bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 18
Deuteronomy 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 19 →
1
Ansembe Achilevi, ndiye kuti fuko lonse la Alevi, asalandireko gawo m'dziko la Israele ngati choloŵa chao. Iwoŵa azidya zoperekedwa nsembe kwa Chauta ndi zina zoyenera Iyeyo.
2
Asakhale ndi choloŵa ngati mafuko ena. Choloŵa chao ndi Chauta amene, potsata malonjezo a Mulungu yemweyo.
3
Mwa zopereka za anthu, zoyenera kuzilandira ansembeŵa, ndi izi: ng'ombe kapena nkhosa zodzaperekera nsembe, mwendo wamwamba, nyama yam'chibwano ndi chifu.
4
Ansembe azilandiranso gawo lanu loyambayamba la tirigu, la vinyo, la mafuta aolivi ndiponso la ubweya.
5
Pa mafuko anu onseŵa Chauta adasankhulapo anthu a fuko la Levi ndi ana ao, kuti azigwira ntchito zaunsembe nthaŵi zonse.
6
Mlevi aliyense atafuna, angathe kubwera ku malo osankhidwa ndi Chauta kuchokera m'mudzi wina uliwonse ku Israele kumene akukhala.
7
Ndipo kumeneko atumikire Chauta, Mulungu wake, pa unsembe, monga momwe achitira Alevi ena onse amene akutumikira kumeneko.
8
Ayenera kulandira chakudya molingana ndi ansembe ena, ngakhale ali ndi ndalama chifukwa chogulitsa za m'banja mwake.
9
Mukadzaloŵa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musakatsate machitidwe onyansa a mitundu ya anthu akumeneko.
10
Pakati panu pasadzapezeke wopereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto ngati nsembe. Pasaoneke munthu woombeza kapena woyeseza kulosa zam'tsogolo, kapena wogwiritsa ntchito nyanga kapena zithumwa.
11
Pasapezekenso munthu wopempha nzeru kwa mizimu ya anthu akufa.
12
Chauta, Mulungu wanu, amadana nawo anthu ochita zoipa zimenezi. Chimene Mulungu akupirikitsira anthuŵa pamene inu mukufika ndi chifukwa chakuti anthuwo ankachita zoipa zoterezi.
13
Inu mukhale okhulupirika kwathunthu kwa Chauta, Mulungu wanu.
14
Anthu amene mukukaŵalanda dziko limene mukakhalemolo, amatsata ndi kumvera amatsenga ndi oombeza. Koma inuyo Chauta, Mulungu wanu, sakulolani kuchita zimenezi.
15
Iye adzakutumizirani mneneri wonga ine wochokera mwa inu amene, ndipo mudzayenera kumumvera iyeyo.
16
Pa tsiku lija mudaasonkhana pa phiri la Horebuli, mudaapempha kuti, “Tisamvenso Chauta, Mulungu wathu, akulankhula, ngakhale kuwonanso moto waukulu choterewu, kuti tingafe.”
17
Apo Chauta adaandiwuza kuti, “Zonse zimene apemphazi anena mwanzeru.
18
Ndidzaŵatumizira mneneri wonga iwe, wochokera mwa iwo amene. Ndidzamuuza zoti anene, ndipo iyeyo azidzauza anthu zonse zimene ndikumlamula.
19
Mneneriyo akalankhula m'dzina langa, Ine ndidzalanga aliyense wosamvera mau angawo.
20
Koma mneneri wina aliyense woyerekeza kulankhula m'dzina langa, Ine osamulamula kuti atero, aphedwe. Ndipo ayeneranso kuphedwa mneneri wina aliyense wolankhula m'dzina la milungu ina.”
21
Mwina mwake munganene kuti, “Kodi munthu angadziŵe bwanji kuti mau a mneneri wakutiwakuti sakuchokera kwa Chauta?”
22
Munthu akati akulankhula m'dzina la Chauta, ndipo ngati zolankhula zakezo sizichitika, pomwepo dziŵani kuti si mau a Chauta amenewo. Mneneri ameneyo wongolankhula zakezake modzikhulupirira, musamuwope ai.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34