bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 18
Matthew 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 19 →
1
Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adadzamufunsa Yesu kuti, “Kodi mu Ufumu wakumwamba wamkulu koposa onse ndani?”
2
Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao,
3
ndipo adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.
4
Nchifukwa chake munthu wodzichepetsa ngati mwana uyu, ameneyo ndiye wamkulu mu Ufumu wakumwamba.
5
Ndipo aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene.”
6
“Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukammiza m'nyanja pozama.
7
Ali ndi tsoka anthu apansipano chifukwa cha zochimwitsa. Zochimwitsazo sizingalephere kuwoneka, koma ali ndi tsoka munthu wobweretsa zochimwitsayo.
8
“Tsono ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli woduka dzanja kapena phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wosatha uli ndi manja onse kapena mapazi onse aŵiri.
9
Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wa Gehena uli ndi maso aŵiri.”
10
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
11
“Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzapulumutsa amene adatayika.”]
12
“Tsono mukuganiza bwanji? Munthu atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nkutayika, kodi sangasiye 99 zina zija m'phiri nkukafunafuna imodzi yotayikayo?
13
Ndithu ndikunenetsa kuti ataipeza, chimwemwe chake chokondwerera imeneyo chimapambana chokondwerera zina zija zimene sizidatayike.
14
Chonchonso Atate anu amene ali Kumwamba safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike.
15
“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo.
16
Koma akapanda kukumvera, utengerepo wina mmodzi kapena ena aŵiri, kuti mau onse akatsimikizike ndi mboni ziŵiri kapena zitatu.
17
Akapanda kuŵamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho.
18
“Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.
19
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani.
20
Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”
21
Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?”
22
Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.
23
“Tsono Ufumu wakumwamba tingaufanizire motere: Panali mfumu ina imene idaaitanitsa antchito ake kuti iwonenso bwino ngongole zao.
24
Atangoyamba kumene, adabwera ndi wantchito wina amene anali ndi ngongole ya ndalama zochuluka kwabasi.
25
Ndiye popeza kuti adaasoŵa chobwezera ngongoleyo, mbuye wake uja adalamula kuti amgulitse wantchitoyo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake ndi zake zonse, kuti ngongole ija ibwezedwe.
26
Apo wantchito uja adamgwadira nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani ndithu zonse.’
27
Mbuye wake uja adamumveradi chifundo, ndipo adamkhululukira ngongole ija, namlola kuti apite.
28
“Koma pamene wantchitoyo ankatuluka, adakumana ndi mmodzi mwa antchito anzake, yemwe iye adaamkongoza ndalama zochepa. Adamgwira pa khosi mwaukali namuuza kuti, ‘Bweza ngongole yako ija.’
29
Apo wantchito mnzake uja adadzigwetsa pansi ku mapazi ake nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani.’
30
Koma iye adakana, nakamponyetsa m'ndende kuti mpaka abweze ndithu ngongoleyo.
31
“Antchito anzake ena ataona zimenezi, adamva chisoni kwambiri. Adapita kukafotokozera mbuye wao zonsezo.
32
Tsono mbuye wakeyo adamuitana namuuza kuti, ‘Wantchito woipa iwe, ine ndinakukhululukira ngongole yonse ija pamene unandidandaulira.
33
Kodi sunayenera kuti iwenso umchitire chifundo wantchito mnzako, monga ndinakuchitira iwe chifundo?’
34
Motero mbuye wakeyo adapsa mtima kwambiri, nampereka kuti akamzunze mpaka atabweza ngongole yonse ija.
35
“Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.”
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28