bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Acts 25
Acts 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 26 →
1
Fesito adayamba ntchito yoweruza m'chigawo chake, ndipo patapita masiku atatu, adapita ku Yerusalemu kuchokera ku Kesareya.
2
Kumeneko akulu a ansembe ndiponso atsogoleri a Ayuda adamufotokozera za mlandu wa Paulo. Iwo adapempha Fesito
3
kuti aŵakomere mtima pakumtumiza Paulo ku Yerusalemu. Adaatero chifukwa anali atapangana zomulalira Paulo kuti amuphe pa njira.
4
Fesito adaŵauza kuti, “Paulo akusungidwa m'ndende ku Kesareya, ndipo ine ndipita komweko posachedwa.
5
Tsono atsogoleri anu apite nane pamodzi kumeneko, kuti akamneneze munthuyo ngatidi iye adachitapo cholakwa.”
6
Fesito atakhala pakati pao ku Yerusalemu kuja masiku osapitirira asanu ndi atatu kapena khumi, adapita ku Kesareya. M'maŵa mwake adakhala pa mpando woweruzira milandu, naitanitsa Paulo kuti abwere pamaso pake.
7
Paulo atafika, Ayuda amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu aja adamzinga, nayamba kumneneza zinthu zoopsa zambiri, zimene iwo sadathe kuzitsimikiza.
8
Paulo poyankha zomnenezazo adati, “Ine sindidalakwirepo Malamulo a Ayuda, kapena Nyumba ya Mulungu, kapenanso Mfumu ya ku Roma.”
9
Fesito pofuna kuchita mkomya kwa Ayuda, adafunsa Paulo kuti, “Kodi ungakonde kupita ku Yerusalemu kuti mlandu wakowu ukazengedwere kumeneko pamaso panga?”
10
Koma Paulo adati, “Ine ndaima pa bwalo lamilandu la Mfumu ya ku Roma, ndiko kumene ayenera kundiweruza. Ayudaŵa ine sindidaŵalakwire chilichonse, monga inu mukudziŵa bwino.
11
Ngati ndili wolakwa, ndipo ngati ndachita kanthu koyenera kuti ndiphedwe, sindikukana kuphedwa ai. Koma ngati zimene aŵa akundinenezazi si zoona, palibe munthu angathe kundipereka kwa iwo. Ine ndikupempha kuti mlandu wangawu ndikagwade kwa Mfumu ya ku Roma.”
12
Tsono Fesito atakambirana ndi abwalo ake, adati, “Wachita apilo kwa Mfumu ya ku Roma. Chabwino, udzapitadi ku Romako kwa Mfumu yaikulu.”
13
Patapita masiku, mfumu Agripa pamodzi ndi mkazi wake Berenise adadza ku Kesareya kudzalonjera Fesito.
14
Atakhala kumeneko masiku angapo, Fesitoyo adafotokozera mfumoyo za mlandu wa Paulo. Adati, “Kuli munthu wina kuno amene Felikisi adamsiya m'ndende.
15
Pamene ndinali ku Yerusalemu, akulu a ansembe pamodzi ndi atsogoleri a Ayuda adandifotokozera za iye, nandipempha kuti ndizenge mlandu wake ndi kugamula kuti ngwolakwa.
16
Ine ndidaŵayankha kuti si mwambo wa Aroma kungompereka munthu ai. Munthu wonenezedwayo amayamba wakumana nawo omnenezawo, kuti iyeyo akhale ndi mwai woyankhapo pa zimene akumnenezazo.
17
Tsono iwo atadzasonkhana kuno, ineyo mosataya nthaŵi, m'maŵa mwake ndidakakhala pa mpando woweruzira milandu, nkumuitanitsa munthuyo kuti abwere pamaso panga.
18
Omneneza aja ataimirira, sadamneneze choipa nchimodzi chomwe pa zimene ndinkaganiza ine.
19
Ankangokangana naye za chipembedzo chao, ndiponso ati za munthu wina dzina lake Yesu, amene adafa, koma Paulo amatsimikiza kuti ali moyo.
20
Ine ndidaathedwa nzeru, osadziŵa kuti ndiifufuze bwanji nkhani imeneyi. Choncho ndidamufunsa Pauloyo ngati akadakonda kupita ku Yerusalemu kuti mlandu wakewo ukazengedwere kumeneko.
21
Koma Paulo adapempha kuti abasungidwa m'ndende mpaka Mfumu ya ku Roma itatsimikiza za mlandu wake. Pamenepo ndidalamula kuti amsunge m'ndende kufikira nditamtumiza kwa Mfumuyo.”
22
Apo Agripa adauza Fesito kuti, “Inenso nkadakonda kuti ndidzimvere ndekha zimene munthuyu anene.” Fesito adati, “Mumumva maŵa.”
23
M'maŵa mwake Agripa ndi Berenise adabwera ndi ulemu waukulu wachifumu. Adaloŵa m'bwalo la milandu pamodzi ndi akulu a asilikali ndiponso akuluakulu a mumzindamo. Fesito adaitanitsa Paulo kuti abwere, iye nkubweradi.
24
Tsono Fesito adati, “Mfumu Agripa, ndi inu nonse amene muli nafe muno, mukumuwona munthu uyu. Ayuda onse adandipempha ku Yerusalemu ndi kuno komwe mofuula kuti ameneyu sayenera kukhalanso moyo.
25
Koma ine sindidapeze konse kuti iye adachita kanthu koyenera kumuphera. Ndiye popeza kuti mwiniwakeyu adapempha kuti mlandu wake ukazengedwe ndi Mfumu ya ku Roma, ndidatsimikiza zomtumiza.
26
Komabe ndilibe kanthu kenikeni koti ndilembere mfumuyo za iyeyu. Motero ndabwera naye kwa inu, makamaka kwa inuinuyo mfumu Agripa, kuti mutamufunsitsa, ndikhale nkanthu koti ndilembe.
27
Ine ndiye ndikuwona kuti ndi chinthu chopusa kutumiza mkaidi popanda kutchula zifukwa za mlandu wake.”
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28