bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 14
Acts 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 15 →
1
Zimene zidachitika ku Antiokeya, zidachitikanso ku Ikonio. Paulo ndi Barnabasi adaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Adaphunzitsa mwamphamvu, kotero kuti anthu ambirimbiri, Ayuda ndiponso anthu a mitundu ina, adakhulupirira.
2
Koma Ayuda amene sadakhulupirire adautsa mitima ya akunjawo kuti adane ndi akhristu.
3
Paulo ndi Barnabasi adakhala komweko kanthaŵi ndithu, akulalika molimba mtima za kukoma mtima kwa Ambuye. Ndipo Ambuye ankachitira umboni mau ao pakuŵapatsa mphamvu zochitira zizindikiro ndi zozizwitsa.
4
Koma anthu amumzindamo adagaŵikana, ena anali mbali ya Ayuda, ena anali mbali ya atumwi.
5
Pamenepo anthu akunja ndi Ayuda, pamodzi ndi akulu ao, adatsimikiza zoŵazunza ndi kuŵaponya miyala.
6
Atumwi aja atamva zimenezi, adathaŵira ku Listara ndi ku Deribe, mizinda ya ku Likaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo.
7
Kumenekonso adayamba kulalika Uthenga Wabwino.
8
Ku Listara kunali munthu wina wopunduka miyendo amene ankangokhala pansi. Adaabadwa wolumala ndipo chikhalire chake sadayende.
9
Iyeyo ankamvetsera pamene Paulo ankalankhula. Paulo adampenyetsetsa, ndipo ataona kuti munthuyo ali ndi chikhulupiriro choti nkuchira,
10
adanena mokweza mau kuti, “Wongola miyendo yako, imirira.” Pomwepo munthuyo adadzambatuka nkuyamba kuyenda.
11
Pamene anthu onse aja adaona zimene Paulo adachita, adafuula m'Chilikaoniya kuti, “Yatitsikira milungu yooneka ngati anthu.”
12
Motero Barnabasi adamutcha Zeusi ndipo Paulo adamutcha Heremesi, chifukwa ndiye ankatsogola polankhula.
13
Nyumba yopembedzeramo Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo. Tsono wansembe wake adabwera ku zipata atatenga ng'ombe yozekedwa maluŵa m'khosi. Iyeyo pamodzi ndi anthu onse aja adaafuna kudzapereka nsembe.
14
Koma pamene atumwi aja, Barnabasi ndi Paulo, adamva zimenezi, adang'amba zovala zao, nathamangira pakati pa anthuwo. Adalankhula mokweza mau kuti,
15
“Anthuni, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Tikukulalikirani Uthenga Wabwino wakuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'menemo.
16
Kale Iye adaalekerera anthu a mitundu yonse kuti azitsata njira zaozao.
17
Komabe sankaleka kudzichitira umboni mwa zabwino zimene amachita. Kuchokera kumwamba amakupatsani mvula ndi nyengo za zipatso. Amakupatsani zakudya ndi zina zambiri zodzaza mitima yanu ndi chimwemwe.”
18
Ngakhale ndi mau ameneŵa, adavutika kuŵaletsa anthu aja kuti asaŵaphere nsembe.
19
Koma kudabwera Ayuda ena ochokera ku Antiokeya ndi ku Ikonio nakopa anthu aja. Tsono anthuwo adamponya Pauloyo miyala, kenaka nkumuguzira kunja kwa mzinda, chifukwa ankayesa kuti wafa.
20
Koma ophunzira ena atasonkhana nkumzungulira, iye adauka naloŵanso mumzindamo. M'maŵa mwake iye ndi Barnabasi adapita ku Deribe.
21
Paulo ndi Barnabasi atalalika Uthenga Wabwino ku Deribe kuja, ndi kukopa okhulupirira ambiri, adabwerera ku Listara, ku Ikonio ndi ku Antiokeya m'dera la Pisidiya.
22
Adaŵalimbitsa mtima ophunzira aja, naŵauzitsa kuti asataye chikhulupiriro chao. Adaŵauza kuti, “Kuti tiloŵe mu Ufumu wa Mulungu tiyenera kupirira masautso ambiri.”
23
Pa mpingo uliwonse adakhazika akulu a mpingo. Ndipo pakupemphera ndi kusala zakudya adaŵapereka kwa Ambuye amene anali atamkhulupirira tsopano.
24
Pambuyo pake adabzola Pisidiya nakafika ku Pamfiliya.
25
Ndipo atalalika mau a Mulungu ku Perga, adapita ku Ataliya.
26
Kumeneko adaloŵa m'chombo kupita ku Antiokeya kuja, kumene adaaperekedwa kwa Mulungu kuti aŵadalitse pa ntchito imene tsopano anali ataitsiriza.
27
Pamene adafika kumeneko, adasonkhanitsa mpingo wonse, naufotokozera zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo, ndiponso m'mene Iye adaatsekulira anthu a mitundu ina njira kuti akhulupirire.
28
Tsono adakhala komweko ndi ophunzira aja nthaŵi yaitali.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28