bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 1
Acts 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 2 →
1
A Teofilo, M'buku langa loyamba lija ndidakulemberani za zonse zimene Yesu ankachita ndi kuphunzitsa kuyambira pa chiyambi,
2
kufikira tsiku limene adatengedwa kupita Kumwamba. Mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, anali atauza atumwi amene adaŵasankha aja zoti iwowo adzachite.
3
Iye ataphedwa, adadziwonetsa wamoyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adaŵaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai.
4
Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adaŵalamula kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani.
5
Pajatu Yohane ankabatiza ndi madzi, koma pasanapite masiku ambiri, inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”
6
Tsono atumwi aja atasonkhana, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi ino ndiyo nthaŵi yoti mukhazikitsenso ufumu mu Israele?”
7
Iye adati, “Si ntchito yanu kuti mudziŵe nthaŵi kapena nyengo pamene zidzachitike zimene Atate adakhazikitsa mwa mphamvu yao.
8
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
9
Atanena zimenezi, Yesu adatengedwa kupita Kumwamba, iwo akupenya. Ndipo mtambo udamlandira nkumubisa, iwo osamuwonanso.
10
M'mene atumwi aja ankayang'anitsitsabe kumwamba, Iye akupita, mwadzidzidzi anthu aŵiri ovala zoyera adaimirira pambali pao.
11
Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Inu anthu a ku Galileya, mwatani mwangoti chilili pamenepa mukuyang'ana kumwamba? Yesuyu amene watengedwa kuchokera pakati panu kupita Kumwamba, adzabweranso monga momwe mwamuwoneramu akupita Kumwambako.”
12
Tsono atumwi aja adabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Phiri la Olivi. Mtunda wake kuchokera ku Yerusalemu ngwosakwanira ngakhale mtunda umodzi.
13
Ataloŵa mumzindamo, adakwera ku chipinda cham'mwamba kumene ankakhala: panali Petro, Yohane, Yakobe ndi Andrea; Filipo ndi Tomasi; Bartolomeo ndi Mateyo; Yakobe (mwana wa Alifeyo,) ndi Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote,) ndiponso Yudasi (mwana wa Yakobe.)
14
Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena, ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.
15
Tsiku lina, patapita masiku angapo, Petro adaimirira pakati pa abale. (Anthuwo onse pamodzi anali ngati 120.) Iye adati,
16
“Abale anga, kunayenera kuti zichitikedi zimene Malembo adaneneratu za Yudasi. Paja kudzera mwa Davide Mzimu Woyera adalankhula za iyeyo amene adatsogolera anthu okagwira Yesu.
17
Yudasiyo anali mmodzi wa gulu lathu, ndipo adaalandira udindo woti azitumikira pamodzi ndi ife.
18
Adagula munda ndi ndalama zimene adapata pochita chosalungama chija. Kumeneko adagwa chamutu, naphulika pakati, matumbo ake onse nkukhuthuka.
19
Anthu onse okhala ku Yerusalemu adamva zimenezi, kotero kuti m'chilankhulo chao mundawo adautcha dzina loti ‘Akeledama,’ ndiye kuti, ‘Munda wa Magazi.’
20
Paja m'buku la Masalimo muli mau akuti, “ ‘Nyumba yake isanduke bwinja, pasakhale munthu wogonamo.’ Muli mau enanso akuti, “ ‘Wina alandire ntchito yake.’
21
“Pali anthu ena amene akhala akutsagana nafe nthaŵi yonse pamene Ambuye Yesu anali pakati pathu,
22
kuyambira pamene Iye adabatizidwa ndi Yohane mpaka tsiku limene adatengedwa kuchoka pakati pathu kupita Kumwamba. Mmodzi mwa anthu ameneŵa akhale mboni pamodzi ndi ife, yakuti Yesu adauka kwa akufa.”
23
Pamenepo iwo adatchula maina aŵiri: Yosefe amene ankamutcha Barsabasi (dzina lake lina ndi Yusto,) ndi Matiasi.
24
Ndipo adapemphera kuti, “Ambuye, Inu amene mumadziŵa mitima ya anthu onse, tiwonetseni ndi uti mwa aŵiriŵa amene mwamusankha
25
kuti alandire ntchito iyi ya utumwi, m'malo mwa Yudasi uja amene adaisiya ndipo adapita ku malo omuyenera.”
26
Tsono adaŵachitira maere anthu aŵiriwo. Maerewo adagwera Matiasi, ndipo iyeyo adawonjezedwa pa gulu lija la atumwi khumi ndi mmodzi.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28