bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 25
Deuteronomy 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 26 →
1
Tiyese kuti anthu aŵiri akangana. Tsono atapita ku bwalo lamilandu, aweruzi nkugamula kuti uyu sadalakwe koma wolakwa ndi winayu.
2
Ngati wolakwayo ayenera kukwapulidwa, muweruziyo amlamule kuti agone pansi ndipo akwapulidwe mikwapulo yolingana ndi kulakwa kwake.
3
Angathe kumkwapula mpaka mikwapulo makumi anai, koma osapitirira pamenepo. Zikapitirira pamenepo, ndiye kuti zidzamchititsa manyazi mbale wanuyo.
4
Ng'ombe imene ikupuntha tirigu, musaimange pakamwa.
5
Abale aŵiri akamakhala pamodzi, ndipo wina nkumwalira, koma osasiya mwana, mkazi wamasiyeyo asakwatiwe ndi munthu wa banja lina. Mbale wake wa malemuyo amtenge, amkwatire ndipo apitirize ntchito ya mbale wake kwa mkazi ameneyo.
6
Mwana woyamba kubadwa m'nyumbamo, adzakhala mwana wa mbale wake womwalirayo, kuti dzina la banja lake lisaferetu m'dziko la Israele.
7
Koma ngati mbale wa malemuyo samufuna mkazi wa mbale wakeyo, mkaziyo angathe kupita ku chipata kwa akuluakulu ndi kukadandaula kuti, “mbale wa mwamuna wanga uja sakufuna kuti dzina la mbale wakeyo lipitirire m'dziko la Israele. Akukana kundiloŵa chokolo.”
8
Pamenepo akuluakulu amumzindamo amuitane kuti alankhule naye. Akapitirira ndithu kukana kumkwatira,
9
mkaziyo apite kwa mlamu wakeyo pamaso pa akuluakulu onsewo, ndipo amuvule nsapato yakumodzi, amthire malovu kumaso ndi kunena kuti, “Zimenezi ndiye zoyenera kumchitikira munthu wokana chokolo cha mbale wake.”
10
M'dziko la Israele, banja la mwamunayo lidzatchedwa banja la munthu amene adamuvula nsapato yakumodzi.
11
Anthu aŵiri akamamenyana ndipo mkazi wa mmodzi pofuna kupulumutsa mwamuna wake, agwira mdani wakeyo ku moyo,
12
musamchitire chifundo mkazi ameneyo, mumdule dzanja.
13
Miyeso yopimira kulemera musakhale nayo iŵiri m'thumba mwanu, waukulu ndi waung'ono.
14
Miyeso yopimira kuchuluka musakhale nayo iŵiri m'nyumba mwanu, waukulu ndi waung'ono.
15
Miyeso ikhale miyeso yeniyeni yabwino, kuti mukakhale nthaŵi yaitali m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.
16
Chauta amadana ndi anthu onyenga mwa njira yotereyi.
17
Kumbukirani zimene adakuchitani Aamaleke nthaŵi ija munkachoka ku Ejipitoyi.
18
Analibe mantha ndi Mulungu. Motero adakuthirani nkhondo pa njira, pamene mudaali mutatheratu nkutopa. Paja adaŵapheratu anzanu onse amene ankachedwa ndi kuyenda m'mbuyo.
19
Motero tsono, Chauta, Mulungu wanu, akadzakupatsani dziko kuti likhale choloŵa chanu, nadzakulanditsani m'manja mwa adani anu onse okuzungulirani, kasamaleni kuti mukaphe Aamaleke onse, kuti munthu asadzaŵakumbukenso mpang'ono pomwe. Musaiŵale zimenezi.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34