bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 28
Acts 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
1
Titapulumuka choncho, tidamva kuti chilumbacho dzina lake ndi Melita.
2
Anthu apamenepo adatichitira zabwino kwambiri. Adatilandira bwino natisonkhera moto, chifukwa kudaayamba kugwa mvula ndipo kunkazizira.
3
Paulo adakatola nkhuni nabwerako ndi mtolo, ndipo pamene ankaziika pa moto, mumtolomo mudatuluka mphiri chifukwa cha kutenthako. Idamluma nkukanirira ku dzanja lakelo.
4
Pamene anthuwo adaona njokayo ili lende ku dzanja lake, adayamba kuuzana kuti, “Ndithudi munthu ameneyu nchigaŵenga. Ngakhale wapulumuka pa nyanja, koma Mulungu wachilungamo sadamlole kuti akhale ndi moyo.”
5
Komabe Paulo adaikutumulira pa moto njokayo, osapwetekedwa konse.
6
Anthu aja ankayembekeza kuti thupi lake litupa, kapena kuti agwa mwadzidzidzi nkufa. Adakhala akumuyang'ana nthaŵi yaitali, koma ataona kuti palibe chilichonse chachilendo chimene chamchitikira, adasintha maganizo nati, “Ameneyu ndi mmodzi wa milungu.”
7
Pafupi ndi malowo panali minda ya Publio, mkulu wa pachilumbapo. Iye adatilandira natisamala bwino masiku atatu.
8
Bambo wake wa Publioyo anali gone, chifukwa ankadwala malungo ndi kamwazi. Paulo adaloŵa m'chipinda chake nayamba kupemphera, ndipo adamsanjika manja nkumuchiritsa.
9
Zitachitika zimenezi, anthu ena onse odwala pachilumbapo adabwera, Paulo nkuŵachiritsa.
10
Anthu aja adatipatsa mphatso zambiri, ndipo pamene tidanyamukanso ulendo wathu wapachombo, adatipatsa zonse zosoŵeka.
11
Patapita miyezi itatu, tidanyamukadi ulendo wathu pa chombo china, chimene chidaakhala pachilumbapo pa nthaŵi yachisanu. Chombocho chinali chochokera ku Aleksandriya, ndipo chinkatchedwa “Ana Amapasa.”
12
Titafika ku Sirakusa, tidakhalako masiku atatu.
13
Kuchokera kumeneko tidapitirira nkukafika ku Regio. Patapita tsiku limodzi, mphepo ya mwera idayamba kuwomba, choncho pa tsiku lotsatira tidafika ku Puteoli.
14
Kumeneko tidapeza abale, ndipo adatiitana kuti tikhale nawo masiku asanu ndi aŵiri. Motero tidakafika ku Roma.
15
Abale akumeneko atamva za ife, adabwera mpaka ku Bwalo la Apio ndiponso ku Nyumba za Alendo Zitatu kudzatichingamira. Paulo ataona ataŵaona, adayamika Mulungu, nalimba mtima.
16
Pamene tidaloŵa mu mzinda wa Roma, Paulo adaloledwa kukhala kwayekha ndi msilikali womulonda.
17
Patapita masiku atatu, Paulo adasonkhanitsa atsogoleri a Ayuda akomweko. Atasonkhana, iye adaŵauza kuti, “Abale anga, ine ndili kuno ngati mkaidi wochokera ku Yerusalemu. Ngakhale sindidalikwire mtundu wathu, kapena miyambo ya makolo athu, komabe ndidaperekedwa kwa Aroma.
18
Iwo atandifunsa, adaafuna kundimasula, chifukwa sadapeze mlandu woyenera kundiphera.
19
Koma pamene Ayuda adakana, ndidakakamizidwa kupempha kuti mlandu wangawo ndidzagwade kwa Mfumu ya ku Roma kuno. Sikuti ndinali ndi kanthu konenezera mtundu wanga ai.
20
Nkuwona ndakuitanani kuti ndilankhule nanu. Pakuti ndamangidwa ndi unyolo uwu chifukwa chokhulupirira chinthu chimene Aisraele akuyembekeza.”
21
Atsogoleriwo adamuyankha kuti, “Ife sitidalandirepo makalata ochokera ku Yudeya onena za inu. Palibenso wina mwa abale athu amene adafika kuno kudzatifotokozera kapena kudzatiwuza zoipa za inu.
22
Koma makamaka nkwabwino kuti mutiwuze maganizo anu, pakuti za gulu lanu lopatulikali tikudziŵa kuti ponseponse anthu akutsutsana nalo.”
23
Pamenepo iwo adapangana naye tsiku, ndipo ambiri adaabwera kunyumba kumene iye ankakhala. Kuyambira m'maŵa mpaka madzulo Paulo adakhala akulankhula nawo, naŵafotokozera za ufumu wa Mulungu. Pakuŵatchulira mau a m'Malamulo a Mose ndiponso m'mabuku a aneneri, ankayesa kuŵakopa kuti akhulupirire Yesu.
24
Ena adakopekadi ndi zimene iye adanena, koma ena sadakhulupirire.
25
Tsono popeza kuti anthuwo sadamvane, adangochokapo. Komabe asanachoke, Paulo adaawonjezapo mau amodzi aŵa akuti, “Mzimu Woyera adaanena zoona pamene adaauza makolo anu mwa mneneri Yesaya kuti,
26
“ ‘Pita kwa anthu a mtundu uwu ndi kuŵauza kuti: Kumva mudzamva, koma osamvetsa, kupenya mudzapenya, koma osazindikira.
27
Ndithu mtima wa anthu a mtundu uwu wauma, agonthetsa makutu ao ndipo atseka maso ao, kuwopa kuti angaone ndi maso ao, ndipo angamve ndi makutu ao, angamvetse ndi mtima wao, natembenukira mwa Ine kuti ndiŵachitiritse.’ ”
28
Paulo adaŵauza kuti, “Dziŵani tsono kuti Mulungu watumiza chipulumutso chakechi kwa anthu a mitundu ina. Iwowo adzamva.” [
29
Paulo atanena mau ameneŵa, Ayuda aja adachokapo akutsutsana kwambiri.]
30
Tsono Paulo adakhala kumeneko zaka ziŵiri zathunthu m'nyumba yake yobwereka, ndipo ankaŵalandira bwino lomwe onse obwera kudzamuwona.
31
Ankalalika za ufumu wa Mulungu, ndi kumaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu poyera, popanda wina aliyense womuletsa.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28