bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 32
Deuteronomy 32
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 33 →
1
Dziko lakumwamba, imva zimene ndikuti ndilankhule. Dziko lapansi imva mau a pakamwa panga.
2
Zophunzitsa zanga zigwe ngati mvula, mau anga atsike ngati mame, ngati mvula yowaza pa msipu wanthete, ngati mvula yamphamvu pa udzu watsopano.
3
Ndidzatamanda dzina la Chauta. Tamandani ukulu wake wa Mulungu.
4
Chauta ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama, ndi Mulungu wokhulupirika ndi wosaipa konse, wachilungamo ndi wosalakwa.
5
Koma inu ndinu osakhulupirika, osayenera kukhala anthu ake, ndinu mtundu wochimwa ndi wonyenga.
6
Inu anthu opusa ndi opanda nzeru konse, kodi mungamubwezere zotere Chauta? Iye ndiye Atate anu ndi Mlengi wanu, ndiye adakupangani ndi kukusandutsani mtundu.
7
Kumbukirani zakale, lingalirani zamakedzana ndithu, funsani atate anu, akuuzani zimene zidachitika. Funsani akuluakulu, akufotokozerani zakalezo.
8
Pamene Wopambanazonse adapereka maiko kwa anthu a mitundu ina, pamene adalekanitsa anthu, adaŵaikira malire potsata kuchuluka kwa anthu a Mulungu.
9
Pajatu chigawo cha Chauta ndicho anthu ake, zidzukulu za Yakobe ndizo chigawo chakechake.
10
Adaŵapeza m'chipululu, kuthengo kwenikweni kopanda kanthu. Adaŵatchinjiriza, ndipo adaŵasamala, monga momwe akadasamalira diso lake.
11
Adachita ngati mphungu imene ikuphunzitsa ana ake kuuluka, imene ikungozungulira pamwamba pa ana akewo nitambalitsa mapiko ake, kuti igwire anawo ndi kuŵanyamula pa mapiko ake otambalitsa.
12
Chauta yekha ndiye adatsogolera anthu ake, popanda thandizo la milungu yachilendo.
13
Adaŵathandiza kuti azilamula maiko amapiri, ndipo adadya zomera zam'minda. Adaŵadyetsa uchi wam'mathanthwe, ndi mafuta ochokera m'nthaka yamiyala.
14
Adaŵamwetsa chambiko wochokera ku ng'ombe ndiponso mkaka wankhosa, adaŵadyetsa nkhosa ndi mbuzi zonenepa, ndiponso nkhosa zamphongo zabwino za ku Basani, pamodzi ndi tirigu wabwino ndi vinyo wokoma.
15
Yesuluni, anthu ake a Chauta adakulupala, koma iwowo adamuukira, adanenepa ndi kukula thupi, ndipo adakhuta zedi, kenaka adasiya Mulungu Mlengi wao, nanyoza mtetezi ndi mpulumutsi wao.
16
Adamchititsa nsanje ndi mafano ao achilendo, ndipo zonyansa zimene adachita zidamkwiyitsa.
17
Iwo adapereka nsembe kwa mizimu yoipa, imene siili milungu konse, milungu imene Aisraele sadaidziŵe nkale lonse, milungu yongobwera kumene, milungu imene makolo ao sankailemekeza konse.
18
Adakana mtetezi wao amene adaŵalenga, adaiŵala Mulungu amene adaŵapatsa moyo.
19
Chauta ataona zimenezi, adaŵakana anthuwo, chifukwa ana ao aamuna ndi aakazi adaautsa mkwiyo wake.
20
Iye adati, “Ndidzaŵafulatira, ndidzaona chomwe chidzaŵachitikire, chifukwa anthu ameneŵa ngonyenga, ndi ana osakhulupirika.
21
Milungu yao yabodza ndachita nayo nsanje, mafano ao andikwiyitsa nawo. Inenso ndidzaŵachititsa nsanje pakusamalira mtundu wina wachabechabe, ndipo ndidzaŵapsetsa mtima pakukondera fuko lina lopanda pake.
22
Mkwiyo wanga udzayaka ngati moto, udzafika mpaka ku dziko la anthu akufa. Udzatentha zonse pa dziko, udzapsereza ndi mapiri omwe mpaka m'tsinde mwake.
23
Ndidzaŵaunjikira masoka osatha, mipaliro yanga yonse idzathera pa iwowo.
24
Ndidzaŵatumizira njala yoopsa, malungo ndi nthenda zofa nazo. Ndidzaŵatumizira zilombo zakuthengo zoŵavuta, zokwaŵa zaululu zidzaŵaluma.
25
M'miseu adzafa chifukwa cha nkhondo, m'nyumba adzafa ndi mantha. Anyamata ndi atsikana adzafa, ngakhale ana ndi okalamba omwe sadzakhala ndi moyo.
26
Achikhala ndidangoŵaononga kotheratu onsewo, kuti anthu pansi pano asaŵakumbukire ndi mmodzi yemwe!
27
Koma sindifuna kuti adani ao azikandinyadira, sindifuna kuti adani azikaganiza molakwa, namanena kuti, ‘Tagonjetsa anthuwo ndife, si Mulungu amene adachita zonsezi.’ ”
28
Aisraele ndi mtundu wopanda maganizo, alibe ndi nzeru zomwe.
29
Achikhala anzeru, akadamvetsa, ndipo akadazindikira zimene zitha kudzaŵagwera.
30
Nanga chifukwa chiyani munthu mmodzi adagonjetsa anthu chikwi chimodzi, ndipo anthu aŵiri adagonjetsa zikwi khumi? Nchifukwa chakuti Chauta, Mulungu wao, waŵasiya, Mulungu wao wamphamvu waŵataya.
31
Adani ao amadziŵa kuti milungu yao ndi yopanda mphamvu, ndi yosalingana ndi Mulungu wa Aisraele.
32
Adani ao ndi oipitsitsa ngati Sodomu ndi Gomora, Ali ngati mipesa yobala mphesa zoŵaŵa ndi zaululu,
33
ndi oipa kwambiri ngati vinyo wosanganiza ndi ululu wa njoka, ululu wopweteka wa mphiri.
34
Zimenezitu ndazisunga, ndi zobisika m'chikatikati cha mumtima mwanga.
35
Kulipsira nkwanga, kubwezera zoyenerera nkwanganso, nthaŵi yoti agwe idzakwana. Tsiku la masoka ao layandikira, chiwonongeko chao chikudza mofulumira.
36
Chauta adzachitira anthu ake zolungama, adzachitira atumiki ake zachifundo, pamene adzaona kuti mphamvu zao zatha, ndipo kuti sipatsala anthu, kaya ndi akapolo kapena mfulu.
37
Pamenepo Chauta adzafunsa anthu ake kuti, “Nanga milungu yamphamvu yomwe mumaikhulupirira ija ili kuti?
38
Mudaidyetsa mafuta a nsembe zanu, mudaipatsa vinyo woti imwe. Ibweretu kuti ikuthandizeni, ikutetezeni.
39
Muwone tsopano kuti Mulungu uja ndine, Ine ndekha, palibenso mulungu wina. Ndimapha, Ine ndemwe ndimapatsanso moyo, ndimapweteka, Ine ndemwe ndimachiritsanso, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene angathe kupulumutsa munthu m'manja mwanga.
40
Ndikukweza dzanja kumwamba, ndikulumbira pali Ine ndemwe wa moyo wosatha,
41
kuti ndidzanola lupanga langa lochezimira, ndipo ndidzaona kuti chilungamo chichitike. Adani anga ndidzaŵabwezera chilango, amene amadana nane ndidzaŵalanga.
42
Mivi yanga idzafiira ndi magazi ao ndipo lupanga langa lidzabayadi mnofu wao. Olasidwa ndi ogwidwa ukapolo magazi ao adzafalikadi, ndiponso mitu yao ya tsitsi litalilitali idzadulidwa.”
43
Inu mitundu yonse ya anthu, tamandani anthu a Chauta. Chauta amalanga onse opha anthu ake, amalipsira adani ake, ndipo amachotsa tchimo m'dziko la anthu ake.
44
Mose ndi Yoswa mwana wa Nuni adanena pamtima mau onse a nyimbo imeneyi, ndipo Aisraele ankamva.
45
Mose atatha kuphunzitsa anthu mau onseŵa,
46
adati: Mukumbukire bwino malamulo onse amene ndakupatsani leroŵa. Muuze ana anu kuti azimvera mosamala mau onse a malamuloŵa.
47
Mauŵa sikuti ndi mau achabe. Mau ameneŵa ndiwo moyo wanu. Muŵamvere, ndipo mudzakhalitsa m'dziko mukukakhalamolo uko kutsidya kwa Yordani.
48
Tsiku lomwelo, Chauta adalankhula ndi Mose kuti,
49
“Kwera phiri loti Nebo ku mtandadza wa mapiri a Abarimu, umene uli m'dziko la Mowabu, kuyang'anana ndi mzinda wa Yeriko. Ulipenye dziko la Kanani limene ndikuŵapatsa Aisraele.
50
Iwe udzafera pa phiri limenelo, monga mbale wako Aroni adafera pa phiri la Horo.
51
Chifukwa chake nchakuti inu nonse aŵiri simudakhulupirike kwa Ine pamaso pa Aisraele. Pamene munali ku madzi a Meriba, pafupi ndi mudzi wa Kadesi, m'chipululu cha Zini, simudandilemekeze kokwanira pamaso pa Aisraele.
52
Nchifukwa chake dziko limene ndikupatsa Aisraele uliwonere chapatali, koma kuloŵa kokha ndiye ai, suloŵamo”.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34