bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Matthew 8
Matthew 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 9 →
1
Yesu atatsika kuphiri kuja, anthu ambirimbiri adamtsatira.
2
Tsono munthu wina wakhate adadzamugwadira nati, “Ambuye, mutafuna mungathe kundichiritsa.”
3
Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi.
4
Tsono Yesu adamuuza kuti, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyi ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.”
5
Pamene Yesu ankaloŵa m'mudzi wa Kapernao, mkulu wina wolamulira gulu la asilikali 100 achiroma adadza kwa Iye.
6
Adampempha kuti, “Ambuye, wantchito wanga ali gone kunyumbaku. Sakutha kuyenda, ndipo akumva kupweteka kwambiri.”
7
Yesu adamuuza kuti, “Chabwino, ndibwera kudzamchiritsa.”
8
Koma mkulu uja adati, “Ambuye, sindili woyenera kuti Inu nkuloŵa m'nyumba mwanga. Mungonena mau okha, ndipo wantchito wangayo achira.
9
Inetu ndili ndi akuluakulu ondilamulira, komanso ndili ndi asilikali amene ineyo ndimaŵalamulira. Ndimati ndikauza wina kuti, ‘Pita,’ amapitadi. Ndikauzanso wina kuti, ‘Bwera,’ amabweradi. Ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Chita chakuti,’ amachitadi.”
10
Yesu atamva zimenezi, adachita chidwi, ndipo adauza anthu amene ankamutsata aja kuti, “Kunena zoona, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere.
11
Ndithu ndikunenetsa kuti ambiri adzabwera kuchokera kuvuma ndi kuzambwe nadzakhala nao pa phwando mu Ufumu wakumwamba pamodzi ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
12
Koma chonsecho amene akadayenera kukhala mu Ufumuwo, adzaŵaponya kunja, ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano chifukwa cha zoŵaŵa.”
13
Kenaka pouza mkulu wa asilikali uja Yesu adati, “Inu pitani bwino, zikuchitikireni monga momwe mwakhulupiriramu.” Tsono wantchito wake uja adachira nthaŵi yomweyo.
14
Pamene Yesu adakaloŵa m'nyumba ya Petro, adaona apongozi a Petro ali gone, akudwala malungo.
15
Adakhudza amaiwo pa dzanja, ndipo malungowo adatha. Pomwepo amai aja adadzuka nayamba kukonzera Yesu chakudya.
16
Madzulo amenewo, anthu adabwera kwa Yesu ndi anzao ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa. Yesu adaitulutsa mizimuyo ndi mau chabe, ndipo onse amene ankadwala adaŵachiritsa.
17
Adachita zimenezi kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena zakuti, “Iye adatenga zofooka zathu, adasenza nthenda zathu.”
18
Pamene Yesu adaona chinamtindi cha anthu amene adaamuzinga, adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.”
19
Koma nthaŵi yomweyo padafika mphunzitsi wina wa Malamulo namuuza kuti, “Aphunzitsi, ndizikutsatani kulikonse kumene muzipita.”
20
Yesu adamuyankha kuti, “Nkhandwe zili ndi michembo yake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe mpogoneka mutu pomwe.”
21
Wophunzira wake wina adauza Yesu kuti, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakaika maliro a atate anga.”
22
Koma Yesu adamuuza kuti, “Iweyo unditsate, aleke akufa aziika akufa anzao.”
23
Yesu adaloŵa m'chombo, ndipo ophunzira ake adatsagana naye.
24
Tsono padauka namondwe woopsa panyanjapo, kotero kuti mafunde ankaloŵa m'chombomo. Koma Yesu anali m'tulo.
25
Pamenepo ophunzira ake aja adamudzutsa, adati, “Ambuye, tipulumutseni, tikumiratu!”
26
Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha, inu anthu a chikhulupiriro chochepa?” Atatero adaimirira nkudzudzula mphepoyo ndi nyanjayo, kenaka padagwa bata lalikulu ndithu.
27
Ophunzira aja adazizwa nati, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja yomwe zizimumvera?”
28
Yesu atafika ku tsidya la nyanja, ku dera la Agadara, anthu aŵiri ogwidwa ndi mizimu yoipa adadzakumana naye kuchokera ku manda. Anali aukali kwambiri, kotero kuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe wotha kudzera njira imeneyo.
29
Mwadzidzidzi anthuwo adayamba kufuula kuti, “Kodi takuputani chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthaŵi isanakwane?”
30
Pafupi pomwepo pankadya gulu lalikulu la nkhumba.
31
Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti, “Mukatitulutsa, bwanji mutitume kuti tikaloŵe m'gulu la nkhumba zili apozo.”
32
Yesu adaiwuza kuti, “Chabwino, pitani!” Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja mpaka kufera m'madzimo.
33
Oŵeta nkhumbazo adathaŵa. Atakaloŵa mu mzinda, adakasimbira anthu zonse zimene zidachitika, ndiponso zimene zidaŵaonekera ogwidwa ndi mizimu yoipa aja.
34
Pamenepo anthu onse amumzindamo adatuluka kuti akakumane ndi Yesu. Tsono atampeza, adamupempha kuti achoke ku dera laolo.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28