bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 20
Acts 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 21 →
1
Phokoso lija litatha, Paulo adaitanitsa ophunzira aja, naŵalimbitsa mtima. Ndipo atatsazikana nawo, adachoka napita ku Masedoniya.
2
Adayendera madera a komweko nalimbitsa mtima anthu ndi mau ambiri. Pambuyo pake adapita ku Grisi,
3
nakakhalako miyezi itatu. Pamene anali pafupi kupita ku Siriya pa chombo, Ayuda adamchita chiwembu. Tsono iye adatsimikiza zodzera ku Masedoniya.
4
Adamperekeza ndi Sopatere, mwana wa Piro, wa ku Berea; Aristariko ndi Sekundo a ku Tesalonika; Gayo wa ku Deribe; Timoteo; ndi Tikiko ndi Trofimo a ku Asiya.
5
Iwoŵa adatsogola nakatidikira ku Troasi.
6
Koma ife tidayenda pa chombo kuchokera ku Filipi, itatha Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa. Ndipo patapita masiku asanu, tidakumana nawo ku Troasi. Kumeneko tidakhalako masiku asanu ndi aŵiri.
7
Pa tsiku loyamba la sabata, tidasonkhana kuti tidye Mgonero, ndipo Paulo ankakamba ndi anthu. Popeza kuti ankayembekeza kupita m'maŵa mwake, adapitiriza kulankhula mpaka pakati pa usiku.
8
M'chipinda cham'mwamba chimene tidaasonkhanamo munali nyale zambiri.
9
Mnyamata wina, dzina lake Yutiko, adaakhala pa windo. Tsono Paulo akukambabe ndi anthu aja, Yutikoyo ankaodzera kwambiri, mpaka adagona tulo ndithu, nagwa pansi kuchokera pa nyumba yam'mwamba. Ndipo adamtola ali wakufa.
10
Pamenepo Paulo adatsika, nadziponya pa mnyamatayo nkumufungatira nati, “Musavutike, ali moyo.”
11
Kenaka Paulo adakweranso, nakanyema nao mkate, nkudya nao. Pambuyo pake adapitiriza kulankhula nao nthaŵi yaitali, nangochoka kutacha kale.
12
Anthu aja adatenga mnyamata uja ali moyo, ndipo onse adasangalala kwambiri.
13
Ife tidatsogola nkukakwera chombo kupita ku Aso, kumene tinkayembekeza kukatengako Paulo. Iye adaakonza motero, chifukwa adaafuna kudzera pa mtunda.
14
Pamene iye adakumana nafe ku Aso, adakwera nafe m'chombomo, ndipo tidakafika ku Mitilene.
15
Tidachokanso kumeneko m'chombo, ndipo m'maŵa mwake tidakafika pafupi ndi Kiyo. M'maŵa mwakenso tidawolokera ku Samo, ndipo mkucha wake tidakafika ku Mileto.
16
Paulo anali atatsimikiza zolambalala Efeso, kuwopa kutaya nthaŵi ku dziko la Asiya. Ankafulumira kuti ngati nkotheka akakhale ali ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste.
17
Paulo ali ku Mileto, adatumiza mau ku Efeso kuitana akulu a mpingo.
18
Iwo atafika, adaŵauza kuti, “Inu nomwe mukudziŵa m'mene ndidakhalira nanu masiku onse, kuyambira tsiku loyamba lija ndidafika ku Asiya.
19
Ndinkatumikira Ambuye modzichepetsa kwenikweni, pakati pa chisoni ndi zovuta zimene zidandigwera chifukwa cha ziwembu za Ayuda.
20
Mukudziŵa kuti sindidakubisireni kanthu kalikonse koti nkukuthandizani. Ndidakulalikirani ndi kukuphunzitsani poyera ndiponso m'nyumba zanu.
21
Ayuda ndi Agriki omwe ndidaŵapempha kolimba kuti atembenukire kwa Mulungu molapa, ndi kumakhulupirira Ambuye athu Yesu.
22
“Ndipo tsopano, onani ndikupita ku Yerusalemu, popeza kuti Mzimu Woyera akundilamula. Zimene zikandigwere kumeneko sindikuzidziŵa konse.
23
Chokhachi ndikudziŵa kuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mazunzo zikundidikira.
24
Koma sindilabada konse za moyo wanga, ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malinga ndikatsirize ntchito yanga, ndi utumiki umene Ambuye Yesu adandipatsa, ndiye kuti kulalika poyera Uthenga Wabwino wonena za kukoma mtima kwa Mulungu.
25
“Tsopano ndikudziŵa kuti inu nonse amene ndidakuyenderani kumakulalikirani za ufumu wa Mulungu, simudzaonanso nkhope yanga ai.
26
Nchifukwa chake ndikukuuzani monenetsa lero, kuti ngati ena mwa inu atayike, izo nzao, ine ndilibepo mlandu.
27
Pajatu sindidakubisireni kanthu ai, koma ndidakulalikirani zonse zimene Mulungu afuna.
28
Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao.
29
Ndikudziŵa kuti ndikadzachoka ine, padzaloŵa mimbulu yoopsa pakati panu, imene siidzalekerera nkhosazo.
30
Ngakhale pakati pa inu nomwe, padzauka ena olankhula zonama nkumakopa ophunzira kuti aŵatsate.
31
Ndiye inu khalani maso. Kumbukirani kuti pa zaka zitatu usana ndi usiku sindidaleke kulangiza aliyense mwa inu ndi misozi.
32
“Choncho tsopano ndikukuikani m'manja mwa Mulungu, mau ake oonetsa kukoma mtima kwake akusungeni bwino. Mauwo ali ndi mphamvu zakukulitsa mpingo, ndi kukupatsani madalitso onse aja amene Mulungu akusungira anthu ake.
33
Sindidasirire ndalama kapena zovala za munthu aliyense ai.
34
Inu nomwe mukudziŵa kuti manja angaŵa adagwira ntchito kuti ndipeze zimene ine ndi anzanga tinkasoŵa.
35
Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ”
36
Paulo atanena zimenezi, adagwada pansi napemphera nawo pamodzi ena onse aja.
37
Onsewo adalira kwambiri. Adamkumbatira Pauloyo namumpsompsona polaŵirana naye.
38
Makamaka adachita chisoni chifukwa cha mau ake aja onena kuti iwo sadzaonanso nkhope yake. Pambuyo pake adamperekeza kuchombo.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28