bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 21
Acts 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 22 →
1
Titalaŵirana nawo, tidachoka kumeneko m'chombo, ndipo tidayenda molunjika kukafika ku Kosi. M'maŵa mwake tidakafika ku Rode, ndipo kuchokera kumeneko tidakafika ku Patara.
2
Kumeneko tidapeza chombo chopita ku Fenisiya. Tsono tidaloŵamo nkunyamuka.
3
Tidaona chilumba cha Kipro, koma tidachisiya ku dzanja lamanzere nkupita ku Siriya. Tidakafika ku Tiro, popeza kuti chombo chinkayenera kukatsitsa katundu kumeneko.
4
Tidafunafuna ophunzira akumeneko, ndipo titaŵapeza, tidakhala nawo masiku asanu ndi aŵiri. Ndi chiwongolero cha Mzimu Woyera iwo aja adauza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu.
5
Koma pamene masiku athu aja adatha, tidachokako nkupitirira ulendo wathu. Onsewo, pamodzi ndi akazi ao ndi ana awo omwe, adatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Tidagwada pa mchenga m'mbali mwa njanja nkupemphera.
6
Ndipo titatsazikana, ife tidakaloŵa m'chombo, iwowo nkumabwerera kwao.
7
Tidapitirira ulendo wathu wochokera ku Tiro mpaka tidakafika ku Ptolemaisi. Kumeneko tidacheza pang'ono ndi abale, nkukhala nawo tsiku limodzi.
8
M'maŵa mwake tidanyamuka nkukafika ku Kesareya. Tidapita kunyumba kwa mlaliki Filipo, mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi aŵiri aja, ndipo tidakhala kunyumba kwakeko.
9
Iyeyo anali ndi ana aakazi anai osakwatiwa, amene ankalalika uthenga wa Mulungu.
10
Ife tili kumeneko masiku angapo, kudabwera mneneri wina kuchokera ku Yudeya, dzina lake Agabu.
11
Iyeyo adadza kwa ife, ali ndi lamba wa Paulo. Tsono adadzimanga mapazi ndi manja nati, “Mzimu Woyera akuti, ‘Mwiniwake lamba uyu Ayuda adzammanga chomwechi ku Yerusalemu, ndi kumpereka m'manja mwa akunja.’ ”
12
Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi athu akumeneko tidampemphha Paulo kuti asapite ku Yerusalemu.
13
Koma iye adati, “Bwanji mukulira ndi kufuna kunditayitsa mtima? Inetu ndili wokonzeka kumangidwa, ngakhalenso kukafera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.”
14
Tsono popeza kuti adaatikanika ndithu, tidangomuleka nkunena kuti, “Zichitike zimene Ambuye akufuna.”
15
Masiku athu okhala kumeneko atatha, tidakonza ulendo wathu ndipo tidapita ku Yerusalemu,
16
Ophunzira ena a ku Kesareya nawonso adatsagana nafe. Adakatitula kunyumba kwa munthu wina, dzina lake Mnasoni, kumene adaakonza kuti tizikakhala. Iyeyu anali wa ku Kipro, ndipo anali wophunzira wakalekale.
17
Titafika ku Yerusalemu, abale adatilandira ndi chimwemwe.
18
M'maŵa mwake Paulo adatitenga kupita kwa Yakobe. Akuluampingo onse anali kumeneko.
19
Atalonjerana nawo, Paulo adaŵafotokozera mwatsatanetsatane zonse zimene Mulungu adaachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.
20
Pamene iwo adamva zimenezi, adayamika Mulungu. Ndipo adauza Paulo kuti, “Inu mbale wathu, mukuwona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene asanduka okhulupirira. Onsewo ngokhulupirika kwambiri pa kutsata Malamulo a Mose.
21
Anthu aŵauza za inu kuti Ayuda onse okhala ku maiko achilendo, inu mumaŵaphunzitsa kuti alekane nawo Malamulowo. Akutinso mumaŵaphunzitsa kuti asamaumbale ana ao kapena kusamala miyambo yachiyuda.
22
Tsono pamenepa titani? Kumva adzamva ndithu kuti mwafika.
23
Ndiye inu, muchite zimene tikuuzeni ife. Tili ndi amuna anai pano amene adachita lumbiro kwa Mulungu.
24
Muŵatenge ndipo muchite nawo mwambo wakudziyeretsa. Tsono muŵalipirire zoti apereke ku Nyumba ya Mulungu kuti amete tsitsi lao. Mukatero, anthu onse adzadziŵa kuti si zoona zimene anthu adaŵauza za inu, koma kuti inu mumasamala ndithu Malamulo a Mose.
25
Koma kunena za anthu a mitundu ina amene adasanduka okhulupirira, ife taŵalembera kalata yoŵauza zimene tidavomerezana: kuti asamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe ku mafano, asamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso asamachite dama.”
26
Pamenepo Paulo adaŵatenga anthu anai aja, ndipo m'maŵa mwake adachita nawo mwambo wakudziyeretsa. Iyeyo adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu nakadziŵitsa ansembe za tsiku loti aliyense mwa iwo adzamperekere nsembe, atatha masiku akudziperekawo.
27
Atatha masiku asanu ndi aŵiri aja, Ayuda ochokera ku Asiya adaona Paulo m'Nyumba ya Mulungu. Adautsa mitima ya anthu onse, namgwira.
28
Tsono iwo adafuula kuti, “Inu Aisraele, tithandizeni! Ndi uyutu munthu uja amene akuphunzitsa anthu ponseponse zonyoza mtundu wathu, Malamulo a Mose ndiponso malo ano. Kuwonjezera apo waloŵetsanso akunja m'Nyumba ya Mulungu muno, ndi kudetsa malo athu opatulikaŵa.”
29
Adanena zimenezi chifukwa anali ataona Trofimo wa ku Efeso ali ndi Paulo mumzindamo, ndiye iwo ankaganiza kuti Paulo ndiye adaamloŵetsa m'Nyumba ya Mulungu.
30
Tsono mumzinda monse mudaloŵa chisokonezo ndipo anthu onse adathamangira pamodzi namgwira Pauloyo. Adamkokera kunja kwa Nyumba ya Mulungu, nkutseka pa makomo nthaŵi yomweyo.
31
Pamene anthu aja ankafuna kupha Paulo, mkulu wa gulu lonse la asilikali achiroma adalandira mau akuti mu mzinda wonse wa Yerusalemu muli chipolowe.
32
Pompo iye adatenga asilikali ndi atsogoleri a magulu a asilikali, nathamangira anthu aja. Pamene anthuwo adaona mkulu wa asilikaliyo ndi asilikali aja, adaleka kummenya Paulo.
33
Pamenepo mkulu wa asilikali uja adafika nagwira Paulo, nkulamula kuti ammange ndi maunyolo aŵiri. Kenaka adafunsa kuti, “Kodi munthuyu ndani? Ndipo watani kodi?”
34
Koma pakati pa anthuwo ena adayamba kufuula zina, ena zina. Chifukwa cha phokosolo mkulu wa asilikali uja sadathe kudziŵa kuti zoona zenizeni nziti. Choncho adalamula kuti amtenge Pauloyo apite naye ku linga la asilikali.
35
Tsono pamene adafika pa makwerero a kulingako, asilikali aja adachita kumnyamula, chifukwa chakuti anthuwo adaalusa zedi.
36
Onsewo ankaŵatsatira akufuula kuti, “Mupheni basi.”
37
Ali pafupi kuloŵa naye m'lingamo, Paulo adapempha mkulu wa asilikali uja kuti, “Kodi mungandilole kuti ndikuuzeni kanthu?” Iye adati, “Kani umalankhula Chigriki?
38
Tsono ndiye kuti sindiwe Mwejipito uja udautsa chipolowe masiku apitawo nkutsogolera zigaŵenga zikwi zinai kupita nazo ku chipululu?”
39
Paulo adayankha kuti, “Inetu ndine Myuda, nzika ya ku Tariso, mzinda wotchuka wa ku Silisiya. Ndikukupemphani tsono, mundilole kuti ndilankhule nawo anthuŵa.”
40
Adamloladi, ndipo Paulo adaima pamakwerero paja, naweyula dzanja kuti anthuwo akhale chete. Pamene onse adakhala chete, Paulo adayamba kulankhula nawo pa Chiyuda. Adati,
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28