bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 4
Acts 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 5 →
1
Petro ndi Yohane akulankhulabe ndi anthu aja, kudadza ansembe ena pamodzi ndi mkulu wa asilikali a ku Nyumba ya Mulungu, ndi Asaduki.
2
Iwoŵa anali okwiya chifukwa chakuti atumwi aŵiriwo ankaphunzitsa anthu ndi kulalika kuti, “Popeza kuti Yesu adauka kwa akufa, ndiye kuti akufa adzaukanso.”
3
Tsono adaŵagwira, ndipo poti kunali kutada kale, adaŵaika m'ndende kufikira m'maŵa.
4
Koma ambiri mwa anthu amene adamva mau aja a atumwi adakhulupirira. Chiŵerengero cha okhulupirirawo chidaakwanira ngati zikwi zisanu.
5
M'maŵa mwake atsogoleri a Ayuda, akulu ao, ndiponso aphunzitsi a Malamulo adasonkhana ku Yerusalemu.
6
Kunalinso Anasi mkulu wa ansembe onse, pamodzi ndi Kayafa, Yohane, Aleksandro ndi ena onse a kubanja kwa mkulu wa ansembe onse.
7
Tsono adaimiritsa Petro ndi Yohane pakati pao naŵafunsa kuti, “Kodi zija mudachitazi, mudazichita ndi mphamvu yanji, kaya mudazichita m'dzina la yani?”
8
Petro, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adaŵayankha kuti, “Inu atsogoleri ndi akuluakulu muli apa,
9
kodi mukutifunsa ife lero za ntchito yabwino imene idachitika pa munthu wopunduka uja, ndi kuchira kwake?
10
Mudziŵetu tsono inu nonse, ndi Aisraele ena onse, kuti munthuyu akuima wamoyo pamaso panu chifukwa cha mphamvu ya dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete. Amene uja inu mudaampachika pa mtanda, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa.
11
Za Yesuyo mau a Mulungu akuti, “ ‘Mwala umene inu amisiri omanga nyumba mudaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa.’
12
Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”
13
Abwalo aja adazizwa poona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane, ndiponso podziŵa kuti anali anthu wamba, osaphunzira kwambiri. Apo adazindikira kuti anali anzake a Yesu.
14
Tsono poonanso munthu wochiritsidwa uja ataimirira pafupi ndi Petro ndi Yohane, adasoŵa poŵatsutsira.
15
Choncho adaŵalamula kuti atuluke m'bwalo la milandu lija, kenaka abwalowo adayamba kukambirana.
16
Adati, “Kodi tiŵachite chiyani anthu ameneŵa? Pajatu anthu onse okhala m'Yerusalemu muno akudziŵa kuti iwoŵa adachitadi chizindikiro chozizwitsa, ndipo ife zimenezo sitingathe kukana.
17
Koma kuwopa kuti mbiriyi ingaŵande ponseponse, tiyeni tiwachenjeze moopseza kuti polankhula ndi munthu aliyense asatchulenso dzina la Yesu.”
18
Atatero adaŵaitana, naŵalamula kuti asatchule konse kapena kuphunzitsa za dzina la Yesu.
19
Koma Petro ndi Yohane adaŵayankha kuti, “Weruzani nokha, kodi pamaso pa Mulungu nkwabwino kumvera inuyo koposa kumvera Mulunguyo?
20
Ife ndiye sitingaleke kulankhula za zimene tidaziwona ndi kuzimva.”
21
Abwalowo adaŵachenjezanso moopseza koposa kale, naŵamasula. Sadapeze njira yoti nkuŵalangira, popeza kuti anthu onse ankatamanda Mulungu chifukwa cha zimene zidaachitikazo.
22
Ndipo munthu wochiritsidwa mododometsayo anali wa zaka zopitirira makumi anai.
23
Petro ndi Yohane atamasulidwa, adapita kwa anzao naŵasimbira zonse zimene akulu a ansembe ndi akulu ena a Ayuda adaaŵauza.
24
Pamene iwo adamva zimenezi, onse adayamba kupemphera ndi mtima umodzi. Adati, “Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lakumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi zonse zili m'menemo.
25
Mwa Mzimu Woyera mudalankhulitsa kholo lathu Davide, mtumiki wanu, pamene adati, “ ‘Chifukwa chiyani anthu akunja adakalipa, anthu a mitundu ina adaganiziranji zopandapake?
26
Mafumu a dziko lapansi adakonzekera, akulu a Boma adasonkhana pamodzi kulimbana ndi Chauta, ndiponso ndi wodzozedwa wake uja?’
27
“Zoonadi, Herode ndi Ponsio Pilato adasonkhana mumzinda muno pamodzi ndi anthu akunja, ndiponso ndi anthu a Israele, kuti alimbane ndi Yesu, Mtumiki wanu wopatulika amene mudamdzoza.
28
Motero iwo adachitadi zonse zija zimene Inu mudaakonzeratu kale mwa mphamvu zanu ndi nzeru zanu kuti zichitike.
29
Ndiye tsono Ambuye, onani zimene akutiwopsezazi, ndipo mutithandize atumiki anufe, kuti tilankhule mau anu molimba mtima ndithu.
30
Tambalitsani dzanja lanu kuti anthu achire, ndipo pachitike zizindikiro ndi zozizwitsa m'dzina la Mtumiki wanu wopatulika.”
31
Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
32
Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “Zimene ndiri nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse.
33
Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankaŵakomera mtima kwambiri.
34
Panalibe munthu wosoŵa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi.
35
Ndipo ndalamazo ankagaŵira munthu aliyense malinga ndi kusoŵa kwake.
36
Panali munthu wina dzina lake Yosefe, wa fuko la Levi, mbadwa ya ku Kipro, amene atumwi adaamutcha Barnabasi, ndiye kuti Wolimbitsa mtima.
37
Nayenso adagulitsa munda wake, nabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28