bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 18
Acts 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 19 →
1
Pambuyo pake Paulo adachoka ku Atene napita ku Korinto.
2
Kumeneko adapezako Myuda wina, dzino lake Akwila, mbadwa ya ku Ponto. Iye anali atangofika chatsopano kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio, Mfumu ya ku Roma, adaalamula kuti Ayuda onse achoke ku Roma. Tsono Paulo adapita kukaŵaona.
3
Ndiye popeza kuti iwo anali amisiri a ntchito imodzimodzi ngati yake, yosoka mahema, iyeyo adakhala nawo namagwirira limodzi ntchito.
4
Pa tsiku la Sabata lililonse iye ankakambirana ndi anthu ku nyumba yamapemphero ya Ayuda, namayesetsa kukopa Ayuda ndi Agriki omwe.
5
Silasi ndi Timoteo atafika kuchokera ku Masedoniya, Paulo tsopano ankangogwira ntchito yolalikira, ndi kuŵauza Ayuda monenetsa kuti Yesu ndiye anali Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
6
Koma pakuti iwo adaatsutsana naye ndi kumchita chipongwe, Paulo adalekana nawo pakukutumula zovala zake, naŵauza kuti, “Mwadziphetsa ndi mtima wanu. Tsono izo nzanu, ine ndilibe chifukwa. Kuyambira tsopano ndipita kwa akunja.”
7
Motero adachoka kumeneko napita ku nyumba ya munthu wina, dzina lake Tito Yusto. Iyeyu anali munthu wopembedza Mulungu, ndipo nyumba yake idaayandikana ndi nyumba yamapemphero.
8
Krispo, mkulu wa nyumba yamapempheroyo pamodzi ndi onse a pa banja lake adakhulupirira Ambuye. Ndipo anthu ambiri a ku Korinto atamva mau a Paulo, adakhulupirira nabatizidwa.
9
Tsiku lina usiku Ambuye adaonekera Paulo m'masomphenya namuuza kuti, “Usaope, koma upitirire kulalika, osakhala chete ai,
10
pakuti Ine ndili nawe pamodzi. Palibe munthu adzakukhudza kuti akuchite choipa, ndipo ndili nawo anthu ambiri mumzinda muno.”
11
Choncho Paulo adakhala komweko chaka chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi, akuŵaphunzitsa mau a Mulungu.
12
Pamene Galio anali bwanamkubwa wa ku Akaiya, Ayuda onse pamodzi adaukira Paulo, namtengera ku bwalo la milandu.
13
Iwo adati, “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwa njira zotsutsana ndi Malamulo athu.”
14
Koma pamene Paulo adati azilankhula, Galio adauza Ayuda kuti, “Ukadakhala mlandu wakuti munthu wachimwira lamulo, kapena wakuti walakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino, Ayuda inu.
15
Koma popeza kuti ndi nkhani yokhudza mau, ndi maina, ndiponso Malamulo anu, mudziwonere nokha. Kuti ndiweruze zimenezi, ine toto.”
16
Atatero adaŵapirikitsa kubwaloko.
17
Pamenepo onsewo adagwira Sostene, mkulu wa nyumba yamapemphero ya Ayuda, nammenyera m'bwalo momwemo. Koma Galio sadasamaleko zimenezi.
18
Paulo adakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Pambuyo pake adalaŵirana ndi abale, naloŵa m'chombo kupita ku Siriya pamodzi ndi Prisila ndi Akwila. Asanaloŵe m'chombomo, Paulo adameta tsitsi lake ku Kenkrea, chifukwa anali atachita lumbiro kwa Mulungu.
19
Iwo adakafika ku Efeso, ndipo kumeneko Paulo adasiyako Akwila ndi Prisila. Koma iye yekha adaloŵa m'nyumba yamapemphero nakambirana ndi Ayuda.
20
Pamene ameneŵa adampempha kuti akhale nawo nthaŵi yaitali, iye sadavomere.
21
Adaŵatsazika naŵauza kuti, “Mulungu akalola ndidzabweranso.” Atatero adachoka ku Efeso m'chombo.
22
Pamene adafika ku Kesareya, adapita ku Yerusalemu kukacheza pang'ono ndi mpingo. Kuchokera kumeneko adapita ku Antiokeya.
23
Atakhala kumeneko kanthaŵi ndithu, adachokako nakayendera dziko la Galatiya ndi la Frijiya, akulimbikitsa ophunzira onse.
24
Myuda wina, dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Aleksandriya, adabwera ku Efeso. Anali munthu wodziŵa kulankhula ndi wodziŵa Malembo kwambiri.
25
Iyeyu adaaphunzitsidwa Njira ya Ambuye, ndipo ndi changu chachikulu ankalankhula ndi kuphunzitsa za Yesu molongosoka, chonsecho ankangodziŵa za ubatizo wa Yohane wokha.
26
Tsono adayamba kulankhula molimba mtima m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Koma pamene Prisila ndi Akwila anamumva, adamtenga namufotokezera Njira ya Mulungu molongosoka koposa.
27
Pamene Apolo adafuna kuwolokera ku Akaiya, abale adamlimbikitsa, nalembera ophunzira akumeneko kalata kuti amlandire bwino. Tsono atafikako, adaŵathandiza kwambiri amene anali atakhulupirira chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu.
28
Pakuti iye adaatsutsa Ayuda mwamphamvu pamaso pa anthu, natsimikiza ndi Malembo kuti Yesu ndiyedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28