bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 33
Deuteronomy 33
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 34 →
1
Mose, munthu wa Mulungu uja, asanafe, adapereka madalitso kwa Aisraele.
2
Poŵadalitsapo adanena mau akuti, “Chauta adabwera kuchokera ku phiri la Sinai, natitulukira kuchokera ku Seiri, ndipo adatiŵalira kuchokera ku phiri la Parani. Angelo zikwi khumi anali naye pamodzi, moto woyaka unali m'manja mwake.
3
Chauta amakonda anthu ake ndipo amatchinjiriza onse amene ali opatulikira Iye. Anthuwo amaphunzira kwa Chauta, amamvera malangizo ake,
4
ndiye kuti malamulo amene adatipatsa Mose. Malamulowo ndi chuma chopambana cha mtundu wa Yakobe.
5
Chauta adakhala mfumu ya anthu ake Aisraele, pamene mafuko ao ndi atsogoleri ao adasonkhanitsidwa pamodzi.”
6
Ponena za fuko la Rubeni, Mose adati, “Rubeni asafafanizike, akhalitse ndithu, ngakhale anthu ake ali pang'ono.”
7
Za fuko la Yuda, adati, “Inu Chauta, mverani pamene iwo akulira, athandizeni, ndipo muŵalumikizenso ndi mafuko ena. Inu Chauta, muŵalimbikitse kuti adziteteze okha, ndipo muŵathandize polimbana ndi adani ao.”
8
Za fuko la Levi adati, “Inu Chauta, Tumimu ndi Urimu adziŵitse kufuna kwanu kudzera mwa Alevi, atumiki anu okhulupirika. Mudaŵayesa ku Masa kuja, ndipo mudalimbana nawo ku madzi a Meriba kuja.
9
Iwo adaonetsa kuti ankakhulupirira Inu kupambana makolo ao, abale ao kapenanso ana ao. Adamvera malamulo anu, ndipo adakhulupirika pa chipangano chanu.
10
Iwowo ndiwo adzaphunzitse ana a Yakobe malangizo anu ndi Aisraele malamulo anu. Adzafukiza lubani pamaso panu, adzapereka nsembe zathunthu zopsereza pa guwa lanu.
11
Inu Chauta, thandizani fuko lao kuti likhale lamphamvu, zochita zao zikukondwetseni. Otsutsana nawo ndi odana nawo onse muŵaononge, kotero kuti asadzadzukenso.”
12
Za fuko la Benjamini adati, “Fuko ili ndilo limene Chauta amalikonda, ndipo amalitchinjiriza. Tsiku ndi tsiku Chauta amalisunga, pokhala m'kati mwa dziko laolo.”
13
Za fuko la Yosefe adati, “Chauta adalitse dziko lao, likhale la mvula yambiri, ndipo la zitsime zochuluka.
14
Dziko lao lidalitsidwe pokhala ndi zipatso zopsa ndi dzuŵa, likhalenso ndi zokolola zochuluka pa nyengo iliyonse.
15
Mapiri ao akalekaleŵa akutidwe ndi zipatso, ndipo adzazidwe ndi zokolola zochuluka.
16
Dziko lao likhale ndi dzinthu dzopambana, lidalitsidwe ndi zokoma za Chauta amene adalankhula m'chitsamba choyaka chija. Madalitso onseŵa atsikire fuko la Yosefe, popeza kuti anali mtsogoleri pakati pa abale ake.
17
Yosefe ali ndi mphamvu zonga za ng'ombe yamphongo, nyanga zake ndi zonga za njati, adzapirikitsa anthu a mitundu ina ndi nyanga zimenezi. Onsewo adzaŵapirikitsira ku malekezero a dziko. Nyanga zimenezi ndi anthu zikwi khumi za Efuremu ndipo anthu zikwi za Manase.”
18
Za mafuko a Zebuloni ndi Isakara, adati, “Zebuloni akondwere pa malonda ake, Isakara akondwere m'zithando mwake.
19
Ku mapiri ao amaitanirako mitundu ya anthu, kumeneko amaperekako nsembe zoyenera, chifukwa choti amapeza chuma pochita malonda m'nyanja, kuchokera mu mchenga wa m'mbali mwa nyanja.”
20
Za fuko la Gadi, adati, “Alemekezeke Chauta amene adakulitsa dziko la Gadi. Gadi amalalira ngati mkango waukazi, amamwetula dzanja ndi bade la mutu lomwe.
21
Adadzitengera dziko labwino kuti likhale lao, gawo la mtsogoleri lidaperekedwa kwa iwowo. Adasunga maweruzo ndi malamulo a Chauta pamene atsogoleri a Aisraele adasonkhanitsidwa pamodzi.”
22
Za fuko la Dani adati, “Dani ali ngati mwana wamkango, amene amalumpha kuchokera ku Basani.”
23
Za fuko la Nafutali, adati, “Chauta wakomera mtima Nafutali namdalitsa kwambiri. Dziko lake lifika mpaka kumwera kuchokera ku nyanja ya Galileya.”
24
Za fuko la Asere, adati, “Asere ndi wodalitsidwa kupambana mafuko ena. Abale ake amkonde, dziko lake likhale lachuma, la mitengo ya olivi.
25
Midzi yake itchinjirizidwe ndi zitseko zachitsulo m'malinga, mphamvu zake zikhalitse monga masiku a moyo wake.”
26
Inu Aisraele, palibe mulungu wina wofanafana ndi Mulungu wanu, amene amayenda ndi ulemerero mu mlengalenga, amakwera pa mitambo namabwera kudzakuthandizani.
27
Chauta ndiye amene ali kothaŵirako ndipo pa dziko lapansili amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda, ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse.
28
Motero Aisraele ali pa mtendere, zidzukulu za Yakobe zikusungidwa bwino m'dzikomo m'mene tirigu ndi vinyo sizisoŵa, m'mene mame amangogwa kuchokera kumwamba.
29
Iwe Israele, ndiwetu wodala, wofanafana nawe palibe. Ndiwe mtundu umene Chauta adaupulumutsa. Chauta weniweniyo ndiye chishango chako ndi lupanga lako, ndiye amene amakutchinjiriza ndi kukupambanitsa. Adani ako adzafika kudzapempha kuti uŵachitire chifundo, koma iwe udzaŵapondereza pansi.
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34