bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 24
Acts 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 25 →
1
Patapita masiku asanu, Ananiya, mkulu wa ansembe onse, adadza pamodzi ndi akuluakulu ena a Ayuda, ndi katswiri wina wolankhulira anthu pa milandu, dzina lake Tertulo. Iwo adafika pamaso pa bwanamkubwa uja, nayamba kuneneza Paulo.
2
Tsono Pauloyo atamuitana, Tertulo uja adayambapo zomunenezazo. Adati, “Inu a Felikisi olemekezeka, ife tikukhala pa mtendere weniweni chifukwa cha inu, ndipo zinthu zambiri zakhala zikukonzeka m'dziko mwathu chifukwa cha utsogoleri wanu wanzeru.
3
Zonsezi timazilandira moyamika kwambiri ponseponse mwa njira iliyonse.
4
Pepani sindikufuna kukutayitsani nthaŵi, komabe ndimapempha kuti mundikomere mtima, mungomvapo mau athuŵa mwachidule.
5
Ndiye kuti munthu uyu ife tampeza kuti ngwovutitsa kwabasi. Wakhala akuutsa chipolowe pakati pa Ayuda pa dziko lonse lapansi, ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lopatulika la Anazarete.
6
Adaayesanso ngakhale kuipitsa Nyumba ya Mulungu yathu. Ndiye ife tidamgwira.” [“Tidafuna kumuweruza potsata Malamulo athu.
7
Koma Lisiasi, mkulu wa asilikali, adadzamtsomphola kumanja kwathu mwankhondo,
8
kenaka nkulamula kuti omneneza adzaonekere kwa inu.”] “Mukamufunsa ameneyu, mutha kudziŵa nokha zonse zimene tikumnenezera.”
9
Ayudanso adavomereza, nanenetsa kuti zonsezo nzoona.
10
Bwanamkubwa uja adakodola Paulo kuti alankhule, ndipo Paulo adati, “Ndikudziŵa kuti inu mwakhala mukuweruza mtundu uwu zaka zambiri tsopano, nchifukwa chake ndakondwa kuti ndiyankhe pamaso panu zimene akundinenezazi.
11
Inu nomwe mutha kupeza umboni wake, sipadapite masiku opitirira khumi ndi aŵiri chipitire changa ku Yerusalemu kukapembedza.
12
Ayuda sadandipezepo ndikukangana ndi munthu aliyense m'Nyumba ya Mulungu, kapena kuutsa chipolowe pakati pa anthu m'nyumba zamapemphero, kaya pena paliponse mumzindamo.
13
Iwoŵa sangakutsimikizireni zimene akundinenezazi.
14
Koma ichi chokha ndikuvomera pamaso panu, kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu potsata Njira imene iwoŵa amati ndi gulu lopatulika. Ndimakhulupirira zonse zolembedwa m'Malamulo a Mose ndiponso m'mabuku a aneneri.
15
Popeza kuti ndimakhulupirira Mulungu, ndimakhulupirira, monga iwonso amakhulupirira, kuti anthu onse, olungama ndi osalungama omwe, adzauka kwa akufa.
16
Nchifukwa chake inenso ndimayesetsa nthaŵi zonse kukhala ndi mtima wangwiro pamaso pa Mulungu, ndi pamaso pa anthu.
17
“Tsono nditakhala kwina zaka zingapo, ndidabwera kudzatula zopereka zachifundo kwa anthu a mtundu wanga, ndiponso kudzapereka nsembe.
18
Pamene ndinkachita zimenezi, iwo adandipeza m'Nyumba ya Mulungu nditachita mwambo wakudziyeretsa. Panalibe konse khamu la anthu kapena chipolowe ai.
19
Koma kunali Ayuda ena a ku Asiya. Iwowo akadayenera kukhala pano pamaso panu kudzandineneza okha ngati ali nane nkanthu.
20
Kapena omwe ali panoŵa anene ngati adandipeza cholakwa pamene ndinali m'Bwalo lao Lalikulu lamilandu.
21
Koma cholakwa changa chingathe kukhala chokhachi chakuti, pamene ndidaaimirira pamaso pao, ndidaafuula kuti, ‘Mukundizenga mlandu ine lero chifukwa ndimakhulupirira kuti anthu akufa adzauka.’ ”
22
Felikisi ankadziŵa bwino za Njira ya Ambuye, choncho adatseka bwalolo ndi mau akuti, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera Lisiasi, mkulu wa asilikali.”
23
Tsono adalamula mtsogoleri wa gulu la asilikali kuti azimlonda, koma azimpatsakonso ufulu, osaletsa abwenzi ake kumamsamala.
24
Patapita masiku angapo Felikisi adabwera ndi mkazi wake Durusila, amene anali Myuda. Adaitana Paulo, nayamba kumvetsera zimene iye ankalankhula za kukhulupirira Khristu Yesu.
25
Koma pamene Paulo adakamba za chilungamo, za kudziletsa, ndi zakuti Mulungu adzaweruza anthu, Felikisi adachita mantha namuuza kuti, “Pakali pano bapita, ndikapeza nthaŵi, ndichita kukuitananso.”
26
Koma ankaganiza kuti Paulo adzampatsa ndalama, nchifukwa chake ankamuitana kaŵirikaŵiri namacheza naye.
27
Patapita zaka ziŵiri, Porkio Fesito adaloŵa m'malo mwa Felikisi. Tsono Felikisiyo pofuna kuchita mkomya kwa Ayuda, adamsiya m'ndende Paulo uja.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28