bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 9
Acts 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 10 →
1
Saulo uja ankaopsezabe ophunzira a Ambuye, nkumafuna kuŵapha. Adapita kwa mkulu wa ansembe onse
2
kukampempha makalata opita nawo ku nyumba zamapemphero za ku Damasiko. Ankafuna kuti ngati akapezeko ena otsata Njira ya Ambuye, kaya ndi amuna kaya ndi akazi, akaŵamange nkubwera nawo ku Yerusalemu.
3
Ali paulendo wakewo, adayandikira mzinda wa Damasiko uja. Mwadzidzidzi kuŵala kochokera kumwamba kudamzinga.
4
Adagwa pansi namva mau akuti, “Saulo, Saulo, ukundizunziranji Ine?”
5
Iye adafunsa kuti, “Ndinu yani, Ambuye?” Iwo adati, “Ndine Yesu amene ukundizunza.
6
Koma dzuka, kaloŵe mumzindamo, ndipo akakuuza chochita.”
7
Anthu amene anali naye pa ulendowo adaima, atangoti chete. Mauwo ankaŵamva, koma osaona munthu.
8
Saulo adadzuka, koma pamene maso ake adaphenyuka, sadathe kupenya kanthu. Tsono anzake aja adamgwira pa dzanja naloŵa naye m'Damasiko.
9
Ndipo adakhala masiku atatu osatha kupenya ndiponso osadya kapena kumwa kanthu.
10
Tsono ku Damasikoko kunali wophunzira wina, dzina lake Ananiya. Iyeyu adaaona m'masomphenya Ambuye akumuitana kuti, “Ananiya!” Iye adati, “Ee, Ambuye.”
11
Apo Ambuye adamuuza kuti, “Nyamuka, upite ku mseu wa mumzindamu umene amati, ‘Njira Yolunjika.’ Ndipo ku nyumba ya Yudasi ukafune munthu wina wa ku Tariso, dzina lake Saulo. Panopa akupemphera,
12
ndipo waona m'masomphenya munthu wina, dzina lake Ananiya, akuloŵa ndi kumsanjika manja kuti apenyenso.”
13
Atamva zimenezo Ananiya adati, “Ambuye, anthu ambiri andiwuza za munthu ameneyu, kuti adaŵachita zoipa zambiri anthu anu ku Yerusalemu.
14
Ndipo wabwera kuno ndi ulamuliro wa akulu a ansembe kuti adzamange onse otama dzina lanu mopemba.”
15
Koma Ambuye adamuuza kuti, “Pita, pakuti iyeyu ndi mtumiki wanga amene ndidamsankha kuti akalalikire dzina langa anthu a mitundu ina, mafumu, ndiponso Aisraele.
16
Ine ndidzamuwonetsa zoŵaŵa zonse zimene adzayenera kumva chifukwa cha Ine.”
17
Pamenepo Ananiya adanyamuka nakaloŵa m'nyumbamo. Adamsanjika manja Sauloyo nati, “Mbale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene adakuwonekera pa njira imene wadzera ija, andituma. Akufuna kuti upenyenso, ndipo udzazidwe ndi Mzimu Woyera.”
18
Pompo m'maso mwake mudachoka zinthu zonga mamba a nsomba, ndipo adayambanso kupenya. Adaimirira nabatizidwa,
19
ndipo atadya chakudya, adapezanso mphamvu. Saulo adakhala masiku angapo limodzi ndi ophunzira a ku Damasiko.
20
Ndipo posakhalitsa adayamba kulalika m'nyumba zamapemphero za Ayuda kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
21
Anthu onse amene ankamva mau akewo ankadabwa, namafunsana kuti, “Kodi ameneyu si yemwe uja amene ku Yerusalemu ankapha anthu otama dzinali mopemba? Kodi siwabwera kuno kuti aŵamange otereŵa ndi kukaŵapereka kwa akulu a ansembe?”
22
Tsono mphamvu za Saulo zinkakulirakulira, ndipo adathetsa nzeru Ayuda okhala ku Damasiko pakuŵatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
23
Patapita masiku ambiri, Ayuda adapangana kuti aphe Saulo,
24
koma anthu ena adamuuzako za chiwembucho. Anthu achiwembuwo ankadikira pa zipata za linga la mzinda usana ndi usiku kuti amuphe.
25
Koma ophunzira ake adamtenga usiku, namtsitsira kunja kwa lingalo m'dengu.
26
Saulo atafika ku Yerusalemu, adayesa kuloŵa m'gulu la ophunzira aja. Koma onse adachita naye mantha, osakhulupirira kuti nayenso ndi wophunzira.
27
Pamenepo munthu wina, dzina lake Barnabasi, adamtenga napita naye kwa atumwi. Iye adaŵafotokozera za m'mene Saulo adaaonera Ambuye panjira paja, ndipo kuti Ambuye adaalankhula naye. Adaŵasimbiranso za m'mene Saulo ku Damasiko ankalankhulira molimba mtima m'dzina la Yesu.
28
Tsono Saulo adakhala nawo, nayendera Yerusalemu yense akulalika molimba mtima m'dzina la Ambuye.
29
Ankalankhulanso ndi kumatsutsana ndi Ayuda olankhula Chigriki, koma iwowo ankafunafuna kumupha.
30
Pamene abale adamva zimenezi, adapita naye ku Kesareya namtumiza ku Tariso.
31
Pamenepo Mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unali pa mtendere. Udakhazikika, ndipo anthu ochuluka adaloŵamo chifukwa anthu ake ankayenda moopa Ambuye, ndipo Mzimu Woyera ankaŵalimbikitsa.
32
Pamene Petro ankayendera anthu a Mulungu uku ndi uku, adakafika kwa amene ankakhala ku Lida.
33
Kumeneko adapezako munthu wina, dzina lake Eneya, amene anali atagona pa mphasa zaka zisanu ndi zitatu, ali wofa ziwalo.
34
Tsono Petro adamuuza kuti, “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa. Dzuka, yalula mphasa yako.” Pomwepo iye adadzukadi.
35
Anthu onse okhala ku Lida ndi ku Saroni atamuwona, adatembenukira kwa Ambuye.
36
Ku Yopa kunali wophunzira wina wamkazi, dzina lake Tabita (pa Chigriki amati Dorika). Iyeyu ankachita ntchito zabwino zambiri ndi kumathandiza osauka.
37
Masiku amenewo maiyo adaadwala, nkumwalira. Anthu adatsuka maliro, nakagoneka mtembo m'chipinda cham'mwamba.
38
Ku Yopa kunali kufupi ndi ku Lida, choncho pamene ophunzira adamva kuti Petro ali ku Lida, adatuma anthu aŵiri kuti akamuuze kuti, “Chonde, mubwere kwathu kuno msanga.”
39
Tsono Petro adanyamuka napita nawo. Pamene iye adafika, adamperekeza ku chipinda cham'mwamba chija. Akazi onse amasiye adangoti kwete m'mbali mwakemu, akungolira, nkumamuwonetsa malaya ndi zovala zina zimene Dorika ankasoka ali nawo pamodzi.
40
Petro adaŵapempha onse kuti atuluke, ndipo adagwada pansi nkumapemphera. Kenaka adatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka!” Apo Tabita adatsekula maso, ndipo pamene adaona Petro, adakhala tsonga.
41
Petro adamgwira dzanja namuimiritsa. Ndipo adaitana anthu a Mulungu ndi azimai amasiye aja, nampereka kwa iwo ali wamoyo.
42
Anthu onse a ku Yopa adamva zimenezi, ndipo ambiri adakhulupirira Ambuye.
43
Tsono Petro adakhala ku Yopa masiku ambiri kwa munthu wina, dzina lake Simoni, mmisiri wa zikopa.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28