bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 10
Acts 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 11 →
1
Ku Kesareya kunali munthu wina, dzina lake Kornelio. Iyeyu anali mkulu wa asilikali 100 achiroma, a m'gulu lotchedwa “Gulu la ku Italiya.”
2
Anali munthu wotsata zachipembedzo, ndipo iye pamodzi ndi banja lake lonse ankaopa Mulungu. Ankathandiza kwambiri Ayuda osauka, ndipo ankapemphera Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi.
3
Tsiku lina dzuŵa litapendeka, nthaŵi ili ngati 3 koloko, adaona zinthu m'masomphenya. Adaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu akubwera kwa iye nkunena kuti, “Kornelio!”
4
Iye adayang'anitsitsa mngeloyo mantha atamgwira, ndipo adamufunsa kuti, “Nkwabwino, Ambuye?” Mngeloyo adati, “Mulungu wakondwera nawo mapemphero ako ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo zako.
5
Tsopano tuma anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina, dzina lake Simoni, wotchedwanso Petro.
6
Akukhala kwa Simoni wina, mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja.”
7
Mngelo amene ankalankhula naye uja atachoka, Kornelio adaitana antchito ake aŵiri, ndiponso msilikali. Msilikaliyo anali mmodzi mwa amene ankamutumikira, ndipo anali munthu wopembedza Mulungu.
8
Kornelio uja ataŵafotokozera zonse, adaŵatuma ku Yopa.
9
M'maŵa mwake, iwo aja akali m'njira koma akuyandikira mudziwo, Petro adakwera pa denga kukapemphera, nthaŵi ili ngati 12 koloko masana.
10
Ali pamenepo, adamva njala, namafuna kudya. Koma pamene anthu ankakonza chakudya, iye adachita ngati wakomoka.
11
Adaona kuthambo kutatsekuka, chinthu china chikutsikira pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa nsonga zake zinai.
12
M'menemo munali nyama zamitundumitundu, ndi zokwaŵa, ndiponso mbalame zamumlengalenga.
13
Tsono Petro adamva mau akuti, “Petro dzuka, ipha udye.”
14
Koma Petro adati, “Iyai, pepani Ambuye, ine sindinadyepo ndi kale lonse chinthu chosayera kapena chonyansa.”
15
Kenaka Petro adamvanso kachiŵiri mau akuti, “Zimene Mulungu waziyeretsa, iwe usati nzosayera.”
16
Zimenezi zidachitika katatu, ndipo pompo chinthu chija chidatengedwa kupitanso kumwamba.
17
Petro adayamba kusinkhasinkha za tanthauzo la zimene adaaziwona m'masomphenya zija. Nthaŵi yomweyo anthu amene Kornelio adaaŵatuma aja, ankafunsa za nyumba ya Simoni, ndipo tsopano adaadzaima pa khomo.
18
Adaitana nkufunsa kuti, “Kodi kuli mlendo kuno, dzina lake Simoni, wotchedwanso Petro?”
19
Pamene Petro ankalingalirabe za zimene adaaziwona m'masomphenya zija, Mzimu Woyera adamuuza kuti, “Iwe, anthu atatu akukufuna.
20
Nyamuka, tsika, upite nawo osakayika, pakuti ndaŵatuma ndine.”
21
Apo Petro adatsika nauza anthu aja kuti, “Amene mukumfunayo ndine. Kodi nkwabwino?”
22
Iwo adati, “Kornelio, mkulu wa gulu la asilikali 100, watituma. Iyeyo ndi munthu wolungama ndi woopa Mulungu, ndipo Ayuda onse amamtama. Mngelo wa Mulungu adamuuza kuti akuitaneni kuti mupite kunyumba kwake akamve mau amene muli nawo.”
23
Pamenepo Petro adaŵaloŵetsa m'nyumba, naŵasamala. M'maŵa mwake adanyamuka napita nawo, ndipo abale ena a ku Yopa adamperekeza.
24
M'maŵa mwake adafika ku Kesareya. Kornelio ankaŵadikira, atasonkhanitsa abale ndi abwenzi ake apamtima.
25
Pamene Petro ankati aziloŵa, Kornelio adadzakumana naye, nadzigwetsa kumapazi kwake, namuŵeramira.
26
Koma Petro adamuimiritsa nati, “Iyai, imirirani, inenso ndine munthu chabe.”
27
Ndipo akulankhula naye, adaloŵa napeza anthu ambiri atasonkhana.
28
Pamenepo Petro adaŵauza kuti, “Inu nomwe mukudziŵa kuti Myuda saloledwa konse kuyanjana ndi munthu wa mtundu wina, ngakhale kuloŵa m'nyumba mwake. Koma Mulungu wandidziŵitsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ngwosayera kapena wonyansa.
29
Nchifukwa chake ndabwera mosaŵiringula pamene mudandiitana. Tsono ndimati ndidziŵe chimene mwandiitanira.”
30
Kornelio adati, “Dzana ilo, ndinkapemphera m'nyumba mwanga, nthaŵi ngati yomwe ino ya 3 koloko dzuŵa litapendeka. Mwadzidzidzi kutsogolo kwangaku kudaimirira munthu wovala zovala zonyezimira.
31
Adandiwuza kuti, ‘Kornelio, Mulungu wamva pemphero lako, ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo.
32
Tsono tuma anthu ku Yopa akaitane Simoni wotchedwa Petro. Iyeyu akukhala kwa Simoni, mmisiri wa zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa njanja.’
33
Nchifukwa chake ndidaakutumirani anthu msanga, ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akulamulani kuti munene.”
34
Petro adayamba kulankhula, adati, “Zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho.
35
Amalandira bwino munthu wa mtundu uliwonse womuwopa nkumachita chilungamo.
36
Mukudziŵa kuti adatumizira Aisraele mau ake naŵauza Uthenga Wabwino wa mtendere kudzera mwa Yesu Khristu, amene ali Ambuye a anthu onse.
37
Mukudziŵa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthaŵi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake.
38
Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.
39
Ife ndife mboni za zonse zimene Iye adachita mu Yerusalemu ndi m'dziko lonse la Ayuda. Iwo adamupha pakumpachika pa mtanda.
40
Komabe mkucha wake Mulungu adamuukitsa kwa akufa, nalola kuti aonekere poyera.
41
Sadaonekere kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zimene Mulungu adazisankhiratu. Ndiye kuti adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa.
42
Ndipo adatilamula kuti tikalalikire anthu onse, ndi kuchita umboni kuti Iyeyo ndiye amene Mulungu adamsankha kukhala Woweruza anthu amoyo ndi akufa omwe.
43
Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.”
44
Petro akulankhulabe, Mzimu Woyera adaŵatsikira anthu onse amene ankamva mauwo.
45
Ndipo okhulupirira achiyuda amene adaaperekeza Petro, adadabwa kuti Mulungu adapereka mphatso ya Mzimu Woyera ndi kwa anthu akunja omwe.
46
Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati,
47
“Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?”
48
Motero adalamula kuti abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Ndipo anthuwo adampempha kuti akhale nawo masiku angapo.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28