bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 8
Acts 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 9 →
1
Saulo uja ankavomerezana nawo za kupha kumeneku. Tsiku limenelo mpingo wa ku Yerusalemu udayamba kuzunzidwa kwambiri, ndipo onse, kupatula atumwi okha, adabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya.
2
Anthu ena okonda Mulungu adakaika maliro a Stefano namlira kwambiri.
3
Koma Saulo uja ankapasula Mpingo. Ankaloŵa m'nyumba za anthu, namagwira amuna ndi akazi omwe, nkumaŵaponya m'ndende.
4
Okhulupirira amene adabalalika aja adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino.
5
Filipo adatsikira ku mzinda wa ku Samariya, namalalikira anthu akumeneko za Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
6
Makamu a anthu ndi mtima umodzi ankatchera makutu ku zimene Filipo ankanena. Onse ankamvetsera mau ake nkumaona zozizwitsa zimene iye ankachita.
7
Pakuti mizimu yonyansa inkatuluka mwa anthu ambiri amene anali atagwidwa nayo, nimafuula kwambiri. Ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo kapena opunduka, ankachira.
8
Choncho munali chimwemwe chachikulu mumzinda muja.
9
Koma mumzindamo munali munthu wina, dzina lake Simoni amene kale ankachita matsenga, namadodometsa anthu onse a ku Samariyako. Iyeyu ankadzimveketsa kuti ndi munthu wamkulu.
10
Anthu onse, aang'ono ndi aakulu omwe, ankamumvera namamtsata nkumanena kuti, “Munthu ameneyu ndiye mphamvu ya Mulungu ija amati, Mphamvu yaikulu.”
11
Ankamutsata chifukwa pa nthaŵi yaitali ankaŵadodometsa ndi matsenga akewo.
12
Koma pamene Filipo ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, ndiponso za dzina la Yesu Khristu, anthu adakhulupirira, ndipo adabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.
13
Simoni uja nayenso adakhulupirira, ndipo atabatizidwa, ankakhalira limodzi ndi Filipo. Adazizwa pakuwona zizindikiro ndi zozizwitsa zimene zinkachitika.
14
Pamene atumwi okhala ku Yerusalemu adamva kuti anthu a ku Samariya alandira mau a Mulungu, adatumako Petro ndi Yohane.
15
Iwowo atafika, adayamba kupempherera okhulupirira aja kuti alandire Mzimu Woyera.
16
Nthaŵiyo nkuti Mzimu Woyera asanafike pa wina aliyense mwa iwo. Onsewo anali atangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.
17
Tsono Petro ndi Yohane adaŵasanjika manja, ndipo adalandira Mzimu Woyera.
18
Simoni uja ataona kuti Mzimu Woyera waperekedwa kwa iwo atumwi aja ataŵasanjika manja, adafuna kuŵapatsa ndalama atumwiwo.
19
Adati, “Bwanji mutandipatsako inenso mphamvu imeneyi, kuti aliyense amene ndikamsanjike manja, akalandire Mzimu Woyera.”
20
Petro adamuyankha kuti, “Ndalama zakozo ukatayike nazo pamodzi. Iwe ukuganiza kuti ungathe kupata mphatso ya Mulungu pakupereka ndalama kodi?
21
Ulibe gawo kapena malo pa ntchito imeneyi, pakuti mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu.
22
Nchifukwa chake tembenuka mtima, uleke choipa chakochi. Pempha Ambuye kuti mwina mwake nkukukhululukira maganizo a mumtima mwakoŵa.
23
Pakuti ndakuwona kuti ndiwe wodzaza ndi ndulu yoŵaŵa, ndiponso ndiwe womangidwa ndi maunyolo a zoipa.”
24
Apo Simoni uja adati, “Mundipempherere inuyo kwa Ambuye kuti zimene mwanenazi zisandigwere.”
25
Petro ndi Yohane atatha kupereka umboni wao ndi kulalika mau a Ambuye, adabwerera ku Yerusalemu. Ankapita nalalika Uthenga Wabwino m'midzi yambiri ya Asamariya.
26
Mngelo wa Ambuye adauza Filipo kuti, “Nyamuka, pita chakumwera, kutsata mseu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu; mseu wodzera m'chipululu uja.”
27
Filipo adanyamukadi napita. Ndipo munthu wina wa ku Etiopiya adaabwera ku Yerusalemu kudzapembedza. Iyeyu anali nduna yaikulu ya m'banja la mfumukazi Kandake wa ku Etiopiya, ndiponso woyang'anira chuma chake chonse.
28
Nthaŵi imeneyo ankabwerera kwao. Anali pa galeta akuŵerenga buku la mneneri Yesaya.
29
Tsono Mzimu Woyera adauza Filipo kuti, “Pita, kayandikane nalo galetalo.”
30
Filipo adathamangira nduna ija, ndipo adaimva ikuŵerenga buku la mneneri Yesaya. Tsono adaifunsa kuti, “Bwana, kodi mukumvetsa zimene mukuŵerengazi?”
31
Iye adati, “Ha, ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Motero adaitana Filipo kuti adzakwere ndi kukhala naye pagaletapo.
32
Mau a m'Malembo amene ankaŵerengawo ndi aŵa: “Iye anali ngati nkhosa yoitsogoza pokaipha, ngati mwana wankhosa wongokhala duu pomumeta. Sadalankhulepo kanthu.
33
Adampeputsa, pa mlandu wake sadamchitire chilungamo. Palibe amene adzatha kusimba za zidzukulu zake, pakuti moyo wake wachotsedwa pa dziko lapansi.”
34
Pamenepo nduna ija idati, “Pepani, tandiwuzani, kodi zimenezi mneneriyo akunena za yani, za iye mwini, kapena za wina?”
35
Apo Filipo adayamba kumlalikira Uthenga Wabwino wa Yesu kuyambira pa Malembo ameneŵa.
36
Ndipo pamene ankapita mumseumo, adafika pena pamene panali madzi. Nduna ija idati, “Madzi si aŵa. Monga pali choletsa kuti ndisabatizidwe?” [
37
Filipo adayankha kuti, “Mungathe kubatizidwa ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse.” Iye adati, “Ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.”]
38
Pamenepo ndunayo idalamula kuti galetalo liime. Aŵiri onsewo, Filipo ndi nduna ija, adatsikira ku madzi, Filipo nkumubatiza.
39
Pamene adatuluka m'madzimo, Mzimu wa Ambuye adamchotsapo Filipo uja. Ndipo nduna ija siidamuwonenso, koma idapitirira ulendo wake ikusangalala.
40
Tsono Filipo adapezeka kuti ali ku Azoto. Adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino m'mizinda yonse, mpaka adakafika ku Kesareya.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28