bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 6
Deuteronomy 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 7 →
1
Tsono aŵa ndi malamulo, malangizo ndi zina zoyenera kuzitsata, zimene Chauta, Mulungu wanu, adandilamula kuti ndikuphunzitseni. Muzikatsata zonsezi m'dziko limene mudzaloŵa ndi kukhalamolo,
2
nthaŵi zonse pamene muli moyo, inu ndi zidzukulu zanu. Muzikaopa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muzikamvera malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsaniŵa, kuti pakutero mukakhale moyo nthaŵi yaitali.
3
Inu Aisraele, mutchere khutu, ndipo muchenjere, mumveredi malamuloŵa. Tsono zinthu zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala mtundu wochuluka zedi ndi kumakhala m'dziko lamwanaalirenji, monga momwe Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakulonjezerani.
4
Mverani, inu Aisraele, Chauta Mulungu wathu ndi mmodzi yekha.
5
Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse.
6
Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa.
7
Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.
8
Amangeni pamikono panu, ndiponso muŵaike pa mphumi pakati pa maso anu.
9
Alembeni pa mphuthu za zitseko za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.
10
Chauta, Mulungu wathu, adalonjeza makolo anu aja Abrahamu, Isaki ndi Yakobe kuti adzakupatsani inu dziko limene lili ndi mizinda ikuluikulu ndi yachuma, imene inu simudaimange.
11
Nyumba zake zidzakhala zodzaza ndi zinthu zabwino zimene inuyo simudaikemo. Zitsime zidzakhala zokumbiratu ndipo padzakhala minda yamphesa ndi yaolivi imene simudalime ndinu. Chauta akadzakuloŵetsani m'dziko limeneli, ndipo mukadzakhala ndi chakudya chambiri,
12
musadzaiŵale Chauta amene adakutulutsani ku Ejipito, dziko laukapolo.
13
Muziwopa Chauta, Mulungu wanu. Muzipembedza Iye yekha, ndipo mukamalumbira, muzitchula dzina lake lokha.
14
Musamapembedza milungu ina, milungu imene amaipembedza anthu okhala mozunguliramu,
15
popeza kuti mukatero, mkwiyo wa Chauta udzakuyakirani ngati moto, ndipo udzakuwonongani kwathunthu, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amene amakhala pakati panu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye.
16
Musamupute Chauta, Mulungu wanu, monga mudachitira ku Masa kuja.
17
Musamale kuti musunge malamulo onse amene Iye akupatsani.
18
Muzichita zokhazo zimene Chauta akuti ndi zolungama ndi zabwino, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. Mudzalandira dziko labwinolo limene Chauta adalonjeza molumbira kuti adzapatsa makolo anu.
19
Adani anu mudzaŵapirikitsa, monga Chauta adalonjezera.
20
Nthaŵi zakutsogoloko, ana anu adzakufunsani kuti, “Kodi chifukwa chiyani Chauta, Mulungu wathu, adakulamulani kuti muzimvera malamulo ndi malangizo ndi zina zonse zoyenera kuzitsatazi?”
21
Tsono inu mudzaŵauze kuti, “Ife tidaali akapolo a mfumu ya dziko la Ejipito, koma Mulungu adatipulumutsa ndi mphamvu zake zazikulu.
22
Ife tidapenya ndi maso athu Chauta akuchita zodabwitsa ndi zoopsa kuti alange Aejipito, mfumu yao ndi banja lao lonse.
23
Mulunguyo adatitulutsa ife ku Ejipito, natifikitsa kuno ndi kutipatsa dziko lino, monga momwe adalonjezera kwa makolo athu.
24
Pamenepo Mulungu wathu adatilamula kuti tizimvera malamulo onseŵa, ndiponso kuti tizimuwopa. Tikamatero, Iyeyo adzasunga mtundu wathu, ndipo adzautukula monga momwe akuchitiramu tsopano.
25
Tikamasunga mokhulupirika zonse zimene Chauta Mulungu wathu watilamula, Iyeyo adzakondwera nafe.”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34