bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 16
Matthew 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 17 →
1
Tsiku lina kudabwera Afarisi ndi Asaduki ena kwa Yesu. Adampempha kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba. Pakutero ankangofuna kumutchera msampha.
2
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Pamene dzuŵa likuloŵa, mumati, ‘Maŵa kucha bwino, popeza kuti kumwamba kuli psuu.’
3
Ndipo m'maŵa mumati, ‘Lero ndiye kugwa mvula yamkuntho, popeza kuti kumwambaku kwachita mitambo yabii.’ Mumatha kutanthauzira m'mene kukuwonekera kumwambaku, koma osatha kutanthauzira zizindikiro za nthaŵi zino.
4
Anthu a mbadwo woipa ndi wosakhulupirika amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzaona chizindikiro china kupatula chokha chija cha mneneri Yona.” Atatero, Yesu adaŵasiya nachokapo.
5
Pamene ophunzira aja adakafika kutsidya, anali ataiŵala kutenga buledi.
6
Yesu adaŵauza kuti, “Muchenjere nacho chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi Asaduki.”
7
Apo ophunzirawo adayamba kukambirana nkumati, “Akuterotu chifukwa sitidatenge buledi.”
8
Yesu adaadziŵa zimene iwo ankanena. Ndiye adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukukambirana zakuti mulibe buledi, inu a chikhulupiriro chochepanu?
9
Kodi mpaka pano simunamvetsebe? Kodi simukukumbukira kuti ndi buledi msanu ndidadyetsa anthu zikwi zisanu? Nanga mudaadzaza madengu angati ndi zotsala?
10
Sujanso ndi buledi msanu ndi muŵiri ndidadyetsa anthu zikwi zinai? Nanga mudaadzaza madengu angati a zotsala?
11
Nanga bwanji simukuzindikira kuti sindimanena za buledi? Chenjera nachoni chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi Asaduki.”
12
Pamenepo iwo adazindikira kuti Yesu sankaŵauza kuti achenjere ndi chofufumitsira buledi, koma kuti achenjere ndi zophunzitsa za Afarisi ndi Asaduki.
13
Pamene Yesu adafika ku madera a ku Kesareya-Filipi, adafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthune ndine yani?”
14
Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu Yeremiya kapena mmodzi mwa aneneri.”
15
Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?”
16
Simoni Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu wamoyo.”
17
Yesu adamuuza kuti, “Ndiwe wodala, Simoni mwana wa Yona, pakuti si munthu wakuululira zimenezi ai, koma ndi Atate anga amene ali Kumwamba.
18
Ndipo Ine ndikuti, Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa.
19
Ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.”
20
Yesu atanena zimenezi, adalamula ophunzira aja kuti asauze munthu aliyense kuti Iye ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
21
Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kudziŵitsa ophunzira ake kuti, “Ndiyenera kupita ku Yerusalemu, kumeneko akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzandizunza kwambiri. Ndidzaphedwa koma mkucha wake ndidzauka.”
22
Apo Petro adamtengera pambali nayamba kumdzudzula. Adati, “Pepani Ambuye, zisatero ai. Mulungu asalole zimenezi.”
23
Koma Yesu adacheuka namdzudzula. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Ufuna kundilakwitsa. Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.”
24
Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata.
25
Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.
26
Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?
27
Ndipotu Mwana wa Munthu adzabwera ndi angelo ake ali ndi ulemerero wa Atate ake. Pamenepo adzabwezera aliyense molingana ndi zochita zake.
28
Ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Mwana wa Munthu akubwera ndi ulemerero waufumu.”
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28