bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 14
Deuteronomy 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 15 →
1
Inu ndinu anthu a Chauta, Mulungu wanu. Mukamalira maliro, musamadzichekacheka kapena kudzimeta pamphumi.
2
Ndinu ake a Chauta, Mulungu wanu, popeza kuti wakusankhulani pakati pa anthu a pa dziko lonse lapansi, kuti mukhale anthu akeake.
3
Chilichonse chimene Chauta akuti nchonyansa, musadye.
4
Nyama zoti muzidya ndi izi: ng'ombe, nkhosa, mbuzi,
5
ngondo, nswala, mphoyo, mphalapala, ngoma, nyumbu ndi mbalale.
6
Mungathe kudya nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogaŵikana ndiponso yobzikula.
7
Koma pakati pa nyama zaziboda kapena zobzikula, musadye izi: ngamira, kalulu ndi mbira, chifukwa ngakhale zimabzikula, koma zilibe ziboda zogaŵikana.
8
Nkhumbanso ndi yonyansa kwa inu. Ziboda ili nazo, komatu sibzikula. Nyama zimenezi musamadya, ndipo musamazikhudza zikafa.
9
Mwa zonse zokhala m'madzi mungathe kudya izi: zonse zimene zili ndi zipsepse ndi mamba.
10
Koma zonse zopanda zipsepse ndi mamba ndi zonyansa kwa inu, choncho musadye.
11
Mbalame zonse zoyenera kuzidya, mudye.
12
Koma mbalame zosayenera kuzidya ndi izi: mphungu, nkhwazi, mwimba,
13
kamtema, khungubwi ndi mtundu uliwonse wa mwimba,
14
mtundu uliwonse wa akhungubwi,
15
nthiŵatiŵa, chipudo, kakoŵa, mtundu uliwonse wa akabaŵi,
16
nkhutukutu, mantchichi, tsakwe,
17
vuwo, dembo, chiswankhono,
18
indwa ndi chimeza ndi zina za mtundu umenewu, ndiponso nsadzu ndi mleme.
19
Ziwala zonse zamapiko ndi zonyansa, choncho musadye zimenezo.
20
Koma zonse zamapiko zosaipitsidwa mungathe kudya.
21
Nyama iliyonse yofa yokha, musadye. Alendo okha amene mumakhala nawo, alekeni adye, kapena mungogulitsa nyamayo kwa alendo ena. Pajatu inu ndinu opatulika a Chauta, Mulungu wanu. Musaphike mwanawankhosa kapena mwanawambuzi mu mkaka wa make.
22
Chachikhumi muziika padera, ndiye kuti limodzi mwa magawo khumi a zokolola zanu za chaka ndi chaka.
23
Tsono pitani mukakhale pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzasankhula kuti anthu azidzampembedzerapo. Ndipo magawo achachikhumi ameneŵa mudyere pa malo amenewo, pamaso pa Mulungu wanu. Magawo ameneŵa ndi a tirigu, vinyo ndi mafuta aolivi, ndiponso ana oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a nkhosa. Muzichita zimenezi masiku onse, kuti motero muphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu.
24
Koma mwina mtunda udzakutalikirani chifukwa kwatalikitsa kumalo kumene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azimpembedzerako. Motero inu mudzalephera kupita nawo kumeneko magawo anu achachikhumiwo, amene mwaŵapeza chifukwa cha madalitso a Chauta, Mulungu wanu.
25
Pamenepo mugulitse zinthuzo, ndipo ndalama zake mupite nazo ku malo achipembedzowo.
26
Ndalamazo mugulire zilizonse zimene mufuna, monga nyama yang'ombe, nyama yankhosa, vinyo ndiponso zakumwa zaukali, malinga nkukhosi kwanu. Tsono inuyo pamodzi ndi mabanja anu, mudzadye ndi kusangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu.
27
Koma Alevi amene mumakhala nawo m'midzi mwanu musaŵaiwale, popeza kuti alibe dziko kapena choloŵa chaochao.
28
Chaka chachitatu chilichonse muzibwera ndi magawo onse achachikhumi ochokera ku zopereka zanu za chaka chimenecho, ndi kuŵaika poyera m'midzi mwanu.
29
Chakudya chimenechi ncha Alevi, poti alibe zaozao. Ndiponso ncha alendo ndi cha ana amasiye ndi akazi amasiye amene amakhala nanu pamodzi m'midzi mwanu. Anthu otere azibwera kudzatenga zimene akusoŵa. Muzichita zimenezi kuti Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitseni pa ntchito zanu zonse.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34