bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 15
Acts 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 16 →
1
Anthu ena ochokera ku Yudeya adabwera ku Antiokeya, namaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuumbala potsata mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.”
2
Koma Paulo ndi Barnabasi adatsutsana nawo kolimba. Tsono abale adapangana kuti Paulo ndi Barnabasi, ndi abale ena a ku Antiokeya, apite ku Yerusalemu kukakambirana ndi atumwi ndi akulu a mpingo za nkhaniyi.
3
Mpingo utaŵatuma, adadzera ku Fenisiya ndi Samariya akufotokoza za m'mene anthu osakhala Ayuda adatembenukira mtima. Mau ameneŵa adakondweretsa abale onse kwambiri.
4
Pamene adafika ku Yerusalemu, adalandiridwa ndi mpingo ndi atumwi ndi akulu a mpingo. Paulo ndi Barnabasi adaŵafotokozera ntchito zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo.
5
Koma okhulupirira ena amene kale anali a m'gulu la Afarisi, adaimirira nati, “Nkofunika kuti okhulupirira a mitundu ina aumbalidwe, ndiponso aŵalamule kuti azitsata Malamulo a Mose.”
6
Tsono atumwi ndi akulu a mpingo adasonkhana kuti aiwone bwino nkhaniyi.
7
Atakambirana nthaŵi yaitali, Petro adaimirira naŵauza kuti, “Abale anga, mukudziŵa kuti pa masiku oyamba aja Mulungu adandisankha ine pakati pa inu kuti ndilalike Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina, kuti amve ndi kukhulupirira.
8
Ndipo Mulungu amene amadziŵa mitima ya anthu, adaŵachitira umboni pakuŵapatsa Mzimu Woyera, monga adapatsira ifeyo.
9
Mulungu sadasiyanitse konse pakati pa ife ndi iwo, koma adayetsera mitima yao ndi chikhulupiriro chao.
10
Tsono mukumuyeseranji Mulungu pakuika m'khosi mwa ophunzirawo goli limene ngakhale makolo athu kapena ife tomwe tidalephera kulisenza?
11
Iyai, timakhulupirira kuti chopulumutsa iwowo, ndi ife tomwe, ndi kukoma mtima kwa Ambuye Yesu.”
12
Onse mumsonkhanomo adangoti chete nkumamvetsera Barnabasi ndi Paulo akufotokoza za m'mene Mulungu adachitira zizindikiro ndi zozizwitsa pakati pa akunja kudzera mwa iwowo.
13
Pamene iwo aja adatha kulankhula, Yakobe adati, “Abale anga, mundimvere.
14
Simoni wafotokoza za m'mene Mulungu pachiyambi pomwe adakumbukira anthu a mitundu ina, pa kupatula ena pakati pao kuti akhale anthu akeake.
15
Zimenezi zikuvomerezana ndi mau a aneneri. Paja kudalembedwa kuti,
16
“ ‘Zitatha zimenezi ndidzabwerera, ndidzamanganso nyumba ya Davide imene idagwa. Ndidzamanganso zopasuka zake, ndi kuikonzanso.
17
Ndidzachita choncho kuti anthu ena onse afunefune Ambuye, ndiye kuti, anthu a mitundu yonse amene amadziŵika ndi dzina langa.
18
Akutero ndi Chauta amene adaulula zimenezi kuyambira kalekale.’
19
“Nchifukwa chake ine ndikuti, tisaŵavute anthu a mitundu ina amene akutembenuka mtima nkumatsata Mulungu.
20
Koma tiŵalembere kalata kuŵauza kuti asamadye zimene zili zosayera chifukwa zidaperekedwa kwa mafano. Alewe dama, ndipo asamadye nyama zochita kupotola, alewenso magazi.
21
Paja kuyambira kalekale mu mzinda uliwonse muli anthu ophunzitsa Malamulo a Mose, ndipo amaŵerenga mau ake m'nyumba zamapemphero pa tsiku la Sabata lililonse.”
22
Pamenepo atumwi ndi akulu a mpingo, pamodzi ndi mpingo wonse, adavomerezana kusankha anthu ena pakati pao kuti aŵatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Barnabasi. Adasankha Yudasi, wotchedwa Barsabasi, ndiponso Silasi, anthu aulemu pakati pa abale,
23
kuti akapereke kalata yonena kuti, “Abale, ife atumwi pamodzi ndi akulu a mpingo tikuti moni inu abale a ku Antiokeya, a ku Siriya, ndi a ku Silisiya, amene simuli Ayuda.
24
Tamva kuti anthu ena ochokera m'gulu lathu akhala akukuvutani ndi kukusokonezani maganizo. Amenewo sitidaŵatume ndife ai.
25
Tsono titasonkhana, tavomerezana kusankha anthu ndi kuŵatuma kwa inu. Adzabwera pamodzi ndi okondedwa athu Barnabasi ndi Paulo.
26
Amene adadzipereka kuti atumikire Ambuye athu Yesu Khristu.
27
Nchifukwa chake tatuma Yudasi ndi Silasi kuti adzakufotokozereni pakamwa zimene talemba m'kalatayi.
28
Maganizo athu agwirizana ndi a Mzimu Woyera kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zofunika zokhazi:
29
musamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe kwa mafano, musamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso musachite dama. Mukalewa zimenezi, mudzachita bwino. Tsalani bwino.”
30
Tsono otumidwa aja adanyamuka nakafika ku Antiokeya. Adasonkhanitsa mpingo wonse napereka kalata ija.
31
Pamene iwo adaiŵerenga, adakondwa chifukwa cha mau ake oŵalimbikitsa.
32
Yudasi ndi Silasi analinso alaliki, ndipo adalimbikitsa abale aja ndi mau ambiri naŵakhazikitsa mtima.
33
Atakhala kumeneko nthaŵi ndithu, abale aja adaŵalola mwamtendere kuti abwerere kwa amene adaaŵatuma. [
34
Koma Silasi adatsimikiza kuti akhalire.]
35
Paulo ndi Barnabasi adakhalabe ku Antiokeya, akuphunzitsa ndi kulalika mau a Ambuye pamodzi ndi anthu ena ambiri.
36
Patapita masiku angapo, Paulo adauza Barnabasi kuti, “Tiyeni tibwerere tizinka tiyendera abale ku mzinda uliwonse kumene tidalalikako mau a Ambuye.”
37
Barnabasi adafuna kutenganso Yohane wotchedwa Marko, kuti apite nao.
38
Koma Paulo adaganiza kuti sibwino kumtenganso, chifukwa paja iye adaaŵasiya ku Pamfiliya, osapita nao ku ntchito.
39
Pamenepo iwo adakangana kwambiri, kotero kuti adapatukana. Barnabasi adamtenga Marko uja naloŵa m'chombo kupita ku Kipro.
40
Koma Paulo adasankhula Silasi, ndipo abale ataŵapempherera kuti Ambuye aŵadalitse, adanyamuka.
41
Adadzera ku Siriya ndi ku Silisiya akulimbikitsa anthu amumpingo.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
Recommended Reading
Commentary
Acts Commentaries
→
Devotional
Acts Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→