bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 9
Deuteronomy 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 10 →
1
Mvetsani inu Aisraele. Muli pafupi kuwoloka mtsinje wa Yordani ndi kukakhala m'dziko la anthu aakulu ndi amphamvu kupambana inu. Mizinda yao ndi ya malinga aatali ofika mpaka kumwamba.
2
Anthu ake ngotchuka ndiponso ataliatali. Anthu amenewo ndi zidzukulu za Aanaki amene mukuŵadziŵa kale. Paja mudamva kale kuti amati, “Ndani angalimbane ndi zidzukulu za Anaki?”
3
Koma lero mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakutsogolerani monga momwe umachitira moto wopsereza. Adzagonjetsa onse pamaso panu, kotero kuti mudzaŵapirikitsa ndi kuŵaononga mwamsanga monga Chauta adakulonjezerani.
4
Chauta, Mulungu wanu, ndiye adzakupirikitsirani iwowo. Ndiye inu musadzanene kuti wakuloŵetsani ndi kukupatsani dzikolo chifukwa cha zabwino zimene mwachita. Ai, Chauta akupirikitsirani anthu ameneŵa chifukwa choti iwowo ngoipa.
5
Chimene Chauta akukulolerani kuŵalanda dziko anthuwo, si chifukwa chakuti ndinu abwino ndi angwiro ai. Akuŵapirikitsa chifukwa iwowo ngoipa, ndiponso chifukwa choti Mulungu ndi wosunga lonjezo limene adachita ndi makolo anu Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
6
Mudziŵe tsono kuti Chauta sakukupatsani dziko labwinoli popeza kuti ndinu olungama ai. Inu ndinu anthu okanika.
7
Musaiŵale m'mene mudakwiyitsira Chauta, Mulungu wanu, m'chipululu muja. Kuyambira tsiku lija mudatuluka ku Ejipito kuja, mpaka tsiku limene mudafika kuno, mwakhala mukuukira Chauta, Mulungu wanu.
8
Ngakhale ku phiri la Horebu kuja, mudakwiyitsa Chauta, kukwiya kwake koti akadakuwonongani.
9
Ine ndidakwera phiri kukalandira miyala iŵiri imene padalembedwapo chipangano chimene Chauta adachita nanu. Ndidakhala kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, ndipo sindidadye kapena kumwa kanthu kalikonse.
10
Tsono Chauta adandipatsa miyala iŵiri ija imene Iye yemwe adaalembapo ndi dzanja lake zonse zimene adalankhula ndi inu ali m'moto, pa tsiku lija mudasonkhana kuphiri kuja.
11
Zedi, patapita masiku makumi anaiwo, usana ndi usiku, Chauta adandipatsa miyala iŵiri ija, imene adaalembapo chipangano.
12
Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Nyamuka tsika msanga, choka kuphiri kuno, chifukwa anthu ako aja udaŵatsogolera kuchokera ku Ejipitoŵa, adziipitsa kwambiri. Sadakhalire kupatuka pa zimene ndidaŵalamula kuti azichita, ndipo adzipangira fano losungunula.”
13
Chauta adandiwuzanso kuti, “Anthuŵa ndikuŵadziŵadi, ndi anthu okanika.
14
Usandiletse, ndikufuna kuŵaononga ndi kufafaniziratu dzina lao pansi pa thambo. Koma iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kupambana iwoŵa.”
15
Pomwepo ndidatsika phiri, nditanyamula m'manja mwanga miyala iŵiri ija ya chipangano. M'phirimo munkatuluka malaŵi a moto.
16
Nditayang'ana, ndidaona kuti inu mudachimwira Chauta, Mulungu wanu, pakudzipangira fano lachitsulo la mwanawang'ombe. Simudakhalire kuleka kusunga malamulo amene Chauta adakulamulani.
17
Pompo ine ndidaponya pansi miyalayo ndi kuiswa, inu mukuwona.
18
Tsono masiku enanso makumi anai, usana ndi usiku, ndidagwada pamaso pa Chauta ndipo ndidapemphera. Sindidadye kapena kumwa kanthu kalikonse, chifukwa inuyo mudaachimwira Chauta ndikumkwiyitsa.
19
Ine ndinkaopa mkwiyo wa Chauta woopsawo, chifukwa kukwiya kwake kunali koti akadakuwonongani. Koma nthaŵi imeneyo Chauta adamvanso pemphero langa.
20
Chauta adakwiyiranso Aroni, kotero kuti akadamupha ndithu, koma ndidampemphereranso nthaŵi yomweyo.
21
Chinthu chimene mudachipangacho, fano lachitsulo la mwanawang'ombelo, ndidaliponya pa moto. Tsono ndidaliphwanya pafupipafupi ndi kuliperapera, ndipo ndidataya phulusa lake ku mtsinje wotsika m'phiri uja.
22
Inu mudakwiyitsanso Chauta, Mulungu wanu, pamene munali ku Tabera, ku Masa ndi ku Kibroti-Hatava.
23
Ndipo Chauta atakutumani kuchokera ku Kadesi-Baranea kuti mupite kukalandira dziko limene adakupatsanilo, inu mudakana malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudamkhulupirire kapena kumumvera.
24
Mwakhala mukumuukira Chauta kuyambira pamene ine ndidakudziŵani.
25
Motero ndidagwada pamaso pa Chauta ndipo ndidapemphera masiku makumi anai, usana ndi usiku, chifukwa Chauta adaatsimikiza zokuwonongani.
26
Ndidapemphera motere, ndidati, “Inu Chauta, Ambuye athu, chonde musaŵaononge anthuŵa amene mudaŵasankha kuti akhale anuanu. Anthu ameneŵa mudaŵapulumutsa ndi ukulu wanu ndipo mudaŵatulutsa ku Ejipito ndi mphamvu zanu zazikulu.
27
Kumbukirani atumiki anu aja, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, ndipo musasamale kukanika kwa anthu anuŵa, kuipa kwao ndi kuchimwa kwao,
28
kuti Aejipito aja angamadzanene kuti Inu simudathe konse kuŵaloŵetsa anthu anu m'dziko limene mudaŵalonjeza. Azidzanenanso kuti: Adaŵatulutsa anthuwo kuti akaŵaphe ku chipululu poti adadana nawo.
29
Chonsecho anthu ameneŵa mudaŵasankha kuti akhale anuanu, ndipo mudaŵatulutsa ku Ejipito ndi mphamvu zanu zazikulu ndi mkono wanu wotambalitsa.”
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34