya, komabe saona, ndipo ngakhale amamva, komabe samva kwenikweni kapena kumvetsa.
14
Ndi iwoŵa zikuchitikadi zimene mneneri Yesaya adaanena kuti, “ ‘Kumva mudzamva ndithu, koma osamvetsa, kuyang'ana mudzayang'ana ndithu, koma osapenya.
15
Ndithu anthu ameneŵa nzeru zao nzobuntha, adagonthetsa makutu ao, ndipo adapsinya maso ao, kuwopa kuti angamapenye ndi maso aowo, angamamve ndi makutu aowo, angamamvetse ndi nzeru zaozo, ndi kutembenuka mtima, Ineyo nkuŵachiritsa.’
16
“Koma inu ndinu odala, popeza kuti maso anu akupenya, ndipo makutu anu akumva.
17
Kunena zoona aneneri ambiri ndi anthu ambiri olungama, adaafunitsitsa kuwona zimene inu mukupenyazi, koma sadaziwone. Adaafunitsitsa kumva zimene inu mukumvazi, koma sadazimve.”
18
“Tsono inu mumvetse bwino tanthauzo lake la fanizo la munthu wofesa mbeu lija.
19
Munthu aliyense akamva mau onena za Ufumu wakumwamba, koma osaŵamvetsa, Woipa uja amabwera nkudzalanda zimene zidafesedwa mumtima mwake. Zimenezi ndiye mbeu zogwera m'njira zija.
20
Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu, nthaŵi yomweyo nkuŵalandira ndi chimwemwe.
21
Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangolimbika kanthaŵi pang'ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthaŵi yomweyo munthuyo amabwerera m'mbuyo.
22
Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu. Koma kutanganidwa ndi za pansi pano ndi kukondetsa chuma kumafooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso.
23
Koma mbeu zofesedwa pa nthaka yabwino zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu naŵamvetsa. Munthu wotere amaberekadi zipatso, mwina makumi khumi, mwina makumi asanu ndi limodzi, mwina makumi atatu.”
24
Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaafesa mbeu zabwino m'munda mwake.
25
Koma anthu onse ali m'tulo, mdani wake adabwera, nkufesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.
26
Tsono pamene mmera udakula nkuyamba kuchita njere, namsongole uja nayenso adayamba kuwoneka.
27
Antchito a mwinimunda uja adadzamufunsa kuti, ‘Bwana, kodi suja mudaafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga bwanji mukuwonekanso namsongole?’
28
Iye adaŵayankha kuti, ‘Ndi mdani amene wachita zimenezi.’ Antchito aja adamufunsa kuti, ‘Bwanji tikamzule?’
29
Koma iye adati, ‘Iyai, mungakazulire kumodzi ndi tirigu pozula namsongoleyo.
30
Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula. Pa nthaŵi imeneyo ndidzauza odula kuti, Yambani mwazula namsongole, mummange m'mitolo kuti mukamtenthe. Kenaka musonkhanitse tirigu ndi kukamthira m'nkhokwe yanga.’ ”
31
Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m'munda mwake.
32
Ndi yaing'ono kwambiri mukaiyerekeza ndi njere zina zonse. Komabe mbeu yake ikakula, imapambana zitsamba zina zonse. Imasanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.”
33
Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.”
34
Zonsezi Yesu adalankhula ndi anthu aja m'mafanizo. Sadalankhule nawo kanthu popanda fanizo.
35
Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri adaanena kuti, “Ndidzalankhula nawo m'mafanizo. Ndidzaulula zimene zinali zobisika chilengedwere dziko lapansi.”
36
Pambuyo pake Yesu adaŵasiya anthu ambirimbiri aja, nakaloŵa m'nyumba. Tsono ophunzira ake adadzampempha kuti, “Tatimasulirani fanizo la namsongole wam'munda lija.”
37
Yesu adati, “Wofesa mbeu zabwino uja ndi Mwana wa Munthu.
38
Munda uja ndi dziko lino lapansi. Mbeu zabwino zija ndi anthu ake a Ufumu wakumwamba. Namsongole uja ndi anthu ake a Woipa uja.
39
Mdani wodzafesa namsongole uja ndi Satana. Kudula kuja nkutha kwake kwa dziko lino lapansi, ndipo odula aja ndi angelo.
40
Monga momwe adaazulira namsongole uja nkumutentha pa moto, zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi.
41
Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake kudzachotsa mu Ufumu wake anthu onse ochimwitsa anzao, ndi ena onse ochita zoipa,
42
nadzaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.
43
Tsono anthu olungama adzaŵala ngati dzuŵa mu Ufumu wa Atate ao. Amene ali ndi makutu, amve!
44
“Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m'munda. Munthu wina atachitumba, amachibisanso. Kenaka mokondwa amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula munda uja.
45
“Ndiponso Ufumu wakumwamba uli ngati munthu wamalonda wonka nafunafuna ngale zokongola zamtengowapatali.
46
Atapeza ngale imodzi yamtengowapatali kwambiri, amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula ngale ija.
47
“Ufumu wakumwamba ulinso ngati khoka limene anthu amaliponya m'nyanja, ndipo limagwira nsomba za mitundu yonse.
48
Likadzaza, anthu amalikokera ku mtunda. Tsono amakhala pansi, nsomba zabwino nkumaziika m'madengu, zachabe nkumangozitaya.
49
Zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. Angelo adzabwera nadzachotsa anthu ochimwa pakati pa anthu olungama,
50
nkumaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”
51
Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Mwazimvetsa zonsezi kodi?” Iwo adati, “Inde.”
52
Apo Iye adaŵauza kuti, “Nchifukwa chaketu mphunzitsi aliyense wa Malamulo, amene adaphunzira za Ufumu wakumwamba, ali ngati mwinibanja amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zinthu zakale m'nkhokwe ya chuma chake.”
53
Yesu atatsiriza kunena mafanizoŵa, adachoka kumeneko.
54
Atafika ku dera lakwao, adayamba kuphunzitsa anthu m'nyumba yao yamapemphero. Amene ankamumva ankadabwa nkumati, “Kodi Iyeyu, nzeru zimenezi ndi mphamvuzi adazitenga kuti?
55
Kodi ameneyu si mwana wa mmisiri wa matabwa uja? Kodi suja mai wake ndi Maria? Ndipo abale ake si Yakobe, Yosefe, Simoni ndi Yuda?
56
Kodi suja alongo ake onse ali nafe pompano? Nanga tsono zonsezi adazitenga kuti?”
57
Choncho adakhumudwa naye. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao ndiponso kubanja kwao.”
58
Motero sadachite zamphamvu zambiri kumeneko, chifukwa cha kusakhulupirira kwa anthuwo.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
Recommended Reading
Commentary
Matthew Commentaries
→
Devotional
Matthew Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→