bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 19
Deuteronomy 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 20 →
1
Chauta, Mulungu wanu, ataononga eniake a dziko limene akukupatsanilo, ndipo inu mutalanda mizinda yao pamodzi ndi nyumba zao, nkukhazikika kumeneko,
2
mudzapatule mizinda itatu m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsenilo.
3
Mudzakonze miseu yake, ndipo mudzaligaŵe patatu dzikolo. Choncho kudzakhala malo amene munthu wopha mnzake adzatha kuthaŵirako.
4
Nali lamulo lokhalira munthu wopha mnzake, amene angapulumutse moyo wake pothaŵira kumeneko: Munthu akapha mnzake mwangozi, osati chifukwa cha chidani, athaŵire ku mzinda uliwonse mwa mizinda imeneyo kuti apulumuke.
5
Mwachitsanzo, anthu aŵiri apita ku thengo limodzi kukadula mitengo. Wina podula mtengo, nkhwangwa nkuguluka, nipha mnzakeyo. Iye angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, napulumuka.
6
Akapanda kutero, mwina chifukwa cha kutalika kwa mtunda, wachibale wofuna kumlipsira adzamthamangira mwaukali, nkumugwira wothaŵayo namupha, ngakhale ali wosayenera kuphedwa, chifukwa paja popha munthu mwangozi analibe chidani chilichonse ndi amene adafayo.
7
Nchifukwa chake ndikukulamulani kuti mupatule mizinda itatu.
8
Chauta, Mulungu wanu, akadzakuza dziko lanu monga momwe adalonjezera makolo anu, ndipo akadzakupatsani dziko lonse limene adalonjeza,
9
pamenepo mudzapatulenso mizinda ina itatu. Adzakuwonjezerani dziko ndithu, malinga mukamakachita zonse zimene ndikukulamulani, ndiye kuti kukonda Chauta, Mulungu wanu, ndi kuchita zonse zimene akukuphunzitsani.
10
Muzidzachita zimenezi kuti musadzalakwe pakupha anthu osachimwa m'dziko limene Chauta akukupatsanilo.
11
Mwina mwake munthu adana ndi mnzake, ndipo amkhalizira namupha mwadala, nkuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti apulumuke.
12
Zikatero, akuluakulu akwao adzamuitanitse kuchokera ku mzinda wakewo, ndi kukampereka kwa woyenera kumlipsira uja kuti aphedwe ndithu.
13
Musamchitire chifundo. Mchotseni pakati pa Aisraele munthu wopha mnzake wosalakwa, kuti zinthu zikuyendereni bwino.
14
M'choloŵa chomwe mudzakhala mutalandira m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musakaŵafutuze malire a mnzanu amene anthu akale adakhazika.
15
Mboni imodzi sikwanira kumtsimikiza munthu kuti wachimwadi kapena kuti wapalamuladi mlandu pakuchita cholakwa chakutichakuti. Chofunika nchakuti pakhale mboni ziŵiri kapena zitatu zotsimikiza kuti munthuyo walakwadi.
16
Munthu wina akaneneza mnzake momnamizira kuti walakwa,
17
aŵiri onsewo abwere, adzaimirire pamaso pa Chauta. Kumeneko aŵaweruze ansembe ndi aweruzi amene ali pa ntchito nthaŵi imeneyo.
18
Aweruziwo adzafufuze za mlanduwo. Akapeza kuti munthu uja ndi mboni yachabe ndipo kuti waneneza mnzake monama,
19
amlange pomchita choipa chimene iyeyo anati achite mnzake. Mwa njira imeneyi, mudzachotsa choipa chimenechi pakati pa inu.
20
Tsono wina aliyense akadzamva zimene zachitika, adzakhala ndi mantha, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzachitenso choipa choterechi.
21
Musachite chifundo. Chilango chake chikhale chakuti moyo ulipe moyo, diso lilipe diso, dzino lilipe dzino, dzanja lilipe dzanja, ndipo phazi lilipe phazi.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34