bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 26
Deuteronomy 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 27 →
1
Mukadzaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo,
2
aliyense mwa inu pa zokolola zonse zoyamba zimene adazipeza m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, atengeko zina ndi kuziika m'dengu, ndipo apite nazo ku malo amene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azidzapembedzerako.
3
Apite kwa mkulu wa ansembe amene ali pa ntchito nthaŵi imeneyo, ndipo amuuze kuti, “Tsopano ndadziŵadi kuti Chauta, Mulungu wanga, wandiloŵetsa m'dziko limene adalonjeza makolo athu kuti adzatipatsa ife.”
4
Wansembeyo ndiye amene adzakulandireni dengulo ndi kuliika patsogolo pa guwa la Chauta, Mulungu wanu.
5
Tsono pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, muzidzanena kuti, “Kholo langa linali Lachiaramu, munthu wongoyendayenda, amene adapita ku Ejipito ndi banja lake nakakhala kumeneko. Popita kumeneko, anthuwo adaali ochepa, koma pambuyo pake adachuluka nasanduka mtundu waukulu ndi wamphamvu.
6
Aejipito adatichita zankhanza ndi kutizunza potigwiritsa ntchito mwaukapolo.
7
Pamenepo ife tidalirira Chauta, Mulungu wa makolo athu, kuti atithandize. Iyeyo adatimva, ndipo adaona kusauka kwathu, ntchito yolemetsa imene iwo aja ankatigwiritsa, ndiponso moyo wathu wopsinjidwawo.
8
Mwa mphamvu zake zazikulu ndiponso ndi dzanja lake lotambalitsa, Chauta adatitulutsa ku Ejipito. Padaoneka zozizwitsa ndi zizindikiro, ndipo padachitika zinthu zoopsa zambiri.
9
Potsiriza adatifikitsa kuno, natipatsa dziko lino, dziko lamwanaalirenji.
10
Motero tsopano, ndikubwera kwa Chauta ndi gawo la zokolola zoyamba za m'dziko limene wandipatsa.” Apo mutatula pansi dengulo pamaso pa Mulungu, mumpembedze pomwepo.
11
Kondwani popeza kuti Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani zabwino, inu ndi a m'banja mwanu. Mukondwe inu ndi Alevi, ndiponso alendo amene mumakhala nawo.
12
Chaka chachitatu chilichonse muzipereka chopereka chachikhumi cha zokolola zanu kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, kuti kumizinda kumene amakhala iwoŵa, adzakhale ndi chakudya chokwanira. Mutachita zimenezi,
13
munene kwa Chauta kuti, “Palibe nchimodzi chomwe chopereka chachikhumi chimene chatsalako m'nyumba mwanga. Zonse ndapereka kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, monga mudandilamulira. Sindidanyoze kapena kuiŵalapo malamulo anu ndi limodzi lomwe.
14
Pa za chachikhumi sindidadyepo nchimodzi chomwe pamene ndinkalira maliro. Pamene ndinali woipitsidwa pa zachipembedzo, sindidagwirepo nchimodzi chomwe. Ndipo sindidaperekepo nchimodzi chomwe kuperekera anthu akufa. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndakumverani. Zonse zimene mudalamula za chopereka chachikhumi ndachita.
15
Yang'anani pansi kuchokera kumwambako ku malo anu oyera, ndipo mudalitse anthu anu Aisraele. Mudalitsenso dziko ili lamwanaalirenji limene mwatipatsali, monga momwe mudalonjezera makolo athu.”
16
Chauta, Mulungu wanu, akukulamulani lero lino kuti mumvere malangizo ndi malamulo ake. Tsono muŵamveredi ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
17
Lero mwamdziŵa Chauta kuti ndi Mulungu wanu. Mwalonjeza kumvera Iyeyo, kusunga malangizo ndi malamulo ake, ndi kuchita zonse zimene akulamulani.
18
Lero Chauta wakulandirani ngati anthu ake, monga momwe adakulonjezerani, malinga nkusunga malamulo ake onse.
19
Motero pa matamando, pa mbiri ndi pa ulemerero adzakukwezani kupambana mitundu ina yonse ya anthu imene adailenga, ndipo mudzakhala anthu ake oyera mtima, monga momwe adalonjezera.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34