bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 24
Matthew 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 25 →
1
Yesu adatuluka m'Nyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankachoka, ophunzira ake adabwera nkumamuwonetsa kamangidwe ka Nyumbayo.
2
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Nanga simukuziwona zonsezi? Ndithu ndikunenetsa kuti sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.”
3
Tsono Yesu atakhala pansi, pa Phiri la Olivi, ophunzira ake adadza kwa Iye paokha. Adamufunsa kuti, “Tatiwuzani, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti nthaŵi yakwana ya kubweranso kwanu, ndiponso ya kutha kwa dziko lapansi?”
4
Yesu adaŵayankha kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni.
5
Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine,’ ndipo adzasokeza anthu ambiri.
6
Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.
7
Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.
8
Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto.
9
“Pambuyo pake anthu adzakuperekani kuti mukazunzidwe, kenaka adzakuphani. Anthu a mitundu yonse ya anthu adzadana nanu chifukwa cha Ine.
10
Pa nthaŵi imeneyo ambiri adzataya chikhulupiriro chao, azidzaperekana nkumadana.
11
Kudzaoneka aneneri onama ambiri, amene azidzasokeza anthu ambiri.
12
Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu.
13
Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
14
Ndipo Uthenga Wabwinowu wonena za ufumu wa Mulungu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, kuti anthu a mitundu yonse apezepo umboni. Pamenepo ndiye chimalizo chidzafike.”
15
“Mudzaona ‘Chosakaza chonyansa chija’ chimene mneneri Daniele adaanena, atachiimika m'Nyumba ya Mulungu. (Amene ukuŵerengawe, umvetse bwino.)
16
Pamenepo amene ali ku Yudeya athaŵire ku mapiri.
17
Amene ali padenga pa nyumba yake, asatsike nkuloŵanso m'nyumba mwake kuti akatenge katundu.
18
Yemwe ali ku munda, asabwererenso ku nyumba kuti akatenge mwinjiro.
19
Ali ndi tsoka azimai amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo.
20
Pempherani kuti nthaŵi pamene muzidzathaŵa, isadzakhale nyengo yachisanu, kapena pa tsiku la Sabata.
21
Chifukwa masautso amene adzaoneka masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso.
22
Masiku amenewo, akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma Mulungu adzaŵachepetsa masikuwo chifukwa cha anthu amene Iye adaŵasankha.
23
“Pa nthaŵi imeneyo wina akadzakuuzani kuti, ‘Ali panotu Khristu uja! Uyo ali apoyo!’ musadzakhulupirire.
24
Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
25
Mvetsetsani, Ine ndiye ndakuuziranitu zimenezi.
26
“Nchifukwa chake, anthu akadzakuuzani kuti, ‘Inu, Khristu ali ku chipululu,’ musadzapiteko. Kapena akadzati, ‘Ali m'kati mwa nyumba,’ musadzakhulupirire.
27
Mwana wa Munthutu kubwera kwake kudzakhala monga muja mphezi imang'animira ndi kuŵala kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe.
28
“Paja adati, Kulikonse kumene kwafera chinthu, miphamba imasonkhana kumeneko.”
29
“Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala, nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka.
30
Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka ku thambo. Anthu a mitundu yonse ya pansi pano adzayamba kulira, ndipo adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.
31
Kudzamveka lipenga lamphamvu, ndipo Iye adzatuma angelo ake, kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”
32
“Yang'anani mkuyu kuti mutengerepo phunziro. Mukamaona kuti nthambi zake zayamba kukhala zanthete, ndipo masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira.
33
Momwemonso, mukadzaona zonse ndanena zija, mudzadziŵe kuti Mwana wa Munthu ali pafupi, ali pakhomo penipeni.
34
Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse.
35
Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.”
36
“Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa; amadziŵa ndi Atate okha basi.
37
Kudza kwa Mwana wa Munthu kudzakhala monga momwe zinthu zidaayendera pa nthaŵi ya Nowa.
38
Masiku amenewo, chisanafike chigumula, anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo.
39
Sadazindikire kanthu mpaka chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Zidzateronso pamene Mwana wa Munthu adzabwera.
40
Pa nthaŵi imeneyo anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.
41
Azimai aŵiri adzakhala akusinja, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.
42
“Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziŵa tsiku limene Ambuye anu adzabwere.
43
Koma dziŵani kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba.
44
Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene inu simukuyembekeza.”
45
“Tsono wantchito wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adamuika kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake?
46
Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi.
47
Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse.
48
Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa.’
49
Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, ndiponso kumadya ndi kumamwa pamodzi ndi zidakwa.
50
Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza.
51
Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu achiphamaso. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28