bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 8
Deuteronomy 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 9 →
1
Zonse zimene ndakulamulani lero, mumvere mokhulupirika, kuti mukhale ndi moyo, muchulukane, ndipo mukakhazikike m'dziko limene Chauta adalonjeza makolo anu.
2
Kumbukirani m'mene Chauta, Mulungu wanu, adakutsogolerani m'chipululu, pa ulendo wa pa zaka zonse makumi anai zapitazi. Adakuvutani nakuyesani ndi zoŵaŵa, kuti adziŵe zimene zinali m'mitima mwanu, ndipo kuti aone ngati mudzamvera malamulo ake kapena ai.
3
Adakutsitsani pokukhalitsani ndi njala, komanso adakupatsani mana kuti mudye. Inu ndi makolo anu simudadyepo ndi kale lonse chakudya chimenechi. Adachita zimenezi kuti akuphunzitseni kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha ai, koma ndi mau onse otuluka m'kamwa mwa Mulungu.
4
Zovala zanu sizidathe, ndipo ngakhale mapazi anu omwe sadatupe konse m'chipululu pa zaka makumi anai zonsezi.
5
Dziŵani kuti Chauta, Mulungu wanu, amakulangani monga momwe bambo amalangira ana ake.
6
Tsono inu, muzichita monga momwe Chauta akulamulirani. Muziyenda m'njira zake ndipo muzimuwopa.
7
Chauta, Mulungu wanu, adzakuloŵetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje, la zitsime, la akasupe otumphukira m'zigwa ndi m'mapiri.
8
Lilinso ndi tirigu, barele, mphesa, nkhuyu, makangaza, olivi ndi uchi.
9
Kumeneko simudzakhala ndi njala, ndipo simudzasoŵa kanthu. Zitsulo zimapezeka m'miyala ya kumeneko, ndipo mungathe kukumbamo mkuŵa m'mapiri mwake.
10
Mudzakhala ndi chakudya chokwanira ndipo mudzakhuta, tsono mudzathokoza Chauta, Mulungu wanu, chifukwa wakupatsani dziko lokoma.
11
Samalani kuti musamaiŵala Chauta, Mulungu wanu. Musamalephera kumvera malamulo ndi malangizo ake amene ndakupatsani leroŵa.
12
Mukadzadya ndi kukhuta, mukadzamanga nyumba zabwino zoti mudzakhalemo,
13
mukadzakhala ndi ng'ombe, nkhosa, siliva ndi golide, ndipo chuma chanu chikadzanka chiwonjezekeraonjezekera,
14
pamenepo musadzanyade ndi kuiŵala Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito kumene mudaali akapolo.
15
Iye adakutsogolerani, mpaka mudabzola chipululu chachikulu ndi choopsa chija, m'mene munali njoka za ululu woopsa ndi zinkhanira. Adakupatsani madzi otuluka m'thanthwe, m'dziko louma lopanda madzi lija.
16
Adakupatsani mana oti mudye, chakudya chimene makolo anu anali asanadyepo, pofuna kukutsitsani ndi kukuyesani, kuti pambuyo pake akuchitireni zokoma.
17
Tsono muchenjere, musamati, “Ndapeza chuma chonsechi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga.”
18
Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.
19
Musamuiŵale Chauta, Mulungu wanu, ndi kutembenukira kwa milungu ina kuti muipembedze. Mukachimwa motero, ndithudi mudzaonongeka.
20
Mukapanda kumvera Chauta, Mulungu wanu, mudzaonongeka monga momwe Chauta akuwonongera mitundu ina pamaso panu.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34