bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 11
Acts 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 12 →
1
Atumwi aja, ndiponso abale onse amene anali ku Yudeya, adamva kuti anthu a mitundu ina nawonso alandira mau a Mulungu.
2
Tsono pamene Petro adabwera ku Yerusalemu, a m'gulu lolimbikira za kuumbala adatsutsana naye.
3
Iwo adati, “Inu mudaloŵa m'nyumba ya anthu osaumbalidwa, nkudya nawo pamodzi.”
4
Apo Petro adayamba kuŵafotokozera mwatsatanetsatane zimene zidachitika. Adati,
5
“Ine ndinkapemphera m'mudzi wa Yopa. Ndidaachita ngati kukomoka, ndiye ndidaona ngati kutulo chinthu china chikutsika pansi kuchokera kumwamba. Chinkaoneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa nsonga zake zinai, ndipo chidafika pamene panali ineyo.
6
Nditachipenyetsetsa, ndidaonamo nyama zoŵeta ndi zakuthengo ndiponso zokwaŵa ndi mbalame zamumlengalenga.
7
Tsono ndidamva mau ondiwuza kuti, ‘Petro dzuka, ipha, udye.’
8
Koma ine ndidati, ‘Iyai pepani Ambuye, ine ndi kale lonse chinthu chosayera kapena chonyansa sichinaloŵepo pakamwa pangapa.’
9
Koma mau ochokera kumwamba aja adanenanso kachiŵiri kuti, ‘Zimene Mulungu waziyeretsa, iwe usati nzosayera.’
10
Zimenezi zidachitika katatu, ndipo zonsezo zinatengedwa kupitanso kumwamba.
11
Nthaŵi yomweyo kudafika anthu atatu kunyumba kumene ndinkakhala. Adaatumidwa kwa ine kuchokera ku Kesareya.
12
Mzimu Woyera anali atandiwuza kuti ndisakayike konse, koma ndipite nawo. Abale asanu ndi mmodzi aŵa nawonso adandiperekeza, ndipo tidakaloŵa m'nyumba ya Kornelio.
13
Iyeyo adatisimbira za m'mene adaaonera mngelo ataimirira m'nyumba mwake nkumuuza kuti, ‘Tuma anthu ku Yopa kuti akaitane Simoni, wotchedwa Petro.
14
Iyeyo adzakuuza mau amene iwe udzapulumuka nawo, ndiponso onse a m'banja mwako.’
15
Tsono pamene ndidayamba kulankhula, Mzimu Woyera adaŵatsikira iwowo, monga momwe adaatitsikiranso ife poyamba paja.
16
Pamenepo ndidakumbukira mau aja amene adaalankhula Ambuye akuti, ‘Yohane adabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.’
17
Tsono ngati Mulungu adaŵapatsa iwowo mphatso yomweyo imene adapatsa ifeyo pamene tidakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, nanga ine ndine yani kuti ndikadatha kumletsa Mulungu?”
18
Pamene otsutsana naye aja adamva zimenezi, adaleka mitsutsoyo. Adatamanda Mulungu adati, “Kodi kani! Ndiye kuti Mulungu wapatsadi ndi akunja omwe mwai woti atembenuke mtima ndi kulandira moyo!”
19
Okhulupirira Khristu aja, amene anali atabalalikana chifukwa cha mazunzo omwe adabuka pa nkhani ija ya Stefano, adafika mpaka ku Fenisiya, ku Kipro, ndiponso ku Antiokeya. Sankalalika mau kwa munthu wina aliyense, koma kwa Ayuda okha.
20
Koma pakati pao panali ena ochokera ku Kipro ndiponso ku Kirene. Ameneŵa adafika ku Antiokeya nayamba kulankhulanso ndi Agriki nkumaŵalalikira Uthenga Wabwino wonena za Ambuye Yesu.
21
Ambuye ankaŵalimbikitsa, mwakuti anthu ambiri adakhulupirira natembenukira kwa Ambuye.
22
Mpingo wa ku Yerusalemu utamva zimene zidachitikazo, udatuma Barnabasi ku Antiokeyako.
23
Pamene iye adafika kumeneko nkuwona m'mene Mulungu adaŵadalitsira, adakondwa, nalimbikitsa onsewo kuti atsimikize mtima kukhala okhulupirika kwa Ambuye.
24
Barnabasiyo anali munthu wolungama, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro. Choncho anthu ambirimbiri adakopeka nadzipereka kwa Ambuye.
25
Pamenepo Barnabasi adapita ku Tariso kukafuna Saulo.
26
Atampeza, adabwera naye ku Antiokeya. Iwo adakhala pamodzi mu mpingo umenewo chaka chathunthu, naphunzitsa anthu ambirimbiri. Ndi ku Antiokeya kumene ophunzira adayamba kutchedwa Akhristu.
27
Masiku amenewo kudafika aneneri ena ku Antiokeya ochokera ku Yerusalemu.
28
Mmodzi mwa iwo, dzina lake Agabu, adaimirira, ndipo ndi mphamvu za Mzimu Woyera adalosa kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lapansi. Njalayo idabweradi pa nthaŵi ya Klaudio.
29
Pamenepo Akhristu aja adatsimikiza zotumiza thandizo kwa abale okhala ku Yudeya, ndipo kuti aliyense atumize molingana ndi kupata kwake.
30
Zimenezi adachitadi, ndipo anatuma Barnabasi ndi Saulo kukapereka thandizolo kwa akulu a mpingo.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28