bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 2
Acts 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 3 →
1
Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m'nyumba imodzi.
2
Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo.
3
Ndipo adaona ngati timalaŵi ta moto tooneka ngati malilime tikugaŵikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake.
4
Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.
5
Tsono, m'Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi.
6
Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankaŵamva akulankhula chilankhulo chake.
7
Adadabwa, nathedwa nzeru ndipo adati, “Kodi onse akulankhulaŵa, si Agalileya?
8
Nanga bwanji aliyense mwa ife akuŵamva akulankhula chilankhulo chakwao?
9
Ena mwa ife ndi Aparti ndi Amedi ndi Aelami, ena ndi okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya,
10
ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma,
11
ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuŵamva anthuŵa akulankhula m'zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.”
12
Onse adazizwa ndi kuthedwa nzeru, ndipo adayamba kufunsana kuti, “Kodi chimenechi nchiyani?”
13
Koma ena ankangoseka nkumati, “Aledzera vinyo watsopano.”
14
Koma Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Ayuda, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu kuno, tamverani ndipo mumvetsetse bwino mau anga.
15
Anthuŵa sadaledzere ai, monga mukuganizira inu, pakuti nthaŵi idakali 9 koloko m'maŵa.
16
Koma zimenezi ndi zomwe mneneri Yowele adalosa kuti,
17
“ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto.
18
Ndithu, pa masiku amenewo ndidzaika Mzimu wanga ngakhale mwa akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndipo azidzalalika za Mulungu.
19
Ndidzachita zozizwitsa ku thambo lakumwamba, ndipo pansi pano zizindikiro izi: magazi, moto ndi utsi watolotolo.
20
Dzuŵa lidzangoti bii ngati mdima ndipo mwezi udzangoti psuu ngati magazi, lisanafike tsiku la Ambuye Mulungu lalikulu ndi laulemerero.
21
Pamenepo aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba, adzapulumuka.’
22
“Inu Aisraele mverani mau aŵa. Yesu wa ku Nazarete anali munthu amene Mulungu adamtuma kwa inu. Mulungu adakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zozizwitsa ndi zizindikiro zimene ankachita kudzera mwa Iyeyo pakati panu, monga mukudziŵa.
23
Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m'mene Iye amadziŵiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda.
24
Koma Mulungu adammasula ku zoŵaŵa za imfa, namuukitsa kwa akufa, chifukwa kunali kosatheka kuti agonjetsedwe ndi imfa.
25
“Paja Davide ponena za Iye adati, ‘Ndinkaona Ambuye Mulungu pamaso panga nthaŵi zonse, pakuti amakhala ku dzanja langa lamanja kuti ndingagwedezeke.
26
Nchifukwa chake mtima wanga udakondwa, ndipo ndinkalankhula mosangalala. Ndithu, ngakhale thupi langa lomwe lidzapumula m'manda,
27
ndikhulupirira kuti simudzandisiya ku Malo a anthu akufa, kapena kulekerera Woyera wanu kuti aole.
28
Mudandidziŵitsa njira zopita ku moyo, ndipo mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
29
“Abale anga, ndingathe kulankhula nanu monenetsa za kholo lathu Davide. Iye adamwalira, naikidwa m'manda, ndipo manda ake alipo mpaka pano.
30
Paja iye anali mneneri, ndipo ankadziŵa zimene Mulungu adamlonjeza molumbira zakuti mmodzi mwa zidzukulu zake ndiye adzaloŵe ufumu wake.
31
Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti, “ ‘Iye sadasiyidwe ku Malo a anthu akufa, ndipo thupi lake silidaole.’
32
Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi.
33
Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira.
34
Pajatu Davide sadakwere kupita Kumwamba, koma iye yemwe adati, “ ‘Ambuye adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja
35
mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’
36
“Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.”
37
Pamene anthu aja anamva zimenezi, zidaŵalasa mtima, ndipo adafunsa Petro ndi atumwi ena aja kuti, “Abale, tsono ifeyo tichite chiyani?”
38
Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
39
Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.”
40
Petro adalankhulanso mau ena ambiri, naŵachenjeza kuti, “Muthaŵe maganizo opotoka a mbadwo woipa uno.”
41
Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao.
42
Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.
43
Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita.
44
Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao.
45
Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.
46
Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu.
47
Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28