bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 17
Acts 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 18 →
1
Paulo ndi anzake aja adapitirira mizinda ya Amfipoli ndi Apoloniya nakafika ku Tesalonika. Kumeneko kunali nyumba yamapemphero ya Ayuda.
2
Tsono Paulo adaloŵa nawo monga adaazoloŵera, ndipo adakambirana nawo za m'Malembo pa masabata atatu.
3
Adaŵamasulira za m'Malembomo ndi kuŵatsimikizira kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa kenaka nkuuka kwa akufa. Paulo adati, “Yesu amene ndikukulalikiraniyu, ndiye Mpulumutsiyo.”
4
Tsono ena mwa iwo adakopeka, natsata Paulo ndi Silasi. Agriki ambirimbiri opembedza Mulungu adateronso, pamodzi ndi akazi ambiri apamwamba.
5
Koma Ayuda ena adachita nsanje, choncho adasonkhanitsa anthu opandapake ongoyendayenda, nayambitsa chipolowe mumzindamo. Adathamangira ku nyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Silasi kuti aŵatulutsire ku anthu.
6
Poona kuti sadaŵapeze, adamtenga Yasoniyo pamodzi ndi abale ena nkuŵaguzira kwa akulu amumzindamo. Tsono adafuula kuti, “Anthu aja amene akhala nasokoneza anthu ponseponse, tsopano afikanso kwathu kuno,
7
ndipo Yasoni waŵalandira. Onseŵa akuchita zosagwirizana ndi malamulo a Mfumu ya ku Roma, pakunena kuti ati kulinso mfumu ina, dzina lake Yesu.”
8
Mau ameneŵa adautsa mitima ya anthuwo ndi ya akulu amumzinda aja.
9
Koma Yasoni ndi anzake aja atalipira mlanduwo, akuluwo adaŵamasula.
10
Kutangoda, abale aja adapititsa Paulo ndi Silasi ku Berea. Atafika kumeneko, adakaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda.
11
Ayuda akumeneko anali a mitima yomasuka, kusiyana ndi aja a ku Tesalonika. Iwoŵa adalandira mau a Mulungu ndi mtima wofunitsitsa, ndipo tsiku ndi tsiku ankafufuza m'Malembo kuti aone ngati nzoona zimene Paulo ndi Silasi ankanena.
12
Motero mwa iwowo ambiri adakhulupirira, ndiponso Agriki ambiripo, akazi apamwamba ndi amuna omwe, adakhulupirira.
13
Koma Ayuda a ku Tesalonika aja atamva kuti Paulo adalalika mau a Mulungu ndi ku Berea komwe, adakafika komwekonso, nayamba kukolezera ndi kuutsa mitima ya anthu.
14
Nthaŵi yomweyo abale aja adatuma anthu ena kuti aperekeze Paulo ku nyanja, koma Silasi ndi Timoteo adakhalira komweko.
15
Anthu amene adaaperekeza Paulo aja adakafika naye mpaka ku Atene. Pambuyo pake adabwerera ku Berea, Paulo ataŵalamula kukauza Silasi ndi Timoteo kuti amlondole msanga.
16
Pamene Paulo ankadikira Silasi ndi Timoteo ku Atene, mtima wake udavutika kwambiri poona kuti mzinda wonse ngwodzaza ndi mafano.
17
Tsono adakambirana m'nyumba yamapemphero ndi Ayuda ndi anthu ena opembedza Mulungu. Adakambirananso ndi anthu amene ankangokumana nawo pa msika tsiku ndi tsiku.
18
Anzeru enanso a magulu a Aepikurea ndi Astoiki adadzatsutsana naye. Ena ankati, “Kodi mbutuma yolongololayi ikufunanso kunena chiyani?” Enanso ankati, “Ameneyu akukhala ngati wolalika za milungu yachilendo.” Ankanena zimenezi chifukwa iye ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Yesu, ndi za kuuka kwa akufa.
19
Tsono adapita naye ku bwalo lamilandu lotchedwa Areopagi, namuuza kuti, “Ife timati mutidziŵitseko zatsopano zimene mukuphunzitsazi?
20
Pakuti zina zimene mukutiwuzazi nzachilendo, ndipo tikufuna kudziŵa kuti zinthuzi nzotani.”
21
Ndiye kuti nzika za ku Atene ndi alendo okhala kumeneko, inali ngati ntchito nthaŵi zonse kumangomvera zatsopano ndi kumazifotokozera.
22
Paulo adaimirira pakati pa bwalo lija la Aeropagi nati, “Inu anthu a ku Atene, pa zonse ndikuwona kuti ndinu anthu opembedza kwambiri.
23
Pakuti pamene ndinalikuyenda mumzindamu, nkumaona malo anu osiyanasiyana achipembedzo, ndinapezanso guwa lina lansembe pamene padalembedwa mau akuti, ‘Kwa Mulungu wosadziŵika.’ Tsonotu amene mumampembedza osamdziŵayo, ndi yemweyo amene ine ndikukulalikirani.
24
Mulungu amene adalenga dziko lapansi ndiponso zonse zili m'menemo, ndiye Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi. Iye sakhala m'nyumba zachipembedzo zomangidwa ndi anthu ai.
25
Anthu sangamtumikire ndi manja ao, ngati kuti Iye amasoŵa kanthu. Pajatu Iye ndiye amapatsa anthu onse moyo, mpweya ndi zina zonse.
26
Kochokera mwa kholo limodzi Iye adalenga mitundu yonse ya anthu, kuti ikhale pa dziko lonse lapansi. Adakonzeratu nthaŵi ya moyo wao, ndiponso malire a pokhala pao.
27
Mulungu adafuna kuti anthu amufunefune, ndipo kuti pomfufuzafufuza, mwina nkumupeza. Komabe Iye sali kutali ndi aliyense mwa ife.
28
Paja “ ‘Mwa Iye ife timakhala ndi moyo, timayenda ndipo timakhala tilipo.’ Monga adanenera opeka ndakatulo anu ena kuti, “ ‘Ifenso ndife ofumira mwa Iye ngati ana ake.’
29
“Tsono popeza kuti tili ngati ana a Mulungu, sitiyenera kuganiza kuti umulungu wake umafanafana ndi fano lagolide kapena lasiliva kapena lamwala, lopangidwa mwa luso ndi nzeru za munthu.
30
Mulungu adaaŵalekerera anthu pa nthaŵi imene iwo anali osadziŵa, koma tsopano akuŵalamula anthu onse ponseponse kuti atembenuke mtima.
31
Chifukwa adaika tsiku pamene Iye adzaweruza anthu a pa dziko lonse lapansi molungama kudzera mwa Munthu amene Iye adamsankha. Adatsimikizira anthu onse zimenezi pakuukitsa Munthuyo kwa akufa.”
32
Pamene anthuwo adamva za kuuka kwa akufa, ena adangoseka. Koma ena adati, “Bwanji mudzatiwuzenso zimenezi tsiku lina.”
33
Choncho Paulo adaŵasiya.
34
Koma ena adamtsata, nakhulupirira. Pakati pao panali Dionizio, mmodzi mwa a bwalo la milandu lotchedwa Areopagi, ndiponso mai wina, dzina lake Damalisi, ndi enanso.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28