bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 19
Acts 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 20 →
1
Pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo adayendera maiko apamtunda, nakafika ku Efeso. Kumeneko adapezako ophunzira ena,
2
ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi mudalandira Mzimu Woyera pamene mudakhulupirira?” Iwo adati, “Nkumva komwe sitinamve kuti kuli Mzimu Woyera.”
3
Paulo adaŵafunsa kuti, “Nanga tsono mudabatizidwa ndi ubatizo wotani?” Iwo adati, “Ndi ubatizo wa Yohane.”
4
Paulo adati, “Yohane ankabatiza anthu otembenuka mtima, koma iye yemwe ankauza anthuwo kuti akhulupirire wina amene analikudza pambuyo pa iyeyo. Winayo ndiye Yesu.”
5
Okhulupirira aja atamva zimenezi, adabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.
6
Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu.
7
Anthuwo onse pamodzi analipo ngati khumi ndi aŵiri.
8
Paulo adaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda, ndipo pa miyezi itatu adakhala akulankhula molimba mtima. Ankakamba ndi anthu za ufumu wa Mulungu, nayesa kuŵakopa.
9
Koma ena adaumitsa mitima yao, osafuna kukhulupirira, nkumanyoza Njira ya Ambuye pamaso pa gulu lonse. Pamenepo Paulo adaŵasiya nachoka nawo ophunzira aja, ndipo tsiku ndi tsiku ankakambirana m'sukulu ya Tirano.
10
Adachita zimenezi pa zaka ziŵiri, kotero kuti anthu onse okhala ku Asiya, Ayuda ndi Agriki omwe, adamva mau a Ambuye.
11
Mulungu adachita zozizwitsa kwambiri kudzera kwa Paulo.
12
Anthu ankati akatenga zitambaya kapena nsalu zina zimene Paulo ankagwiritsa ntchito, nakaziika pa anthu odwala, odwalawo ankachira, ndipo mizimu yoipa inkatuluka mwa iwo.
13
Ayuda ena oyendayenda, otulutsa mizimu yoipa, nawonso adayesa kutchula dzina la Ambuye Yesu pa anthu ogwidwa ndi mizimu yoipa. Ankati, “M'dzina la Yesu amene Paulo amamlalika, ndikukulamulani kuti mutuluke.”
14
Amene ankachita zimenezi ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri a Skeva, mkulu wa ansembe onse wachiyuda.
15
Koma mzimu woipawo udayankha kuti, “Yesu ndimamdziŵa, Paulonso ndimamdziŵa, koma inuyo ndinu yani?”
16
Kenaka munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa uja adaŵalumphira naŵagwira onse. Adaŵagonjetsa kotero kuti iwowo adathaŵanso m'nyumba muja ali maliseche ndiponso atapwetekedwa.
17
Anthu onse okhala ku Efeso, Ayuda ndi Agriki atamva zimenezi, adachita mantha. Ndipo anthu ankatamanda dzina la Ambuye Yesu kopambana.
18
Ambiri amene tsopano adaayamba kukhulupirira, adabwera nkumavomera poyera ndi kuulula zoipa zimene ankachita.
19
Ambiri amene ankakonda kuchita matsenga, adasonkhanitsa mabuku ao naŵatentha pamaso pa anthu onse. Pamene adaonkhetsa mtengo wa mabukuwo, adapeza kuti udaakwanira ngati ndalama zikwi makumi asanu.
20
Motero mau a Mulungu adanka nafalikirafalikira ndi kugwira ntchito mwamphamvu.
21
Zitachitika zimenezi, Paulo adatsimikiza zopita ku Yerusalemu kudzera ku Masedoniya ndi ku Akaiya. Adati, “Kuchokera kumeneko ndiyeneranso kukayenda ku Roma.”
22
Tsono adatuma Timoteo ndi Erasito ku Masedoniya. Ameneŵa anali aŵiri mwa anthu omuthandiza. Koma mwiniwakeyo adakhalirabe ku Asiya kanthaŵi.
23
Nthaŵi yomweyo padabuka chipolowe chachikulu chifukwa cha Njira ya Ambuye.
24
Mmisiri wina wa ntchito za siliva, dzina lake Demetrio, ankapanga timafanizo tasiliva ta nyumba yopembedzeramo Aritemi, mulungu wao wamkazi, ndipo ntchito yakeyo inkaŵapindulitsa kwambiri antchito ake.
25
Demetrioyo adasonkhanitsa anthu akewo, pamodzi ndi ena ogwira ntchito ya mtundu womwewo, naŵauza kuti, “Abale anga, mukudziŵa kuti chuma chathu chimachokera ku ntchito imeneyi.
26
Mukuwona ndi kumva zimene akuchita mkulu uyu amati Pauloyu. Iye akunena kuti ati milungu yopangidwa ndi anthu si milungu konse. Ndipo wakopa anthu ambiri nkuŵapatutsa, osati ku Efeso kokha kuno ai, komanso pafupi dziko lonse la Asiya.
27
Tsono choopsa nchakuti ntchito yathuyi ifika ponyozeka. Si pokhapo ai, komanso nyumba yopembedzeramo Aritemi, mulungu wathu wamkulu, anthu sadzaiyesa kanthu. Ndiye basitu udzawonongeka ulemerero wonse wa Aritemiyo, amene anthu onse a ku Asiya ndi a pa dziko lonse lapansi amampembedza.”
28
Anthu aja atamva mau ameneŵa, adakwiya kwabasi, nayamba kufuula kuti, “Ndi wamkulu Aritemi wa Aefeso!”
29
Choncho mumzinda monse mudadzaza chisokonezo. Tsono anthuwo adagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, anzake aulendo a Paulo, nathamangira nawo ku bwalo lamaseŵera.
30
Paulo adaafuna kuloŵa pakati pa anthuwo, koma ophunzira sadamloleze.
31
Akulu ena a Boma a ku Asiya komweko, amene anali abwenzi ake, adamtumiranso mau omupempha kuti asaloŵe dala m'bwalo lamaseŵeralo.
32
Msonkhano wonse wa anthu aja udangoti pwirikiti: ena akufuula zina, enanso zina; ambiri osadziŵa ndi chimene asonkhanira chomwe.
33
Ena m'khamumo adaaganiza kuti Aleksandro alipo ndi chonena, ataona kuti Ayuda amkankhira kutsogolo. Tsono iye adakweza dzanja kuti aŵakhalitse chete, kuti afotokozere anthu mlanduwo.
34
Koma pamene anthu aja adazindikira kuti iyeyo ndi Myuda, onsewo adafuula pamodzi pa maola aŵiri kuti, “Ndi wamkulu Aritemi wa Aefeso!”
35
Mlembi wa mzindawo ataŵatontholetsa anthu aja, adaŵauza kuti, “Inu Aefeso, ndani amene sadziŵa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo wosunga nyumba yopembedzeramo Aritemi wamkulu, ndiponso wosunga mwala wopatulika uja umene udachita kugwa kuchokera kumwamba?
36
Tsono popeza kuti palibe amene angatsutse zimenezi, inu muyenera kukhala chete, osachita zinthu mopupuluma.
37
Inu mwabwera ndi anthu aŵa kuno, ngakhale iwo sadabe za m'nyumba ya mulungu wathu wamkazi, kapena kumchita chipongwe.
38
Ngati Demetrio ndi amisiri anzake ali ndi kanthu ndi munthu wina, mabwalo amilandu alipo, oweruza aliponso. Akakambirane milandu yao komweko.
39
Koma ngati mukufunanso kanthu kena, kameneko msonkhano waulamuliro wa anthu onse ndiwo ukatsirize.
40
Pakuti pali choopsa chakuti tingathe kuimbidwa mlandu wochita chipolowe chifukwa cha zimene zachitika lerozi. Palibe chifukwa chilichonse cha chipolowechi, ndipo tikasoŵa ponena akatifunsa.”
41
Atanena zimenezi, adauza anthu aja kuti azipita.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28