bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 11
Deuteronomy 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 12 →
1
Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndipo nthaŵi zonse muzimvera malamulo ndi malangizo ake onse.
2
Popeza kuti si ana anu, koma ndinu amene mudazidziŵa ndi kuziwona zakale zonsezo, mukumbukire za Chauta, Mulungu wanu. Ukulu wake mudauwona, mudaonanso dzanja lake lamphamvu ndi mkono wake wotambalitsa.
3
Mudaona zizindikiro ndi ntchito zimene Chauta adachita polanga Farao ndi dziko lake lonse.
4
Mudaona zimene adachita polimbana ndi ankhondo a ku Ejipito ndiponso ndi akavalo ndi magaleta ao. Pamene iwo ankathamangitsa inu, mudaona m'mene Chauta adalamulira madzi a Nyanja Yofiira kuti aŵaphimbe ndi kuŵaononga onsewo.
5
Mudaona zonse zimene Chauta adakuchitirani m'chipululu muja, musanafike kuno.
6
Mudaona zimene Chauta adachita pa Datani ndi pa Abiramu, ana a Eliyabu, a fuko la Rubeni. Pamaso pa Aisraele onse nthaka idatsekuka nkuŵakwirira anthuwo, pamodzi ndi a m'banja mwao, mahema ao ndi zoŵeta zao zomwe.
7
Zoonadi mudaona zazikulu zonse zimene Chauta adachita.
8
Muzimvera zonse zimene ndakulamulani lerozi. Tsono mukatero, mudzakhala amphamvu, ndipo mudzaloŵa ndi kukhazikika m'dzikomo.
9
Mudzakhaladi nthaŵi yaitali m'dziko lamwanaalirenjilo, limene Chauta adalumbira kuti adzapatsa makolo anu ndi zidzukulu zao.
10
Dziko limene mukukakhalamolo likusiyana ndi dziko la Ejipito kumene mudachokera. Kumene kuja munkati mukafesa mbeu zanu, munkachita kuthirira ngati m'madimba.
11
Koma dziko limene mukukaloŵamolo ndi lamapiri ndi lazigwa. M'dziko limenelo mvula siitha.
12
Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene amasamalira dziko limenelo ndi kumaliyang'anira chaka chonse mosalekeza.
13
Nchifukwa chake tsono muzimvera malamulo ndakupatsani leroŵa: kukonda Chauta, Mulungu wanu, ndi kumamtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
14
Ndipo Iye azidzagwetsa mvula m'dziko mwanu pa nthaŵi yake, monga nthaŵi yadzinja ndiponso nthaŵi yachilimwe, kotero kuti mudzakhala ndi tirigu wambiri, vinyo wambiri ndiponso mafuta aolivi ambiri.
15
Adzameretsa udzu woti ng'ombe zanu zizidzadya, ndipo inunso mudzapeza chakudya ndi kukhuta.
16
Chenjerani, musasokeretsedwe ndi kutembenukira kwa milungu ina, kuti muziipembedza ndi kuitumikira,
17
chifukwa Chauta adzakukwiyirani, adzakumanani mvula, ndipo nthaka sidzabalanso zipatso zake. Motero mudzaonongeka msanga m'dziko lokomali limene Chauta akukupatsani.
18
Malamulo ameneŵa akhale m'mitima mwanu ndi m'maganizo mwanu. Muŵamange pamikono panu ndi pa mphumi pakati pa maso anu, kuti akhale chikumbutso.
19
Muŵaphunzitse kwa ana anu. Muziphunzitsa mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.
20
Alembeni pa mphuthu za zitseko za nyumba zanu ndi pa makomo anu.
21
Pamenepo inu ndi ana anu, mudzakhala ndi moyo nthaŵi yaitali m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adalumbira kuti adzapatsa makolo anu. Mudzakhala m'dziko limenelo nthaŵi zonse.
22
Muzimvera mokhulupirika zonse zimene ndakuuzanizi. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zonse zimene akulamulani, ndipo mukhale okhulupirika kwa Iye.
23
Tsono pamene inu mukupita, Chauta adzapirikitsa mitundu ina yonseyo, ndipo mudzalanda maiko a mitundu ya anthu akuluakulu ndi amphamvu kupambana inu.
24
Nthaka yonse imene mupondepoyo idzakhala yanu. Dziko lanulo lidzayambira ku chipululu kumwera, mpaka ku phiri la Lebanoni kumpoto, ndiponso kuyambira ku mtsinje wa Yufurate kuvuma, mpaka ku Nyanja Yaikulu kuzambwe.
25
Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adzakuletseni. Kulikonse kumene mudzapite m'dziko limenelo, anthu azidzakuwopani, monga momwe Mulungu wakulonjezerani kuti adzaŵachititsa mantha anthu amenewo.
26
Lero ndikukupatsani zinthu ziŵiri kuti musankhepo, madalitso kapena matemberero.
27
Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa.
28
Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.
29
Chauta akadzakuloŵetsani m'dziko limene mukupita kukakhalamolo, muzikalalika madalitso ameneŵa mutakwera pa phiri la Gerizimu, koma matembereroŵa muzikaŵalalika mutakwera pa phiri la Ebala.
30
Mapiri aŵiri ameneŵa ali chakuzambwe kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, m'dziko la Akanani amene amakhala m'chigwa cha Yordani, pafupi ndi mitengo ya thundu ya ku More, kuyang'anana ndi Giligala.
31
Muli pafupi kuwoloka Yordani ndi kukakhalamo m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani. Mukakalilandira ndi kukhalamo,
32
mukasamale kumvera malamulo ndi malangizo onse amene ndikukupatsani leroŵa.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34