bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 13
Deuteronomy 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 14 →
1
Mwina mneneri kapena womasulira maloto adzaoneka pakati panupo, namanena kuti adzachita chizindikiro kapena chozizwitsa,
2
Chizindikirocho kapena chozizwitsacho chikachitikadi, iye nakuuzani kuti mupembedze ndi kutumikira milungu ina imene simudaipembedzepo nkale lonse,
3
inu musamvere zimenezo. Chauta, Mulungu wanu, akulola zimenezo kuti akuyeseni, kuti aone ngati mumamkondadi ndi mtima wanu wonse.
4
Mutsate Chauta, Mulungu wanu, ndi kuwopa Iye yekha. Mutsate malamulo ake ndi kumvera mau ake. Mutumikire Iye ndi kuphathana naye.
5
Koma aphedwe mneneri aliyense kapena womasulira maloto aliyense amene akuuzani kuti muukire Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito ndi kukuwombolani m'dziko laukapolo. Munthu wotero ndi woipa, chifukwa akufuna kukusiyitsani njira imene Chauta akufuna kuti muitsate. Aphedwe, ndipo pakutero mudzachotsa choipa chimenechi pakati panu.
6
Munthu atha kukunyengererani mobisa kuti mupembedze milungu ina, milungu imene inu ndi makolo anu simudaipembedzepo. Munthuyo ngakhale akhale mbale wanu weniweni wa mimba imodzi kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena bwenzi lanu lapamtima, musaipembedze milunguyo mpang'ono pomwe.
7
Milungu yake mwina idzakhala milungu ya anthu omwe mwayandikana nawo, kapena milungu ya amene mwatalikirana nawo.
8
Inu musakopeke kapena kumvera zimene iyeyo akunena. Musamchitire chifundo kapena chisoni, ndipo musamtchinjirize.
9
Mupheni! Yambani ndinu kumponya miyala, ndipo mutatero, pamenepo aliyense amponyenso miyala.
10
Mumuphe ndi miyala. Iye adati akusokeretseni, kuti musiyane ndi Mulungu wanu amene adakutulutsani ku dziko la Ejipito kumene mudaali kuukapolo kuja.
11
Tsono Aisraele onse adzamva zimene zachitikazo nadzachita mantha, ndipo palibe wina pakati panu amene adzachitenso choipa choterechi.
12
Pomakhala m'midzi imene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsaniyo, nthaŵi zina kapena mudzamva
13
kuti anthu ena a mtundu wanu asokeretsa anthu m'mizinda yao yomwe. Akuŵapembedzetsa milungu imene inu simudaipembedzepo nkale lonse.
14
Mbiri yoteroyo muifufuze bwino. Mukapeza kuti mbiriyo njoona, kuti chinthu choipa choterechi chidachitikadi,
15
pompo muphe anthu onse amumzindamo pamodzi ndi zoŵeta zomwe. Muwononge mudzi umenewo kotheratu.
16
Zinthu zonse za anthu a mu mzinda umenewo muzisonkhanitse pamodzi, ndipo muziwunjike pakati pa bwalo lalikulu la mzindawo. Tsono mutatero, muutenthe mzindawo pamodzi ndi zonse zam'menemo, kuti zikhale ngati nsembe yopsereza kwa Chauta, Mulungu wanu. Muusiye choncho kuti ukhale bwinja mpaka muyaya.
17
Musagwireko kanthu kena kalikonse koyenera kuwonongedwa. Tsono Chauta adzaleka osakukwiyiraninso, adzakumverani chisoni ndipo adzakuchitirani chifundo, nadzakuchulukitsani monga adalonjezera makolo anu.
18
Adzakuchitirani zimenezi mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, mukamatsata malamulo ake amene ndikukuuzani lero, ndipo mukamachita zolungama pamaso pa Chauta, Mulungu wanu.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34