bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 5
Acts 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 6 →
1
Munthu winanso, dzina lake Ananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, adagulitsa munda wao.
2
Mopangana ndi mkazi wake, adapatulapo ndalama zina za mundawo, nakapereka zotsala kwa atumwi.
3
Koma Petro adamufunsa kuti, “Iwe Ananiya, chifukwa chiyani walola mtima wako kugwidwa ndi Satana mpaka kumanamiza Mzimu Woyera pakupatula ndalama zina za munda wako?
4
Usanaugulitse, sunali wako kodi? Ndipo utaugulitsa, suja ndalama zake zinali m'manja mwako? Nanga udalola bwanji zoterezi mumtima mwako? Pamenepatu sudanamize anthu, koma wanamiza Mulungu.”
5
Pamene Ananiya adamva mau ameneŵa, adagwa pansi, naafa pomwepo. Ndipo anthu onse amene adamva zimenezi adachita mantha aakulu.
6
Tsono achinyamata adabwera namkulunga m'nsalu. Adamnyamula nakamuika m'manda.
7
Patapita ngati maora atatu, mkazi wake adaloŵa, osadziŵa zimene zachitika.
8
Petro adamufunsa kuti, “Tandiwuzani, kodi pogulitsa munda wanu, mtengo wake unali ndalama izi?” Maiyo adati, “Inde, mtengo wake unali womwewo.”
9
Tsono Petro adamufunsa kuti, “Bwanji mudapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Ndipotu anthu amene akaika mwamuna wanu ndi aŵa ali pakhomoŵa, akunyamulani inunso.”
10
Pomwepo adagwa pansi ku mapazi a Petro, naafa. Pamene achinyamata aja adaloŵa, adampeza atafa kale. Adamnyamula nakamuika pafupi ndi mwamuna wake.
11
Ndipo mpingo wonse ndi anthu onse amene adamva zimenezi, adagwidwa ndi mantha aakulu.
12
Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Khonde la Solomoni.
13
Mwa anthu enawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaalimba mtima kuti azisonkhana nawo, komabe anthu onse ankaŵatama.
14
Ndipo anthu okhulupirira Ambuye ankachulukirachulukira, mwakuti linali ndithu gulu lalikulu la amuna ndi akazi omwe.
15
Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m'miseu yamumzinda, nkumaŵagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiŵafike.
16
Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yoŵaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa.
17
Pamenepo mkulu wa ansembe onse pamodzi ndi anzake aja, ndiye kuti a m'chipani cha Asaduki, onsewo adadukidwa nazo. Tsono adagamula zochitapo kanthu.
18
Adagwira atumwi aja, naŵatsekera m'ndende ya Boma.
19
Koma usiku mngelo wa Ambuye adatsekula zitseko za ndendeyo naŵatulutsa. Adaŵauza kuti,
20
“Pitani m'Nyumba ya Mulungu muzikauza anthu mau onse okhudza za moyo watsopanowu.”
21
Atumwi aja adamveradi zimenezi, adakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu m'mamaŵa, nayamba kuphunzitsa. Pamene mkulu wa ansembe onse adafika pamodzi ndi anzake aja, adaitanitsa msonkhano wa Bungwe Lalikulu, ndiye kuti Bwalo lonse la akuluakulu a Aisraele. Tsono adatuma anthu kuti apite ku ndende akaŵatenge atumwi aja.
22
Koma pamene anthuwo adafika kundendeko, sadaŵapezemo. Adabwerako nadzaŵafotokozera.
23
Adati, “Takapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndipo alonda ali chilili pa makomo, koma titatsekula zitseko, sitidapezemo munthu.”
24
Pamene mkulu wa asilikali a ku Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe adamva mau ameneŵa, adatha nawo nzeru, osadziŵa kwachitika zotani.
25
Koma munthu wina adadzaŵauza kuti, “Anthu amene mudaŵatsekera m'ndende aja, ali m'Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.”
26
Pamenepo mkulu wa asilikali uja pamodzi ndi asilikaliwo adapita nkukaŵatenga atumwiwo. Sadaŵatenge mwankhondo ai, chifukwa ankaopa kuti anthu angaŵaponye miyala.
27
Atafika nawo, adaŵakhazika pamaso pa Bungwe Lalikulu lija, ndipo mkulu wa ansembe onse adayamba kuŵafunsa mafunso.
28
Adati, “Paja tidakuletsani mwamphamvu kuti musaphunzitse konse m'dzina la Yesu, koma inu mwafalitsa zophunzitsa zanuzo m'Yerusalemu monse, ndipo mukufuna kusenzetsa ife imfa ya munthu ameneyu.”
29
Koma Petro ndi atumwi enawo adati, “Tiyenera kumvera Mulungu koposa kumvera anthu.
30
Mulungu wa makolo athu adaukitsa Yesu kwa akufa, Iye amene inu mudaamupha pakumpachika pa mtanda.
31
Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi. Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao akhululukidwe.
32
Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera Iye.”
33
Pamene abwalo aja adamva zimenezi, adakwiya kwambiri nafuna kuŵapha.
34
Koma wina mwa iwo, Mfarisi dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa Malamulo, amene anthu onse ankamlemekeza, adaimirira. Adalamula kuti anthu aja abaapita panja.
35
Tsono adauza abwalowo kuti, “Inu Aisraele, chenjerani ndi zimene mukufuna kuŵachita anthuŵa.
36
Pajatu si kale pamene munthu wina dzina lake Teudasi adaabwera nkuyesa kudzimveketsa, ndipo anthu ngati mazana anai adamtsata. Iye uja adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana natheratu.
37
Pambuyo pake, pa nthaŵi ya kalembera, padabweranso wina dzina lake Yudasi, wa ku Galileya, nakopa anthu ambiri kuti amtsate. Iyenso adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana.
38
Nchifukwa chake pa nkhani imeneyi ndikukuuzani kuti, muŵaleke anthuŵa, ndipo muŵalole azipita. Ngati zimene iwo akuganiza ndiponso zimene akuchitazi nzochokera kwa anthu, zidzakanika zokha.
39
Koma ngati nzochokera kwa Mulungu, inu simungathe kuŵaletsa ai. Mwina mungapezeke kuti mukulimbana ndi Mulungu.”
40
Abwalowo adavomerezana naye, naŵaitana atumwi aja. Adaŵakwapula, naŵaletsa kuti asalankhulenso m'dzina la Yesu, kenaka adaŵalola kuti apite.
41
Iwo adachoka kubwaloko ali okondwa kuti Mulungu waŵaŵerengera ngati oyenera kunyozeka chifukwa cha dzina la Yesu.
42
Tsono tsiku ndi tsiku ankaphunzitsabe ndi kulalika m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba za anthu, Uthenga Wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28