bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 16
Acts 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 17 →
1
Paulo adafika ku Deribe ndi ku Listara. Kumeneko kunali wophunzira wina, dzina lake Timoteo. Mai wake anali Myuda wosanduka wokhulupirira, koma bambo wake anali Mgriki.
2
Abale a ku Listara ndi a ku Ikonio ankamtama Timoteoyo.
3
Motero Paulo adafuna kuti iye amperekeze. Tsono adamuumbala chifukwa cha Ayuda amene anali kumeneko, pakuti onse ankadziŵa kuti bambo wa Timoteo ndi Mgriki.
4
Pamene ankadutsa m'mizinda, ankadziŵitsa anthu mfundo zimene atumwi ndi akulu a mpingo a ku Yerusalemu aja adaapanga, nkumaŵauza kuti azisunge.
5
Motero mipingo ya akhristu inkamangidwa pa chikhulupiriro cholima, ndipo oloŵamo ankachulukirachulukira tsiku ndi tsiku.
6
Paulo ndi anzake aja adapitirira dera la Frijiya ndi la Galatiya, pakuti Mzimu Woyera adaaŵaletsa kulalika mau a Mulungu ku Asiya.
7
Pamene adafika ku malire a Misiya, adayesa kuloŵa m'dera la Bitiniya, koma Mzimu wa Yesu sadaŵalole.
8
Motero adapitirira Misiya nakafika ku Troasi.
9
Usiku Paulo adaona m'masomphenya munthu wina wa ku Masedoniya ataima nkumampempha kuti, “Olokerani ku Masedoniya kuno, mudzatithandize.”
10
Iye ataona zimenezi, nthaŵi yomweyo tidakonza ulendo wopita ku Masedoniya, chifukwa tidaadziŵadi kuti Mulungu ndiye watiwongolera kuti tikaŵalalikire Uthenga Wabwino anthu akumeneko.
11
Kuchokera ku Troasi tidayenda m'chombo kulunjika ku chilumba cha Samotrase, ndipo m'maŵa mwake tidapitirira mpaka ku Neapoli.
12
Kuchokera kumeneko tidapita ku Filipi, mzinda wa m'chigawo choyamba cha m'dera lija la Masedoniya, ndiponso boma la Aroma. Tidakhala mu mzinda umenewo masiku angapo.
13
Pa tsiku la Sabata tidatuluka mumzindamo kupita kumtsinje kumene tinkaganiza kuti kuli malo opemphererako. Tsono tidakhala pansi nkumalankhula ndi akazi amene adaasonkhana kumeneko.
14
Pakati pao padaali mai wina, dzina lake Lidia. Anali wa ku mzinda wa Tiatira, ndipo ntchito yake inali yogulitsa nsalu zofiirira. Anali munthu wopembedza Mulungu, ndipo Ambuye adaatsekula mtima wake kuti azisamale zimene Paulo ankanena.
15
Iye ndi a m'banja mwake atabatizidwa, iyeyo adatipempha kuti, “Ngati mwandiwonadi kuti ndine munthu wokhulupirira Ambuye, dzaloŵeni m'nyumba mwanga, mudzakhale nafe.” Mwakuti adatikakamiza ndithu, ife nkukaloŵadi.
16
Nthaŵi ina pamene tinkapita ku malo opemphererako, tidakumana ndi kapolo wachitsikana amene adaagwidwa ndi mzimu woipa womunenetsa zakutsogolo. Ankapindulitsa mbuye wake kwambiri ndi kulosa kwakeko.
17
Iyeyo adayamba kutitsatira Paulo ndi ife, akufuula kuti, “Anthu aŵa ndi atumiki a Mulungu Wopambanazonse, akukulalikirani njira ya chipulumutso.”
18
Mtsikanayo adachita zimenezi masiku ambiri. Koma Paulo zimenezo zidamunyansa, choncho adatembenuka nauza mzimu woipa uja kuti, “Iwe, m'dzina la Yesu Khristu ndikukulamula kuti utuluke mwa munthuyu.” Ndipo nthaŵi yomweyo udatulukadi.
19
Ambuye ake a mtsikana uja ataona kuti sangapindule nayenso, adagwira Paulo ndi Silasi naŵakokera ku bwalo, kwa akulu.
20
Atafika nawo kwa akulu oweruza milandu, adaŵauza kuti, “Anthu aŵa ndi Ayuda, ndipo akuvutitsa mumzinda mwathu.
21
Akuphunzitsa miyambo imene ife sitiloledwa kuivomera kapena kuitsata, popeza kuti ndife Aroma.”
22
Anthu onse adagudukira Paulo ndi Silasi, ndipo akulu oweruza milandu aja adaŵang'ambira zovala zao, nalamula kuti aŵakwapule.
23
Ataŵakwapula kwambiri, adaŵaponya m'ndende, nalamula woyang'anira ndendeyo kuti aŵasunge bwino, angathaŵe.
24
Chifukwa cha mau ameneŵa, woyang'anira ndende uja adakaŵatsekera m'chipinda cha m'katikati mwa ndende, namangirira mapazi ao m'matangadza.
25
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera.
26
Mwadzidzidzi kudachita chivomezi champhamvu, kotero kuti maziko a ndende adagwedezeka. Nthaŵi yomweyo zitseko zonse zidatsekuka, maunyolo a mkaidi aliyense nkumasuka.
27
Woyang'anira ndende uja atadzuka, naona kuti zitseko zonse za ndende nzotsekuka, adaayesa kuti akaidi athaŵa. Pamenepo adasolola lupanga lake nati adziphe.
28
Koma Paulo adafuula kuti, “Iwe usadzipweteke! Tonse tilipo!”
29
Apo woyang'anira ndende uja adaitanitsa nyale, nathamangira m'kati, ndipo ali njenjenje ndi mantha, adadzigwetsa ku mapazi a Paulo ndi Silasi.
30
Tsono adaŵatulutsira kunja, naŵafunsa kuti, “Mabwana, Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumuke?”
31
Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.”
32
Kenaka adamlalikira mau a Ambuye iyeyo ndi onse a m'nyumba mwake.
33
Nthaŵi yomweyo, ngakhale unali usiku, iye adaŵatenga nakaŵatsuka mabala ao. Ndipo pompo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake adabatizidwa.
34
Pambuyo pake adapita nawo kunyumba kwake, naŵapatsa chakudya. Ndipo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake adasangalala kwambiri chifukwa cha kukhulupirira Mulungu.
35
M'maŵa kutacha, akulu oweruza milandu adatuma asilikali kukanena kuti, “Amasuleni anthu aja azipita.”
36
Woyang'anira ndende uja adafotokozera Paulo mauwo, adati, “Akulu oweruza milandu atumiza mau kuti tikumasuleni. Ndiye inu tulukani, muzipita ndi mtendere.”
37
Koma Paulo adauza asilikaliwo kuti, “Iwo aja adatikwapulira pa anthu, osaweruza mlandu wathu, chonsecho ndife nzika za ufumu wa Aroma, kenaka nkutiponya m'ndende. Ndiye tsopano akufuna kutitulutsa mobisa? Izo ndizo ai! Abwere iwowo adzatitulutse okha.”
38
Asilikali aja adapita kukaŵafotokozera akulu oweruza milandu aja mau ameneŵa. Pamene iwo aja adamva kuti ndi nzika za ufumu wa Aroma, adachita mantha.
39
Motero adabwera naŵapepesa, kenaka adaŵatulutsa naŵapempha kuti achokemo mumzindamo.
40
Paulo ndi Silasi atatuluka m'ndende muja adapita kunyumba kwa Lidia. Kumeneko adaonana ndi abale, ndipo ataŵalimbikitsa, adachoka.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28