bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 22
Acts 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 23 →
1
“Inu abale anga ndi inu akuluakulu, mvereni ndiyankhe tsopano zimene akundinenezazi.”
2
Pamene iwo adamumva akulankhula nawo pa Chiyuda, adakhala chete kopambana. Tsono Paulo anati,
3
“Inetu ndiye Myuda mbadwa ya ku Tariso, mzinda wa ku Silisiya, koma ndidaleredwa mu mzinda wa Yerusalemu mom'muno. Gamaliele ndiye anali mphunzitsi wanga amene adandiphunzitsa kwenikweni kusunga Malamulo a makolo athu. Ndipo ndinkalimbikira kwambiri pa za Mulungu, monga momwe mukuchitira nonsenu lero lino.
4
Ndinkazunza anthu otsata Njira Yatsopanoyi, mpaka kumaŵapha. Ndinkaŵagwira anthuwo amuna ndi akazi omwe, nkumaŵamangitsa.
5
Mkulu wa ansembe onse ndi onse a m'Bungwe la akuluakulu a Ayuda angathe kundivomereza. Iwowo adaandipatsa makalata opita nawo kwa abale athu achiyuda ku Damasiko. Tsono ndidapita komweko kuti ndikaŵagwire anthu ameneŵa, ndi kubwera nawo ku Yerusalemu ali omangidwa, kuti adzalangidwe.”
6
“Pamene ndinali pa ulendowo ndi kuyandikira Damasiko, nthaŵi ili ngati 12 koloko yamasana, mwadzidzidzi kuŵala kwakukulu kochokera kumwamba kudandizinga.
7
Ndidagwa pansi kenaka ndidamva mau onena kuti, ‘Saulo, Saulo, ukundizunziranji?’
8
Ine ndidafunsa kuti, ‘Ndinu yani, Ambuye?’ Ndipo iwo adati, ‘Ine ndine Yesu wa ku Nazarete, amene iwe ukumzunza.’
9
Anzanga apaulendo adaakuwona kuŵalako, koma mau a amene ankalankhula naneyo sadaŵamve.
10
Tsono ine ndidafunsa kuti, ‘Ndichite chiyani, Ambuye?’ Ndipo Ambuye adati. ‘Dzuka, pita ku Damasiko, kumeneko akakuuza zonse zimene Mulungu wakonza kuti ukachite.’
11
Sindidathe kupenyanso chifukwa cha kuŵala kwakukulu kuja, nchifukwa chake anzanga aja adachita kundigwira pa dzanja nkumanditsogolera mpaka kukaloŵa m'Damasiko.
12
“Kumeneko kunali munthu wina, dzina lake Ananiya. Anali munthu woopa Mulungu ndi wosamala Malamulo athu, ndipo Ayuda onse akumeneko ankamutama.
13
Iyeyo adafika nadzaimirira pafupi nane, nkundiwuza kuti, ‘Mbale wanga Saulo, yambanso kupenya.’ Nthaŵi yomweyo ndidayambadi kupenya ndipo iyeyo ndidamuwona.
14
Tsono adandiwuza kuti, ‘Mulungu wa makolo athu adakusankha kuti udziŵe zimene Iye akufuna, uwone Wolungama uja, ndipo umve mau ake olankhula nawe.
15
Pakuti udzamchitira umboni kwa anthu onse pa zimene waziwona ndi kuzimva.
16
Nanga tsono ukuchedweranji? Dzuka ndi kutama dzina lake mopemba, ubatizidwe ndi kusambitsidwa kuti machimo ako achoke.’ ”
17
“Tsono ndidabwerera ku Yerusalemu, ndipo pamene ndinkapemphera m'Nyumba ya Mulungu, ndidachita ngati ndakomoka.
18
Ndidaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira, tuluka msangamsanga m'Yerusalemu muno, chifukwa anthuŵa sadzauvomera umboni wako wonena za Ine.’
19
Ine ndidati, ‘Zoonadi Ambuye, chifukwa iwo omwe akudziŵa kuti ine ndinkapita ku nyumba iliyonse yamapemphero kukaŵagwira ndi kuŵaponya m'ndende, nkumaŵakwapula onse okhulupirira Inu.
20
Pamene ankapha Stefano, mboni yanu, inenso ndinali pomwepo. Ndinkavomerezana nawo, ndipo ndinkasunga ndine zovala za amene ankamuphawo.’
21
Apo Ambuye adandiwuza kuti, ‘Nyamuka, chifukwa Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.’ ”
22
Mpaka apa anthu aja ankamvetsera bwinobwino mau a Paulo. Koma pamene adadzatchula mau otsirizaŵa, iwo adayamba kufuula kuti, “Munthu wotere koma kungokonzeratu. Sayeneranso kukhala moyo.”
23
Iwowo ankafuula nkumazunguza malaya ao, namawaza fumbi kumwamba.
24
Nthaŵi yomweyo mkulu wa asilikali uja adalamula kuti aloŵe naye Paulo m'linga la asilikali lija. Adaŵauza kuti amkwapule, kuti iyeyo aulule chifukwa chimene anthu aja ankamukuwizira chotere.
25
Pamenepo padaaimirira mtsogoleri wa gulu la asilikali 100. Tsono asilikali ake atamanga Paulo kuti amkwapule, Pauloyo adafunsa kuti, “Kodi malamulo anu amalola kukwapula mfulu yachiroma musanazenge nkomwe mlandu wake?”
26
Pamene mtsogoleriyo adamva zimenezi, adapita kwa mkulu wa asilikali uja namufunsa kuti, “Kodi inu mukuti mutani? Munthu ujatu ndi mfulu yachiroma.”
27
Apo mkuloyo adadzafunsa Paulo kuti, “Kodi ati iwe ndiwe mfulu yachiroma?” Iye adati, “Inde.”
28
Tsono mkulu uja adamuuza kuti, “Ine ndidachita chogula ufulu wangawu ndi ndalama zambiri.” Paulo adati, “Koma ine wangawu ndidachita chobadwa nawo.”
29
Pompo asilikali aja amene adaati afunse Paulo mafunso, adamleka. Mkulu ujanso adachita mantha atazindikira kuti adaamanga munthu amene ali mfulu yachiroma.
30
Mkulu wa asilikali uja adaafuna kudziŵa kwenikweni chifukwa chimene Ayuda adaadzanenezera Paulo. Choncho m'maŵa mwake adammasula, nalamula kuti akulu a ansembe ndi onse a pa Bwalo Lalikulu lamilandu la Ayuda asonkhane. Kenaka adabwera ndi Paulo namuimika pakati pao.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28