bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 23
Acts 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 24 →
1
Paulo adaŵapenyetsetsa a m'Bwalo Lalikulu aja nati, “Abale anga, ine moyo wanga wonse mpaka lero lino ndakhala ndi mtima wangwiro pamaso pa Mulungu.”
2
Apo Ananiya, mkulu wa ansembe onse, adalamula amene adaaimirira pafupi ndi Paulo kuti, “Mtchayeni kukamwako!”
3
Pamenepo Paulo adamuuza kuti, “Mulungu adzatchaya iweyo, chipupa chopaka njeresawe! Iwe wakhala pamenepo kuti undiweruze potsata Malamulo a Mose, nanga bwanji ukuŵaphwanya Malamulowo pakulamula kuti anditchaye?”
4
Apo amene adaaimirira pafupi adauza Paulo kuti, “Bwanji ukunena zachipongwe kwa mkulu wa ansembe wa Mulungu?”
5
Paulo adati, “Pepani abale, sindimadziŵa kuti ndi mkulu wa ansembe onse. Paja mau a Mulungu akuti, ‘Usamnenere zoipa woweruza anthu ako.’ ”
6
Pamene Paulo adaona kuti ena mwa iwo ndi a m'gulu la Asaduki, ena a m'gulu la Afarisi, adanena mokweza mau m'Bwalo muja kuti, “Abale anga, inetu ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ineyo ndikuweruzidwa chifukwa ndimakhulupirira kuti anthu adzauka kwa akufa.”
7
Atanena zimenezi, Afarisi ndi Asaduki aja adayamba kukangana, ndipo msonkhano udagaŵana.
8
Paja Asaduki amati anthu sadzauka kwa akufa, ndiponso kuti kulibe angelo kapena mizimu. Koma Afarisi amakhulupirira zonsezi.
9
Anthu aja adayamba kufuula kwambiri. Tsono aphunzitsi ena a Malamulo, a m'gulu la Afarisi, adaimirira nanenetsa kuti, “Sitikupeza konse cholakwa mwa munthuyu ai. Mwina nkukhala kuti mzimu kapena mngelo walankhula naye!”
10
Anthu aja adafika pokangana koopsa, kotero kuti mkulu wa asilikali uja ankaopa kuti angamkadzule Paulo. Choncho adalamula asilikali kuti, “Pitani mukamlanditse kwa anthuwo, mukamloŵetse m'linga la asilikali.”
11
Tsiku lomwelo, usiku, Ambuye adadzaima pafupi ndi Paulo namuuza kuti, “Limba mtima. Monga wandichitira umboni kuno ku Yerusalemu, uyenera kukandichitiranso umboni ku Roma.”
12
Kutacha, Ayuda ena adakhala upo, ndipo adapangana molumbira kuti, “Ife sitidya kapena kumwa chilichonse mpaka titamupha Pauloyo basi.”
13
Anthu amene adaapangana za chiwembu chimenechi analipo opititira makumi anai.
14
Iwowo adapita kwa akulu a ansembe ndi kwa akulu a Ayuda nakaŵauza kuti, “Ife talumbira kolimba kuti sitilaŵa kanthu mpaka titamupha Pauloyu.
15
Tsono inu, pamodzi ndi Bwalo Lalikulu lamilandu, mutumize mau kwa mkulu wa asilikali kuti abwere naye Paulo kwa inu, ngati kuti mukufuna kufunsitsa bwino za mlandu wake. Ife tili okonzeka kudzamuphha asanafike kuno.”
16
Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo atamva za chiwembuchi, adakaloŵa m'linga la asilikali lija nakamtsina khutu Paulo.
17
Apo Paulo adaitana mmodzi mwa atsogoleri a asilikali namuuza kuti, “Tapitani ndi mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali, akuti ali naye ndi mau.”
18
Iye adamtengadi mnyamatayo kupita naye kwa mkulu wa asilikali, namuuza kuti, “Mkaidi uja Paulo anandiitana, nandipempha kuti ndibwere ndi mnyamatayu kwa inu, akuti ali nanu ndi mau.”
19
Mkulu wa asilikali uja adamgwira pa dzanja mnyamatayo, namtengera pambali, ndipo ali paokha adamufunsa kuti, “Kodi ndi mau anji ukufuna kundiwuza?”
20
Iyeyo adati, “Ayuda ena apangana zodzakupemphani kuti mupite ndi Paulo ku Bwalo lao Lalikulu lamilandu maŵa, ngati kuti iwowo akufuna kufunsitsa bwino za mlandu wake.
21
Koma pepani, inu musaŵamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anai amene akukamlalira Paulo pa njira. Iwowo alumbira kuti sadzadya kapena kumwa chilichonse mpaka atamupha. Panopa ali okonzeka ndipo akungodikira kuti inu muŵabvomere.”
22
Tsono mkulu wa asilikali uja adauza mnyamatayo kuti, “Chabwino, iwe pita, koma usaululire wina aliyense kuti wadzandifotokozera zimenezi.”
23
Mkulu wa asilikali uja adaitana atsogoleri aŵiri a asilikali naŵauza kuti, “Uzani asilikali 200 akhale okonzeka kuyambira nthaŵi ya 9 koloko usiku uno, kupita ku Kesareya pamodzi ndi asilikali makumi asanu ndi aŵiri okwera pa kavalo, ndiponso 200 amikondo.
24
Mumkonzerenso Paulo akavalo kuti akwerepo, ndipo mukamufikitse bwino kwa Felikisi, bwanamkubwa.”
25
Tsono adalemba kalata iyi:
26
“Ine Klaudio Lisiasi, ndikupereka moni kwa inu olemekezeka, a Felikisi, bwanamkubwa.
27
Munthuyo Ayuda adaamugwira, ndipo anali pafupi kumupha. Nditamva kuti iyeyo ndi mfulu wachiroma, ndidapita ndi asilikali nkukamlanditsa.
28
Ndinkafuna kudziŵa chifukwa chimene ankamunenezera, choncho ndidapita naye ku Bwalo lao Lalikulu lamilandu.
29
Ndidapeza kuti ankamneneza chifukwa cha nkhani yokhudza Malamulo ao, koma osati mlandu womuphera kapena womuponyera m'ndende.
30
Tsono popeza kuti ndamva kuti pali chiwembu chimene ampanganirana munthuyu, ndamtumiza kwa inu msanga. Ndauza omnenezawo kuti adzanene mau ao kwa inu.”
31
Pamenepo asilikali aja adatenga Paulo monga momwe adaaŵalamulira, napita naye ku Antipatri usiku.
32
M'maŵa mwake iwo adabwerera ku linga la asilikali, nasiya okwera pa kavalo aja kuti apitirire ndi Paulo.
33
Iwo aja atafika ku Kesareya, adapereka kalata ija kwa bwanamkubwa, naperekanso Paulo m'manja mwake.
34
Bwanamkubwa uja ataŵerenga kalatayo, adafunsa Paulo za dera kumene ankachokera. Pamene adamva kuti ngwochokera ku Silisiya,
35
adamuuza kuti, “Ndidzamva mlandu wako akadzabwera okunenezawo.” Atatero adalamula kuti abamulondera ku nyumba ya mfumu Herode.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28