bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 27
Acts 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 28 →
1
Zitatsimikizika kuti tiyenera kupita ku Italiya pa chombo, adampereka Paulo pamodzi ndi akaidi ena kwa mtsogoleri wa asilikali, dzina lake Julio, wa gulu la asilikali lochedwa gulu la Augusto.
2
Tidakwera chombo chochokera ku Adramitio chimene chinali chokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tidanyamuka. Aristariko, Mmasedoni wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe.
3
M'maŵa mwake tidafika ku Sidoni, ndipo Julio adakomera mtima Paulo, namlola kupita kwa abwenzi ake kuti akamsamale.
4
Kuchokera kumeneko tidadzera kumpoto kwa chilumba cha Kipro chifukwa mphepo inkawomba mopenyana nafe.
5
Tidawoloka nyanja mbali ya ku Silisiya ndi Pamfiliya nkumafika ku Mira, mzinda wa ku Likiya.
6
Kumeneko mtsogoleri wa asilikali uja adapezako chombo chochokera ku Aleksandriya chimene chinkapita ku Italiya, ndipo adatikweza m'chombo chimenechi.
7
Tidayenda pang'onopang'ono pa masiku angapo, nkukafika pafupi ndi Kinido movutikira. Tsono popeza kuti mphepo idaativuta zedi, tidalephera kupitirira ulendo wathu molunjika, choncho tidadzera kumwera kwa chilumba cha Krete, titabzola Salimone.
8
Tidayenda movutikira m'mbali mwa chilumbacho, nkukafika ku malo ena otchedwa Madooko Okoma, pafupi ndi mzinda wa Lasea.
9
Nthaŵi yaikulu idapita, ndipo ngakhale nthaŵi yosala zakudya inali itapita kale. Nthaŵiyo ulendo wapamadzi unali woopsa. Pamenepo Paulo adaŵachenjeza kuti,
10
“Abale, ine ndikuwona kuti pa ulendowu zinthu zambiri zidzawonongeka ndi kutayika, osati katundu yekha ndi chombo ai, komanso moyo wathu.”
11
Koma mtsogoleri wa asilikali uja adamvera kapitao wa chombo ndiponso mwiniwake wa chombocho, osati mau a Paulo ai.
12
Tsono popeza kuti dooko silinali labwino kukhalako pa nthaŵi yachisanu, ambiri mwa iwo adafuna kuchokako, nayesa kuti angathe kukafika ku Fenikisi nkukakhala kumeneko pa nthaŵi yachisanu. Fenikisi linali dooko la ku Krete, loloza kumwera chakumadzulo, ndiponso kumpoto chakumadzulo.
13
Mphepo yakumwera itayamba kuwomba monyengerera, anthu aja adayesa kuti tsopano apeza mpata woti achite zimene ankafuna. Motero adanyamuka ulendo, nayenda m'mbali mwa chilumba chija cha Krete.
14
Koma posachedwa mphepo yamkuntho, yotchedwa Yurakulo, idayamba kuwomba kuchokera ku mtunda.
15
Idaomba chombo chija, ndiye popeza kuti sitidathe kuchiwongolera moyang'anana ndi mphepoyo, tidaigonjera nkungotengedwa nayo.
16
Tidafika pafupi ndi kachilumba kotchedwa Kauda, ku mbali yosawombapo mphepo. Kumeneko movutikira tidatha kuwongolera kabwato kokokedwa ndi chombo chija.
17
Kenaka adakweza kabwatoko pa chombo, ndipo pambuyo pake adakulunga chombocho ndi zingwe kuti achilimbitse. Tsono poopa kuti angakagunde ku mchenga wa ku Siriti, adatsitsa mathanga nalola kungotengedwa ndi mphepo.
18
Popeza kuti tinkavutika naye kwambiri namondweyo, m'maŵa mwake adayamba kutaya katundu m'madzi.
19
Ndipo pa tsiku lachitatu lake adataya m'nyanja ndi zipangizo za chombo zomwe.
20
Sitidaone dzuŵa kapena nyenyezi masiku ambiri, koma namondwe ankakalipabe, mpaka tonse tidaatayiratu chikhulupiriro chakuti tipulumuka.
21
Pa nthaŵi yaitali anthu aja sadadye kanthu. Tsono Paulo adaimirira pakati pao nati, “Abale, mukadamvera zija ndidaanena inezi, osachoka ku Krete, sibwenzi zinthu zitawonongeka nkutayika chotere.
22
Koma tsopano ndikukuuzani kuti mulimbe mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene atayike, koma chombo chokha ndiye chiwonongeke.
23
Usiku womwe wathawu kunandibwerera mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake, ndipo amene ndimamlemekeza.
24
Mngeloyo anandiwuza kuti, ‘Usachite mantha, Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Mfumu ya ku Roma. Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, walola kuti anzako onse aulendo akhale moyo.’
25
Ndiye inu, limbani mtima, pakuti ndikukhulupirira Mulungu, kuti zimene wandiwuzazi zidzachitikadi momwemo.
26
Koma tidzatsakamira pa chilumba china.”
27
Pakati pa usiku wa khumi ndi chinai, mphepo ikutikankhabe pa nyanja ya Adriya, antchito apachombo adaganiza kuti akuyandikira mtunda.
28
Tsono atayesa kuzama kwa nyanja, adapeza mamita 37. Atayenda pang'ono, adayesanso napeza mamita 27.
29
Poopa kuti chombo chingakatsakamire pa matanthwe, adatsitsira anangula anai m'nyanja kumbuyo kwa chombo. Kenaka ankangoyembekeza molakalaka kuti kuche.
30
Antchito apachombo aja ankafuna kuthaŵamo m'chombo muja. Choncho adatsitsira kabwato kaja pa madzi, nachita ngati akufuna kutsitsira anangula m'nyanja kutsogolo kwa chombo.
31
Apo Paulo adauza mtsogoleri wa asilikali uja, pamodzi ndi asilikali ake omwe kuti, “Ngati anthu aŵa sakhala m'chombo muno, ndithu inu simutha kupulumuka ai.”
32
Pamenepo asilikali aja adadula zingwe za kabwato kaja nakaleka kuti kagwe.
33
Kuli pafupi kucha, Paulo adaŵapempha onse aja kuti adyeko kanthu. Adaŵauza kuti, “Mwakhala masiku khumi ndi anai tsopano mitima ili m'malere, nthaŵi yonseyi osadya kapena kulaŵa kanthu.
34
Ndikukupemphani tsono mudye kanthu kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzataye ngakhale tsitsi limodzi la kumutu kwake.”
35
Atanena zimenezi, Paulo adatenga buledi, nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo adamnyema bulediyo nayamba kudya.
36
Pamenepo onse aja adalimba mtima, iwonso nkuyamba kudya.
37
Tonse pamodzi tinali anthu okwanira 276 m'chombomo.
38
Onse aja atadya nkukhuta, adapeputsa chombo pakutaya tirigu m'nyanja.
39
Kutacha, anthu sadazindikire mtundawo, koma adaona bondo la nyanja lamchenga. Tsono adaganiza kuti ngati nkotheka, akakocheze chombo kumeneko.
40
Choncho adataya anangula naŵasiya m'nyanja. Nthaŵi yomweyo adamasula zingwe zomangira nkhafi zoongolera, nakweza thanga lakutsogolo, kuti mphepo ikankhe chombo, ndipo adalunjika ku mtunda.
41
Koma chombo chija chidakatsakamira pa mchenga wobisika ndi madzi, ndipo chidaima. Mbali yakutsogolo ya chombocho idajima, kotero kuti sichidathe kuyendanso. Ndipo mbali yakumbuyo idaonongeka ndi mphamvu ya mafunde.
42
Asilikali aja adaganiza zakupha akaidi, kuwopa kuti ena mwa iwo angasambire kukafika ku mtunda nkuthaŵa.
43
Koma mtsogoleri wa asilikali uja adafuna kupulumutsa Paulo, motero adaŵaletsa. Adalamula kuti onse otha kusambira, adziponye m'madzi, asambire kuti akafike ku mtunda.
44
Otsalawo adaŵalamula kuti agwire matabwa kapena zina za chombo choswekacho. Motero onse adapulumuka nakafika kumtunda.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28