bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 9
Matthew 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 10 →
1
Yesu adaloŵa m'chombo naoloka nyanja, nkukafika ku mzinda wakwao.
2
Kumeneko anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu wa ziwalo zakufa ali chigonere pa machira. Poona chikhulupiriro chao, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Limba mtima, mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”
3
Apo aphunzitsi ena a Malamulo adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Munthu ameneyu akuchita chipongwe Mulungu.”
4
Koma Yesu adaadziŵa zimene iwo ankaganiza, motero adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuganiza zoipa mumtima mwanu?
5
Chapafupi koposa nchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, yamba kuyenda?’
6
Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”
7
Munthu uja adadzukadi namapita kwao.
8
Anthu onse aja ataona zimenezi, adachita mantha, ndipo adatamanda Mulungu amene adapatsa anthu mphamvu zotere.
9
Yesu atachoka pamenepo, adaona munthu wina, dzina lake Mateyo, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.” Iye adanyamuka nkumamutsatadi.
10
Tsono pamene Yesu ankadya m'nyumba, kudabwera anthu ambiri okhometsa msonkho, ndi anthu ochimwa, kudzadya nao ndi Yesuyo ndi ophunzira ake.
11
Pamene Afarisi adaona zimenezi, adafunsa ophunzira a Yesu kuti, “Bwanji aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi okhometsa msonkho ndiponso ndi anthu ochimwa?”
12
Yesu atamva zimenezo, adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala.
13
Kamvetsetseni tanthauzo la mau a Mulungu aja akuti, ‘Ndimafuna chifundo, osati nsembe ai.’ Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa.”
14
Pambuyo pake ophunzira a Yohane Mbatizi adabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Kodi bwanji ife ndi Afarisi timasala zakudya kaŵirikaŵiri, pamene ophunzira anu sasala nkomwe?”
15
Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.
16
Munthu satenga chigamba cha nsalu yatsopano, nkuchisokerera pa chovala chakale. Chigamba chotere chimakoka nkunyotsolako chovalacho, ndiye kung'ambika kwake kumakhala kwakukulu koposa kale.
17
Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, matumbawo amaphulika, vinyoyo natayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso. Apo zonse ziŵiri zimasungika bwino.”
18
Pamene Yesu ankakamba zimenezi, munthu wina wamkulu adadzamgwadira nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira tsopano apa. Chonde bwerani mudzamsanjike manja, kuti akhale ndi moyo.”
19
Pamenepo Yesu adanyamuka, namtsatira pamodzi ndi ophunzira ake.
20
Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake.
21
Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale chovala chake chokhacho, ndichira.”
22
Pamenepo Yesu adacheuka, naona maiyo, ndipo adati, “Limbani mtima mai, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani.” Nthaŵi yomweyo mai uja adachiradi.
23
Pamene Yesu adafika kunyumba kwa mkulu uja, adaona anthu oimba zitoliro, ndiponso anthu ambiri obuma.
24
Tsono Iye adaŵauza kuti, “Tatulukani! Mtsikanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.” Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola.
25
Koma onsewo atatulutsidwa, Yesu adaloŵa, nagwira mtsikanayo pa dzanja, iye nkuuka.
26
Mbiri imeneyi idawanda m'dera lonselo.
27
Pamene Yesu ankachoka kumeneko, anthu aŵiri akhungu adamtsatira. Ankafuula kuti, “Inu Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.”
28
Yesu ataloŵa m'nyumba, akhungu aja adadzampeza, Iye nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukukhulupirira kuti ndingathe kuchita zimenezi?” Iwo adati, “Inde, Ambuye.”
29
Apo Yesu adakhudza maso ao nati, “Zikuchitikireni monga momwe mwakhulupiriramo.”
30
Pamenepo maso ao adaphenyuka. Tsono Yesu adaŵalamula mwamphamvu kuti, “Wina aliyense asazidziŵetu zimenezi.”
31
Koma iwo adachoka pamenepo nkumakawanditsa mbiri yake ku dera lonselo.
32
Pamene iwowo ankatuluka m'nyumbamo, anthu ena adabwera kwa Yesu ndi munthu wosatha kulankhula, chifukwa chogwidwa ndi mzimu woipa.
33
Yesu atatulutsa mzimu woipawo, munthu uja adayamba kulankhula. Apo anthu onse adazizwa nati, “Nkale lonse Aisraele sadaziwone zotere.”
34
Koma Afarisi adati, “Ameneyu amatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu zomupatsa mfumu ya mizimu yoipa ija.”
35
Yesu adayendera mizinda ndi midzi yonse. Adanka naphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, nkumalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wakumwamba. Ndiponso ankachiritsa nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
36
Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.
37
Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito.
38
Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28