bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 26
Acts 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 27 →
1
Agripa adauza Paulo kuti, “Tikukulola kuti unene mau ako.” Tsono Paulo adatambalitsa dzanja lake nayamba kunena nkhani yake. Adati,
2
“Inu Mfumu Agripa, ine ndikuganiza kuti ndine wamwai kuti ndi pamaso panu pamene ndiyankhe lero zonse zimene Ayuda akhala akundineneza.
3
Makamaka chifukwa inu mumaidziŵa bwino miyambo yonse yachiyuda, ndiponso mikangano yao yonse, ndikukupemphani kuti mundimvere moleza mtima.
4
“Ayuda onse akudziŵa za moyo wanga wonse kuyambira ndili mwana. Akudziŵa m'mene ndinkakhalira chiyambire pakati pa anthu a mtundu wanga, ndiponso ku Yerusalemu.
5
Iwo adandidziŵa kuyambira kale, ndipo ngati afuna, angathe kundichitira umboni kuti moyo wanga wonse ndakhala Mfarisi, mmodzi wa gulu lija limene limasamala chipembedzo chathu koposa.
6
Ndipo tsopano ngati akundizenga mlandu, nchifukwa chakuti ndikuyembekeza zimene Mulungu adalonjeza makolo athu.
7
Mafuko onse khumi ndi aŵiri a mtundu wathu, popembedza Mulungu usana ndi usiku mosafookera, amayembekeza kudzalandira zimene Iye adalonjezazo. Mwakuti nchifukwa cha chiyembekezo chimenechi, amfumu, kuti Ayuda akundineneza.
8
Bwanji ena mwa inu Ayuda mumayesa kuti nkosatheka kukhulupirira kuti Mulungu nkuukitsa anthu kwa akufa?
9
“Ine ndemwe ndinkaganiza kuti ndinkayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthetsa mbiri ya Yesu wa ku Nazarete.
10
Ndipo ndidaazichitadi ku Yerusalemu. Akulu a ansembe atandipatsa ulamuliro, ine ndinkaŵatsekera m'ndende anthu ambiri a Mulungu. Pamene iwo ankaphedwa, ine ndinkavomereza.
11
Kaŵirikaŵiri ndinkaŵalanga m'nyumba zonse zamapemphero, ndi kuyesa kuŵakakamiza kuti amnyoze Yesuyo. Ndinkaŵachitira ukali woopsa, kotero kuti ndinkaŵazunza ngakhale ku mizinda ya ku maiko achilendo.”
12
“Pa ulendo wina wotere, ndinkapita ku Damasiko ndi ulamuliro ndi mphamvu zondipatsa akulu a ansembe.
13
Pa njira, nthaŵi yamasana dzuŵa lili pa mutu, inu amfumu, ndidaona kuŵala kochokera kumwamba. Kuŵalako kunali koposa kuŵala kwa dzuŵa, ndipo kudatizinga tonse, ine ndi anzanga aulendo.
14
Tonse tidagwa pansi, ndipo ine ndidamva mau ondiwuza pa Chiyuda kuti, ‘Saulo, Saulo, ukundizunziranji? Ukungodzipweteka wekha ngati ng'ombe yoponda zidyali pa chobayira.’
15
Apo ndidafunsa kuti, ‘Ndinu yani, Ambuye?’ Ambuyewo adati, ‘Ine ndiye Yesu, amene ukumzunza.
16
Koma dzuka, imirira. Pakuti ndakuwonekera kuti ndikuike kuti ukhale mtumiki wanga ndi mboni yanga. Ndifuna kuti ukhale mboni ya m'mene wandiwonera lero, ndiponso ya zimene ndidzakuwonetsa m'tsogolo.
17
Ndidzakulanditsa kwa anthu a mtundu wako, ndiponso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutuma.
18
Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’
19
“Nchifukwa chake, mfumu Agripa, sindidakane kumvera zimene Mulungu adandiwonetsa m'masomphenyazo.
20
Koma ndidalalika poyamba kwa anthu a ku Damasiko ndi a ku Yerusalemu, ndipo bwino lake ku dziko lonse la Yudeya, ndiponso kwa anthu a mitundu ina. Ndidalalika kuti atembenuke mtima, kutembenukira kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zotsimikiza kuti atembenukadi mtima.
21
Chifukwa cha zimenezi Ayuda adandigwira m'Nyumba ya Mulungu nafuna kundipha.
22
Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero. Motero ndaimirira pano kuti ndichite umboni pamaso pa anthu onse, aakulu ndi ang'ono omwe. Zimene ndikuŵauza si zina ai, koma ndi zomwezo zimene aneneri ndi Mose adanena kuti zidzachitika.
23
Paja iwo adati Mpulumutsi wolonjezedwa uja adzamva zoŵaŵa, ndipo popeza kuti Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalengeza Ayuda ndi amene sali Ayuda za kuŵala kwa chipulumutso.”
24
Pamene Paulo ankadziteteza ku zomnenezazo, Fesito adanena mokweza mau kuti, “Misalatu imeneyi, iwe Paulo! Kuphunziritsa kwako kukukupengetsa.”
25
Koma Paulo adati, “Pepani, a Fesito olemekezeka, sindine wamisala ai. Zimene ndikunenazi nzoona ndi zanzeru.
26
Mfumu Agripa akudziŵa zonsezi, nkuwona ndikulankhula pamaso pao momasuka. Ndikhulupirira kuti palibe kanthu nkamodzi komwe pa zimenezi kamene iwo sakadziŵa. Pakuti sizidachitike mobisika ai.
27
Inu mfumu Agripa, kodi mumakhulupirira mau a aneneri? Ndikudziŵa kuti mumaŵakhulupirira.”
28
Apo Agripa adauza Paulo kuti, “Uganiza kuti nkundisandutsa mkhristu pa kanthaŵi kochepa, komweka?”
29
Paulo adati, “Kaya ndi pa kanthaŵi kochepa kaya nthaŵi yaitali, Mulungu akadalola kuti osati inu nokha, komanso anthu onse amene alikumva mau anga lero, akhale monga momwe ndiliri inemu, kupatula maunyolo okhaŵa.”
30
Pamenepo mfumu Agripa, bwanamkubwa, Berenise, ndi onse amene anali nawo adaimirira.
31
Atachokapo adauzana kuti, “Munthuyu sakuchita chilichonse choyenera kumuphera kapena kumponyera m'ndende.”
32
Tsono Agripa adauza Fesito kuti, “Tikadammasula munthuyu akadapanda kupempha kuti mlandu wakewu ukazengedwe ndi Mfumu ya ku Roma.”
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28