bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 12
Acts 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 13 →
1
Pafupi ngati nthaŵi imeneyo mfumu Herode adagwira ena a mu Mpingo kuti aŵazunze.
2
Adalamula kuti Yakobe, mbale wake wa Yohane, aphedwe ndi lupanga.
3
Ndipo ataona kuti zimenezi zidakondweretsa Ayuda, adapitiriza ndithu nkugwiranso Petro. Zimenezi zidachitika pa masiku a Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa.
4
Atamgwira, adamtsekera m'ndende, nampereka kwa magulu anai a asilikali kuti azimlonda, gulu lililonse asilikali anai. Tsono Herode ankafuna kuzenga mlandu wake pamaso pa anthu onse, chikondwerero cha Paska chitapita.
5
Motero Petro ankasungidwa m'ndende. Koma Mpingo unkamupempherera kwa Mulungu kosalekeza.
6
Usiku woti m'maŵa mwake Herode azenga mlandu wake, Petro adaagona pakati pa asilikali aŵiri. Anali womangidwa ndi maunyolo aŵiri, ndipo pakhomo pa ndende panali alonda ena.
7
Mwadzidzidzi kudafika mngelo wa Ambuye ndipo kuŵala koti mbee kudaunika m'chipindamo. Mngeloyo adagunduza Petro m'nthitimu kuti amdzutse, ndipo adati, “Dzuka msanga!” Pompo maunyolo aja adakolopoka m'manja mwake.
8
Kenaka mngelo uja adamuuza kuti, “Vala lamba wako ndi nsapato zako.” Petro atachita zimenezi mngelo uja adamuuzanso kuti, “Fundira mwinjiro wako, unditsate.”
9
Apo Petro adatuluka namtsata, osazindikira kuti zimene mngelo ankachitazo nzoona. Ankangoyesa kuti akuwona zinthu m'masomphenya chabe.
10
Onsewo adapitirira gulu loyamba la asilikali aja, kenaka lachiŵiri, mpaka kukafika pa chitseko chachitsulo cha pa chipata choloŵera mu mzinda. Chitsekocho chidangodzitsekukira chokha, iwowo nkutuluka. Adayenda ndithu mu mseu wina wamumzindamo. Atafika polekezera pake mngelo uja adamchokera.
11
Pamenepo Petro adadzidzimuka nati, “Tsopano ndikudziŵadi kuti Ambuye anatuma mngelo wao ndipo andipulumutsa kwa Herode, ndi ku zoipa zonse zimene Ayuda ankayembekeza kuti zidzandichitikira.”
12
Atazindikira zimenezi, adapita kunyumba kwa Maria, amai ake a Yohane wotchedwanso Marko. Anthu ambiri anali atasonkhana kumeneko akupemphera.
13
Pamene Petro adagogoda pa chitseko chapakhomo, mtsikana wina, dzina lake Roda, adabwera kuti amtsekulire.
14
Atazindikira liwu lake kuti ndi la Petro, adakondwa kwambiri, kotero kuti sadatsekule chitsekocho, koma adathamangiranso m'kati nakawuza ena aja kuti, “Petro ali pakhomopa!”
15
Anthuwo adati, “Wapenga iwe!” Koma iye adalimbikira kuti nzoonadi. Apo iwo adati, “Ndi mngelo wake ameneyo.”
16
Koma Petro ankangogogodabe. Pamene adamtsekulira nkuwona kuti ndiyedi, adangoti kakasi.
17
Petro adakweza dzanja kuti iwo akhale chete, naŵafotokozera m'mene Ambuye adaamtulutsira m'ndende muja. Ndipo adati, “Mumuuze Yakobe ndi abale ena aja zimenezi.” Pamenepo iye adatuluka napita kwina.
18
Kutacha, asilikali aja adasokonezeka kwabasi nati, “Petro wapita kuti?”
19
Herode adamufunafuna, koma osampeza. Adaŵazenga mlandu alonda aja, nalamula kuti aphedwe. Pambuyo pake Herode adachoka ku Yudeya kupita ku Kesareya, nakakhala kumeneko.
20
Herode adaaŵakwiyira anthu a ku Tiro ndi a ku Sidoni. Tsono anthuwo adadza pamodzi kwa iye. Adaayamba akopa Blasito, kapitao wa ku nyumba ya mfumu kenaka nkukapempha mtendere, chifukwa chakudya cha m'dziko laolo chinkachokera m'dziko la mfumuyo.
21
Adapangana tsiku, ndipo pa tsikulo Herode adavala zovala zake zachifumu nkukhala pa mpando wake wachifumu, nayamba kuŵalankhula anthu aja.
22
Anthuwo adanena mokweza mau kuti, “Ameneŵa ndi mau a mulungu, osati a munthu ai.”
23
Pompo mngelo wa Ambuye, adamkantha Herodeyo chifukwa sadapereke ulemu kwa Mulungu. Mphutsi zidamudya ndipo adafa.
24
Koma mau a Mulungu adanka nafalikirafalikira.
25
Tsono Barnabasi ndi Saulo atakwaniritsa zimene adaaŵatumira ku Yerusalemu, adabwerako. Adatengako Yohane wotchedwa Marko uja.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28