bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 20
Deuteronomy 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 21 →
1
Mukadzapita kukamenyana ndi adani anu, ngati muwona kuti magaleta ao ngochuluka kuposa anu, ngamira zao ndi zochulukanso, ndipo ngakhale ankhondo ao omwe ngokuposani, musakaŵaope. Chauta, Mulungu wanu, amene adakupulumutsani ku Ejipito, adzakhala nanu.
2
Musanayambe kumenya nkhondo, wansembe abwere, ndipo auze ankhondowo kuti,
3
“Imvani, inu Aisraele! Lero mukuyamba kumenya nkhondo ndi adani anu. Musataye mtima ai! Musaŵaope adaniwo, musanjenjemere, musachite mantha.
4
Chauta, Mulungu wanu, apita nanu Iye yemwe kuti akuthandizeni pa nkhondoyo ndipo kuti akupambanitseni.”
5
Pamenepo akuluakulu a ankhondo adzauza anthu kuti, “Kodi alipo pano munthu amene wangomanga nyumba yatsopano, koma sanaipereke kwa Mulungu? Ngati alipo abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzaipereka nyumbayo.
6
Kodi alipo pano wina amene wangooka mipesa m'munda, koma osakhala ndi mwai woti nkuthyola mphesa zake? Ngati alipo abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzamwe vinyoyo.
7
Kodi alipo wina pano amene adafunsira mbeta koma mkaziyo sanaloŵane naye? Ngati alipo, abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzakwatire mbetayo.”
8
Pamenepo akuluakuluwo adzafunsanso anthu kuti, “Kodi alipo pano wina aliyense amene akuwopa ndipo mtima wake wafumuka ndi mantha? Ngati alipo, abwerere kwao, kuti angamakadederetse anzake.”
9
Akuluakulu atamaliza kulankhula ndi gulu lankhondolo, asankhe mtsogoleri pa gulu lililonse.
10
Mukamapita kukathira nkhondo mzinda, poyamba apatseni anthu amumzindawo mwai woti agonje okha.
11
Akakutsekulirani zipata nakugonjerani, akhale akapolo anu onsewo, ndipo akugwirireni ntchito yaukapolo.
12
Koma ngati anthu a mu mzinda umenewo akana kugonja, nasankhula nkhondo, uzingeni mzindawo ndi gulu lanu lankhondo.
13
Chauta, Mulungu wanu, akakulolani kugonjetsa mzindawo, muphe mwamuna aliyense m'menemo.
14
Koma akazi ndi ana mungoŵagwira, ndipo mutengenso zoŵeta ndi zonse zimene zili mumzindamo ngati zofunkha zanu. Zinthu zonse za adani anu muzigwiritse ntchito, Chauta wakupatsani zimenezo.
15
Umu ndi m'mene muzikachitira ndi mizinda ya kutali ndi inu, imene siili mizinda ya anthu akuno.
16
Koma mukadzalanda mizinda imene ili m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsaniyo, muphe aliyense.
17
Muŵaononge kotheratu onse anthu aŵa: Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi, monga momwe Chauta Mulungu wanu adakulamulirani.
18
Iphani onse, kuti angadzakuchimwitseni kuchimwira Chauta, Mulungu wanu, pokuphunzitsani zoipa zimene iwowo amachita akamapembedza milungu yao.
19
Pamene muzinga mzinda nthaŵi yaitali ndi cholinga choti muulande, musagwetse mitengo yake yazipatso, mungathe kudya zipatso zake, koma mitengo yake musagwetse, chifukwa adani anu si mitengoyo.
20
Koma mitengo ina yosabereka zipatso mungathe kuidula ndi kumagwira nayo ntchito popanga makina ankhondo okhalirira mzinda umene mukulimbana nawo mpaka mutaugonjetsa.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34