bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 3
Acts 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 4 →
1
Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu pa 3 koloko madzulo, nthaŵi ya mapemphero.
2
Anthu ena adaanyamula munthu wina wopunduka miyendo chibadwire. Masiku onse ankamuika pa khomo la Nyumba ya Mulungu lotchedwa “Khomo Lokongola,” kuti iye azipempha kwa anthu oloŵa m'Nyumbamo.
3
Pamene iye adaona Petro ndi Yohane akuloŵa m'Nyumba ya Mulungu, adaŵapempha kuti ampatseko kanthu.
4
Iwo adampenyetsetsa, ndipo Petro adamuuza kuti, “Tatiyang'ana”
5
Iye nkuŵayang'anadi namaganiza kuti alandira kanthu kwa iwo.
6
Koma Petro adamuuza kuti, “Ndalama ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: m'dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete, yenda!”
7
Atatero adamgwira dzanja lamanja, namuimiritsa. Pompo mapazi ake ndi akakolo ake adalimba.
8
Adalumpha, naimirira, nayamba kuyenda, ndipo adaloŵa nao m'Nyumba ya Mulungu akuyenda ndi kulumpha ndi kutamanda Mulungu.
9
Anthu onse adamuwona akuyenda ndi kutamanda Mulungu.
10
Adamzindikira kuti ndi yemwe uja amene ankakhala pa Khomo Lokongola la Nyumba ya Mulungu. Ndipo adazizwa ndithu ndi kudabwa ndi zimene zidamchitikira.
11
Munthu uja adaakangamira Petro ndi Yohane, ndipo anthu onse adadabwa, naŵathamangira ku Khonde lotchedwa Khonde la Solomoni.
12
Pamene Petro adaona zimenezi, adalankhula nawo anthuwo, adati, “Inu Aisraele, bwanji mukuzizwa ndi zimenezi? Bwanji mukutiyang'ana ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu zathuzathu? Kodi mukuyesa kuti nchifukwa choti ndife opembedza Mulungu kopambana?
13
Iyai, koma Mulungu wa makolo athu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, adapereka ulemerero kwa Yesu, Mtumiki wake. Inu mudampereka kwa adani ake ndi kumkana pamaso pa Pilato, pamene Pilatoyo adaatsimikiza kuti ammasula.
14
Yesu anali woyera mtima ndi wolungama, koma inu mudamkana, ndipo m'malo mwake mudapempha kuti akumasulireni chigaŵenga.
15
Mudapha Wopatsa moyo, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi.
16
Munthuyu, amene mukumuwona ndipo mukumdziŵa, wakhulupirira dzina la Yesu. Chikhulupirirocho chimene ali nacho mwa Yesu, ndicho chalimbitsa miyendo yake, chamchiritsa kwenikweni, monga inu nonse mukuwoneramu.
17
“Ndiponso tsopano abale anga, ndikudziŵa kuti inu ndi akuluakulu anu mudachita zimenezi mosadziŵa.
18
Koma Mulungu adaaneneratu mwa aneneri onse kuti Wodzozedwa wake wolonjezedwa uja adzamva zoŵaŵa, ndipo zidachitikadi momwemo.
19
Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo,
20
ndipo adzakutumizirani Yesu uja amene adamusankhuliratu kuti akhale Mpulumutsi wanu.
21
Iyeyo anayenera kukhala Kumwamba mpaka nthaŵi yakukonza zonse kwatsopano, monga Mulungu adanenera kuyambira kalekale mwa aneneri ake oyera mtima.
22
Paja Mose adati, ‘Ambuye Mulungu adzasankhula mmodzi pakati pa abale anu, kuti akhale Mneneri wanu monga ine. Mudzamvere zonse zimene Iye adzakuuzeni.
23
Aliyense amene sadzamvera Mneneriyo, amchotseretu mwa Aisraele ndi kumuwononga.’
24
Ndipo aneneri onse amene adalankhula, kuyambira Samuele, mpaka onse amene adadza pambuyo pake, ankalalika za masiku omwe ano.
25
Zimene Mulungu adalonjeza kudzera mwa aneneri nzokhudza inuyo ana ao. Momwemonso chipangano chimene adachita ndi makolo anu chikukhudza inu ana ake. Paja adauza Abrahamu kuti, ‘Mwa chidzukulu chako china ndidzadalitsa mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi.’
26
Choncho Mulungu atasankhula Mtumiki wake adayamba kumtuma kwa inu, kuti akudalitseni pakuthandiza aliyense mwa inu kusiya njira zake zoipa.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28