bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 15
Deuteronomy 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 16 →
1
Chikatha chaka chachisanu ndi chiŵiri chilichonse, muzikhululukira onse amene adakongola zinthu zanu.
2
Zimenezi zizichitika motere: aliyense amene adakongoza Mwisraele mnzake ndalama, afafanize ngongole imeneyo. Asamuumirize kapena mbale wake kuti abweze ndalamazo, popeza kuti Chauta walamula kuti ngongoleyo ifafanizidwe.
3
Mungathe kulonjerera ngongole kwa mlendo yekha, koma ngongole ya munthu wa mtundu wanu muifafanize.
4
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu a mtundu wanu amene adzasauke, (poti Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko limene Iye adzakupatsani ngati choloŵa chanu,)
5
malinga mukamamvera mau ake ndi kusamala zotsata malamulo amene ndikukulamulani leroŵa.
6
Chauta adzakudalitsani inu monga momwe adalonjezera. Mudzakongoza mitundu yambiri, koma inuyo simudzakongola kwa wina aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri, koma palibe mtundu wina uliwonse umene udzakulamulireni inu.
7
Pakati pa abale anu pakakhala wina wosauka m'midzi yanu, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musadzaume mtima, ndipo musadzaume manja.
8
Makamaka muzidzamchitira chifundo ndi kumkongoza monga momwe angafunire.
9
Musadzakhale ndi maganizo achabe akuti, “Chaka chofafaniza ngongole chili pafupi.” Mukapanda kumuwonetsa mtima wachifundo mbale wanu wosaukayo, osampatsa kanthu, iyeyo adzakunenezani kwa Chauta molira, ndipo mudzapezeka olakwa.
10
Dzampatseni mwaufulu mosaŵinya, ndipo Chauta adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.
11
Nthaŵi zonse padzakhala Aisraele ena osauka, osoŵa zinthu. Motero ndikukulamulani kuti otereŵa muzidzaŵachitira chifundo.
12
Muhebri mnzanu, mwamuna kapena mkazi, akadzigulitsa kwa inu kuti akhale kapolo wanu, mummasule atangokutumikirani zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, mumlole kuti apite mwaufulu.
13
Mukammasula, musangomchotsa ali chimanjamanja.
14
Mpatseniko momkomera mtima zonse zimene Chauta adakudalitsa nazoni monga: nkhosa, tirigu ndi vinyo.
15
Kumbukirani kuti mudaali akapolo ku Ejipito, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adakuwombolani. Nchifukwa chake ndikukupatsani lamulo limeneli tsopano lino.
16
Koma kapoloyo akakhala kuti akukukondani inu ndi banja lanu, chifukwa mukukhala naye bwino, mwina sangafune nkuchoka komwe. Ngati zili choncho,
17
mutenge zingano ndipo muboole khutu la kapoloyo, mpaka zinganoyo iloŵe m'chitseko. Mukatero, adzakhala kapolo wanu moyo wake wonse. Ngati ndi kapolo wamkazi, mudzamchite chimodzimodzi.
18
Kumasula kapolo, kuti akhale mfulu, kusakuipireni. Adakutumikirani kale zaka zisanu ndi chimodzi pa theka la mtengo wa wantchito wolembedwa. Chitani zimenezi, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.
19
Ana onse amphongo oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a zoŵeta zina, muŵapatule kuti akhale a Chauta, Mulungu wanu. Ng'ombe zimenezi musazigwiritse ntchito, ndipo nkhosazo musazimete bweya.
20
Chaka ndi chaka inu, pamodzi ndi banja lanu, muzidya zimenezi pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, ndiponso ku malo amene Chauta adzasankhe.
21
Koma ngati pali kanthu kolakwika pa nyamayo, monga kutsimphina kapena khungu, kapena chilema chilichonse, musaphere nsembe Chauta nyama yoteroyo.
22
Nyama zotero, mudyere kwanu. Nonsenu, kaya ndinu oyeretsedwa pa za chipembedzo kapena ai, mungathe kudya zimenezo, monga momwe mumadyera mphoyo kapena ngondo.
23
Magazi okha musadye, koma mungoŵataya pansi ngati madzi.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34